Yob. 17 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Mtima wanga wasweka

ndipo masiku anga atha, manda andiyasamira kukamwa.

2Ndithudi, pali ondiseka ponseponse pondizungulira,

ndikupenya m'mene akundinyozera.

3“Inu nokha Mulungu,

mukhale ngati chigwiriro changa.

Kulibenso wina woti nkunditchinjiriza.

4Inu mwatseka mitima yao

kuti asamvetsetse bwino zanzeru,

choncho musalole kuti iwowo apambane.

5Paja akuti munthu akapereka abwenzi ake

chifukwa cha chuma, ana ake amazunzika.

6“Andisandutsa chisudzo chochiseka anthu,

akandiwona amangoti malovu nzee.

7M'maso mwanga mwada ndi chisoni,

ndaonda ndi mutu womwe.

8Anthu olungama akudabwa nazo kwambiri zimenezi.

Anthu osachimwa akupsera mtima anthu osamvera Mulungu.

9Komabe anthu olungama enieni amapitirira m'njira zao,

anthu osalakwa amalimbikira kukhalabe oyera.

10“Tsono nonsenu bwerani, mubwereze mau anu,

pakati panupa sindidzapezapo ndi mmodzi yemwe wanzeru.

11Masiku anga atha,

ndipo zimene ndidaakonza zalephereka.

Zimene ndinkayembekeza zapita padera.

12Koma abwenzi anga amanena kuti

usiku ndi usana womwe.

Amati, ‘kuŵala ndiye kuli pafupi,’

chonsecho mdima uli goo.

13Chimene ndikuyembekeza ndicho kukakhala ku manda,

ndikayaleko mphasa yanga mumdima.

14Ndidzauza dzenje la manda kuti,

‘Iwe ndiwe bambo wanga.’

Ndidzalankhulanso ndi mphutsi kuti,

‘Ndiwe mai wanga,’ kapena kuti, ‘Ndiwe mlongo wanga.’

15Tsono chiyembekezo changa chili kuti?

Ndani angaone populumukira panga?

16Ndithu, sindidzakhalanso ndi chiyembekezo chilichonse

poloŵa m'manda, pamene ndidzatsikira ku fumbi.”

Bilidadi

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help