1Nthaŵi imeneyo Merodaki-Baladani, mwana wa Baladani, mfumu ya ku Babiloni, adatuma amithenga naŵapatsira makalata ndi mphatso kuti akapereke kwa Hezekiya, poti adaamva kuti ankadwala ndipo adachira.
2Hezekiya adaŵalandira anthuwo, naŵaonetsa nyumba yosungiramo zinthu zake, monga siliva, golide, zokometsera chakudya, mafuta onunkhira amtengowapatali, zida zonse zankhondo ndiponso zonse zimene ankazisunga m'nyumba zake zosungiramo chuma. Panalibe kanthu kalikonse m'nyumbamo ndi mu ufumu wake wonse kamene sadaŵaonetse.
3Tsono mneneri Yesaya adapita kwa mfumu Hezekiya namufunsa kuti, “Kodi anthu amene aja adakuuzani zotani, ndipo adaachokera kuti?” Hezekiya adayankha kuti, “Adaachokera ku dziko lakutali, ku Babiloni.”
4Yesaya adamufunsanso kuti, “Kodi m'nyumba mwanumo adaona chiyani?” Hezekiya adayankha kuti, “Adaona za m'nyumba mwanga. Palibe ndi chimodzi chomwe chimene sindidaŵaonetse m'nyumba zanga zosungiramo chuma.”
5Pamenepo Yesaya adauza Hezekiya kuti,
6“Chauta Mphambe akunena kuti nthaŵi idzafika pamene zonse za m'nyumba mwanu ndi zonse zimene makolo anu adazisonkhanitsa mpaka lero lino, adzakulandani kupita nazo ku Babiloni. Sipadzatsalapo ndi kanthu kamodzi komwe.
7Dan. 1.1-7; 2Maf. 24.10-16; 2Mbi. 36.10 Ena mwa ana anu, obereka inu nomwe, adzatengedwa, ndipo adzaŵasandutsa adindo ofulidwa kuti azikatumikira ku nyumba ya mfumu ku Babiloni.”
8Tsono mfumu Hezekiya adauza Yesaya kuti “mau amene Chauta walankhulaŵa ndi abwino.” Ponena zimenezo, ankaganiza kuti, “Palibe kanthu ai, malinga kuti padzakhale mtendere ndi bata masiku onse a moyo wanga.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.