1 Yer. 25.11; 29.10 Chaka choyamba cha ulamuliro wa Kirusi, mfumu ya ku Persiya, Chauta adachitadi zimene adaanena kudzera mwa Yeremiya. Adaika maganizo mumtima mwa Kirusi, ndipo iye adalengeza m'dziko lake lonse ndi mau apakamwa, mpakanso ochita kulemba. Adati,
2 Yes. 44.28 “Kirusi, mfumu ya ku Persiya, akunena kuti, ‘Chauta, Mulungu Wakumwamba, wandipatsa ine maiko onse a pa dziko lonse lapansi, ndipo wandilamula kuti ndimmangire Nyumba ku Yerusalemu, ku dziko la Yuda.
3Tsono inu nonse amene muli akeake, Mulungu wanuyo akhale nanu. Aliyense mwa inu apite ku Yerusalemu, ku dziko la Yuda, kuti akamange Nyumba ya Chauta, Mulungu wa Israele. Iyeyo ndiye Mulungu amene amampembedza ku Yerusalemu.
4Motero kulikonse kumene anthu otsalawo amakhala, athandizidwe ndi eni dzikolo. Aŵapatse siliva ndi golide, katundu ndi ziŵeto, ndi zopereka zaufulu zoti akapereke ku Nyumba ya Mulungu, imene ili ku Yerusalemu.’ ”
5Choncho atsogoleri amabanja a fuko la Yuda ndi la Benjamini, ndiponso ansembe ndi Alevi, adayamba kukonzeka, aliyense amene mumtima mwake Mulungu adamupatsa maganizo oti apite kukamanganso Nyumba ya Chauta ku Yerusalemu.
6Onse oyandikana nawo adaŵathandiza poŵapatsa ziŵiya zasiliva, golide, katundu, ziŵeto ndiponso mphatso zamtengowapatali, kuphatikizapo zopereka zija zimene ankazipereka mwaufulu.
7Nayenso mfumu Kirusi adatulutsa ziŵiya za ku Nyumba ya Chauta zimene Nebukadinezara adaazitenga kuzichotsa ku Yerusalemu, kudzaziika m'nyumba ya milungu yake.
8Kirusi, mfumu ya ku Persiya, idazitulutsa zimenezi nkuzipereka kwa Metiredati, msungachuma wake, amene adaziŵerenga pamaso pa Sesibazara, nduna yaikulu ya ku dziko la Yuda.
9Chiŵerengero chake chinali chotere: Mabeseni agolide 30 a zopereka, mabeseni asiliva 1,000 a zopereka, zofukizira 29,
10timikhate tagolide 30, timikhate tasiliva 2,410, ndi ziŵiya zinanso 1,000.
11Ziŵiya zagolide ndi zasiliva zonse pamodzi zidakwanira 5,400. Zonsezi ndizo zimene Sesibazara adabwera nazo pamene akuukapolo aja ankabwerera ku Yerusalemu kuchokera ku Babiloni.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.