1Uwu ndi Uthenga Wabwino wonena za Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu.
2Mal. 3.1 Udayamba monga mneneri Yesaya adalembera m'buku mwake kuti, “Mulungu akuti,
“Ndidzatuma wamthenga wanga m'tsogolo mwako
kuti akakonzeretu njira yoti iwe udzapitemo.
3 Yes. 40.3 Liwu la munthu wofuula m'chipululu:
akunena kuti,
‘Konzani mseu wodzadzeramo Ambuye,
ongolani njira zoti adzapitemo.’ ”
4Zimenezi zidachitikadi pamene Yohane Mbatizi adaafika ku chipululu, nayamba kulalika. Ankauza anthu kuti, “Tembenukani mtima, mubatizidwe, ndipo Mulungu adzakukhululukirani machimo anu.”
5Anthu ochokera ku dera lonse la Yudeya ndi a ku Yerusalemu ankadza kwa iye. Tsono ankati iwo akaulula machimo ao, iye nkumaŵabatiza mu Mtsinje wa Yordani.
6 2Maf. 1.8 Yohaneyo ankavala zovala za ubweya wa ngamira, ndipo ankamangira lamba wachikopa m'chiwuno. Chakudya chake chidaali dzombe ndi uchi wam'thengo.
7Kulalika kwake ankati, “Pambuyo panga pakubwera wina wamphamvu kuposa ine, mwakuti ineyo ndine wosayenera ngakhale kuŵerama nkumasula zingwe za nsapato zake.
8Ine ndakubatizani ndi madzi, koma Iyeyo adzakubatizani mwa Mzimu Woyera.”
Yesu abatizidwa nakayesedwa(Mt. 3.13—4.11; Lk. 3.21-22; 4.1-13)9Pa masiku amenewo Yesu adafika kuchokera ku Nazarete, mudzi wa ku Galileya, ndipo Yohane adambatiza mu mtsinje wa Yordani.
10Potuluka m'madzimo, adangoona kuthambo kukutsekuka, ndipo Mzimu Woyera akutsika pa Iye ngati nkhunda.
11Gen. 22.2; Mas. 2.7; Yes. 42.1; Mt. 3.17; 12.18; Mk. 9.7; Lk. 3.22Tsono kudamveka mau ochokera kumwamba akuti, “Iwe ndiwe Mwana wanga wapamtima. Ndimakondwera nawe kwambiri.”
12Nthaŵi yomweyo Mzimu Woyera adapititsa Yesu ku chipululu.
13Yesuyo adakhala kumeneko masiku makumi anai, Satana akumuyesa. Komweko kunalinso nyama zakuthengo, ndipo angelo ankamutumikira.
Yesu ayamba ntchito yake ku Galileya(Mt. 4.12-14; Lk. 4.14-15)14Yohane uja ataponyedwa m'ndende, Yesu adapita ku Galileya akulalika Uthenga Wabwino wonena za Mulungu.
15Mt. 3.2Ankati, “Nthaŵi yakwana, Ufumu wa Mulungu wayandikira. Tembenukani mtima ndi kukhulupirira Uthenga Wabwinowu.”
Yesu aitana asodzi anai(Mt. 4.18-22; Lk. 5.1-11)16Pamene Yesu ankayenda m'mbali mwa nyanja ya Galileya, adaona anthu aŵiri, Simoni ndi mbale wake Andrea, akuponya khoka m'nyanjamo, popeza kuti anali asodzi.
17Yesu adaŵauza kuti, “Inu, munditsate, ndikakusandutseni asodzi a anthu.”
18Pomwepo iwo adasiya makoka ao, namamtsatadi.
19Atapitirira pang'ono, Yesu adaona Yakobe ndi Yohane, ana a Zebedeo. Iwowo anali m'chombo, akukonza makoka ao,
20nthaŵi yomweyo Iye nkuŵaitana. Pamenepo iwowo adasiya bambo wao Zebedeo m'chombomo pamodzi ndi antchito ake, namatsata Yesu.
Yesu achiritsa munthu wogwidwa ndi mzimu woipa(Lk. 4.31-37)21Onsewo adapita ku Kapernao. Tsono litafika tsiku la Sabata, Yesu adaloŵa m'nyumba yamapemphero, nayamba kuphunzitsa.
22Mt. 7.28, 29Zophunzitsa zake anthu zidaaŵagwira mtima kwambiri, chifukwa ankaphunzitsa moonetsa ulamuliro, kusiyana ndi m'mene ankachitira aphunzitsi a Malamulo.
23M'nyumba yamapempheroyo mudaaloŵa munthu wogwidwa ndi mzimu womuipitsa. Adalankhula mokuŵa kuti,
24“Kodi takuputani chiyani, Inu Yesu wa ku Nazarete? Kodi mwadzatiwononga? Ndakudziŵani, ndinu Woyera uja wa Mulungu.”
25Koma Yesu adazazira mzimu woipawo, adati, “Khala chete, tuluka mwa munthuyu.”
26Apo mzimu womuipitsa uja udamugwedeza kwamphamvu munthuyo, ndipo udakuwa koopsa, nkutuluka.
27Anthu onse aja adazizwa kwambiri, mpaka kumafunsana kuti, “Kodi zimenezi nzotani? Zophunzitsa zamtundutu zimenezi! Ngakhale mizimu yoipitsa anthu yomwe akuilamula ndi mphamvu, ndipo ikumumveradi.”
28Mwamsanga mbiri yake idawanda ponseponse ku dera lonse la ku Galileya.
Yesu achiritsa anthu ambiri(Mt. 8.14-17; Lk. 4.38-41)29Pambuyo pake Yesu adachoka ku nyumba yamapemphero kuja, nakaloŵa pamodzi ndi Yakobe ndi Yohane m'nyumba ya Simoni ndi Andrea.
30Apongozi a Simoni anali gone, akudwala malungo, ndipo nthaŵi yomweyo anthu adamufotokozera za matendawo.
31Yesu adapita nakaŵagwira pa dzanja amaiwo nkuŵadzutsa, ndipo malungowo adatha. Pomwepo amai aja adayamba kukonzera anthu chakudya.
32Madzulo amenewo, dzuŵa litaloŵa, anthu adabwera kwa Yesu ndi anzao onse ovutika, ndi ogwidwa ndi mizimu yoipa.
33Anthu a m'mudzi monsemo adaasonkhana pakhomopo.
34Yesu adachiritsa ambiri amene ankavutika ndi matenda osiyanasiyana, ndipo adatulutsa mizimu yoipa yambiri. Koma mizimuyo ankailetsa kuti isalankhule, chifukwa idaamzindikira.
Yesu anka kukalalika ku Galileya(Lk. 4.42-44)35M'mamaŵa ndithu, kusanache, Yesu adadzuka napita kumalo kosapitapita anthu. Kumeneko adakapemphera.
36Simoni ndi anzake aja adamlondola komweko.
37Atampeza adamuuza kuti, “Anthu onse akukufunafunani.”
38Koma Iye adaŵauza kuti, “Tiyeni tinke ku midzi ina kufupi konkuno, ndikalalike mau kumenekonso, pakuti ndizo ndidadzera.”
39Mt. 4.23; 9.35Tsono adapita nalalika m'nyumba zamapemphero ku Galileya konseko, ndipo ankatulutsa mizimu yoipa.
Yesu achiritsa munthu wakhate(Mt. 8.1-4; Lk. 5.12-16)40Munthu wina wakhate adadza kwa Yesu. Adamugwadira nayamba kumdandaulira. Adati, “Mutafuna, mungathe kundichiritsa.”
41Yesu adamumvera chifundo. Adatambalitsa dzanja nkumukhudza nati, “Chabwino, ndikufuna, chira!”
42Pomwepo khate lake lija lidatha, ndipo adachiradi.
43Tsono Yesu adamlamula kuti apite, namuuza mau amphamvu.
44Lev. 14.1-32Adati, “Chenjera, usakambire wina aliyense zimenezi. Ingopita, ukadziwonetse kwa wansembe, ndipo ukapereke nsembe adalamula Mose ija. Imeneyo ikhale yotsimikizira anthu onse kuti wachiradi.”
45Koma munthuyo atachoka pamenepo, adayamba kumaulula zonse, ndi kufalitsa nkhani imeneyi, kotero kuti Yesu sadathenso kuwonekera poyera m'mudzi uliwonse. Nchifukwa chake ankakhala kwina, kumalo kosapitapita anthu, koma anthu ankabwerabe kwa Iye kuchokera uku ndi uku.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.