Eks. 38 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Apanga guwa la nsembe zopsereza(Eks. 27.1-8)

1Pambuyo pake adapanga guwa la nsembe zopsereza la matabwa a mtengo wa kasiya. Linali lalibanda, muutali mwake munali masentimita 229, muufupi mwakenso ngati masentimita 229 mbali zonse zinali zofanana, msinkhu wake ngati masentimita 137.

2Pa ngodya zake zinai adapangapo nyanga zotuluka m'guwalo, mwakuti zidangolumikizika nkukhala chinthu chimodzi ndi guwalo. Ndipo guwa lonselo adalikuta ndi mkuŵa.

3Adapanganso zipangizo zonse za guwalo, mbale zolandirira phulusa, mafosholo, mabeseni, ngoŵe zokoŵera zinthu, ndiponso ziwaya zosonkhapo moto. Zonsezo zidapangidwa ndi mkuŵa.

4Tsono adapanga chitsulo cha sefa, cha guwa lansembelo, cholukidwa ndi mkuŵa wokhawokha, ndipo adachiika kunsi kwake kwa chibumi cha guwa, kuti chifike pakatimpakati pa guwalo.

5Adapanga mphete zinai ndipo adazilumikiza ku ngodya zinai za sefa ija, kuti apisemo mphiko zonyamulira.

6Adasema mphiko zonyamulira za mtengo wa kasiya, nazikuta ndi mkuŵa.

7Tsono guwalo pomalinyamula, mphikozo ankazilonga m'mphete zija, pa mbali zonse ziŵiri za guwa. Guwalo adalipanga ndi matabwa, ndipo adalijoba m'kati mwake.

8 Eks. 30.18 Ndipo adapanga beseni lamkuŵa losambira, pamodzi ndi phaka lake. Adapanga zimenezi ndi akalilole a akazi amene ankatumikira ku chipata choloŵera m'chihema chamsonkhano chija, kumene Chauta ankakumanako ndi anthu ake.

9Tsono adapanga bwalo. Nsalu zake zochingira bwalolo chakumwera kwake zinali za bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino, ndipo kutalika kwake kunali mamita 46.

10Nsanamira zake makumi aŵiri, pamodzi ndi masinde ake makumi aŵiri, zonsezo zinali zamkuŵa, koma ngoŵe za pa nsanamirazo, pamodzi ndi mitanda yake, zinali zasiliva.

11Ku mbali yakumpoto kunali nsalu zochingira, kutalika kwake mamita 46. Nsanamira zake makumi aŵiri ndi masinde makumi aŵiri zinali zamkuŵa. Koma ngoŵe za pa nsanamirazo, pamodzi ndi mitanda yake, zinali zasiliva.

12Pa mbali yakuzambwe panali nsalu zochingira, kutalika kwake mamita 23, ndi nsanamira zake khumi ndi masinde khumi. Ngoŵe zake ndiponso mitanda yake zinali zasiliva.

13Pa mbali inayo yakuvuma panalinso mamita 23.

14Panali nsalu zochinga pa mbali imodzi ya chipata, zotalika mamita asanu ndi aŵiri, zokhala ndi nsanamira zake zitatu ndi masinde atatu.

15Pa mbali inayo panali chimodzimodzi. Choncho pa mbali zonse ziŵirizo za chipata choloŵera ku bwalo chija, panali nsalu zochinga, zotalika mamita asanu ndi aŵiri, zokhala ndi nsanamira zitatu ndi masinde atatu.

16Nsalu zonse zochinga kuzungulira bwalolo zinali za bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino.

17Masinde a nsanamirazo anali opangidwa ndi mkuŵa. Ndipo ngoŵe za pa nsanamirazo, mitanda yake ndi zokutira nsonga za nsanamirazo, zonsezo zinali zasiliva. Nsanamira zonse za bwalolo zidalumikizidwa ndi mitanda yasiliva.

18Nsalu zochingira pa chipata cha ku bwalolo, zokongoletsedwa ndi zopetapeta, zinali zobiriŵira, zofiirira ndi zofiira, ndiponso za bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino. Kutalika kwake kunali mamita asanu ndi anai, msinkhu wake unali masentimita 229 monga zochingira zake za bwalolo.

19Nsaluzo adazikoloŵeka ku nsanamira zinai zokhala m'masinde anai amkuŵa. Ngoŵe za pa nsanamira, mitu yake ndi mitanda yake, zonsezo zinali zasiliva.

20Koma zikhomo zake za chihema cha Chauta, ndiponso zikhomo zake za bwalolo, zonsezo zinali zamkuŵa.

Zipangizo zachitsulo za malo opatulika

21Nachi chiŵerengero cha golide, siliva ndi mkuŵa zimene ankazigwiritsa ntchito m'chihema chaumboni cha Chauta, monga momwe Mose adalamulira. Alevi ndiwo anali ndi udindo wakuziŵerenga, ndipo amene ankaŵatsogolera ndi Itamara, mwana wa wansembe Aroni.

22Ndipo Bezalele, mwana wa Uri, mdzukulu wa Huri, wa fuko la Yuda, adapanga zonse zimene Chauta adalamula Mose kuti apange.

23Mthandizi wake Oholiyabu, mwana wa Ahisamaki, wa fuko la Dani, anali wodziŵa kuzokota miyala, kulemba mapulani, ndi kuwomba nsalu yopetedwa ndi thonje lobiriŵira, lofiirira ndi lofiira, ndiponso nsalu ya bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino.

24Golide yense amene ankagwiritsa ntchito popanga malo opatulika, anali golide amene anthu adaapereka kwa Chauta, ndipo ankalemera makilogaramu 1,000, potsata miyeso ya ku Nyumba ya Mulungu.

25Eks. 30.11-16Siliva wochokera kwa mpingo wonse wa anthu, anali wolemera makilogaramu 3,430, potsata miyeso ya ku Nyumba ya Mulungu.

26Mt. 17.24 Munthu aliyense ankapereka beka imodzi (ndiye kuti magaramu ngati 6, potsata muyeso wa ku Nyumba ya Mulungu.) Anthu onse olembedwa m'kaundula analipo 603,550 amuna okha, a zaka makumi aŵiri kapena kupitirira.

27Siliva wolemera makilogaramu 3,400 adamangira masinde 100 a malo opatulika ndi a nsalu zochingira. Tsinde lililonse linkalira siliva wolemera makilogaramu 34.

28Ndi makilogaramu otsalawo adapanga ngoŵe za pa nsanamirazo ndipo adakuta nsonga za nsanamira ndi kupanga mitanda yake.

29Mkuŵa umene adaapereka kwa Chauta udakwana makilogaramu 2,425 pamodzi.

30Tsono ndi mkuŵa umenewu adapanga masinde a pa chipata choloŵera ku chihema chamsonkhano. Adapanganso guwa la nsembe zopsereza, pamodzi ndi chitsulo cha sefa, zipangizo zonse za guwalo,

31masinde a bwalo lonse lozungulira, ndi zikhomo zonse za chihema cha Chauta ndi za bwalo lonse lozungulira.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help