Ezek. 37 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Chigwa cha mafupa ouma

1Mphamvu ya Chauta idandigwira, Mzimu wa Chauta udandinyamula nkukandikhazika pakati pa chigwa. Chigwacho chinali chodzaza ndi mafupa.

2Chauta adandiyendetsa uku ndi uku pakati pa mafupawo. Mafupawo analitu ochuluka kwambiri m'chigwa chonsecho, ndipo anali ochita kuti gwaa kuuma kwake.

3Tsono adandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi mafupa ameneŵa angathe kukhalanso ndi moyo?” Ine ndidati, “Ambuye Chauta, ndi Inuyo amene mukudziŵa zimenezi.”

4Apo adandiwuza kuti, “Alalikire mafupa ameneŵa, uŵauze mafupa oumawo kuti amve mau a Ine Chauta.

5Unene kuti zimene Ine Ambuye Chauta ndikuŵauza mafupawo ndi izi: Ndidzauzira mpweya mwa inu, ndipo mudzakhalanso ndi moyo.

6Ndidzakupatsani mitsempha ndi mnofu, nkukukutani ndi khungu. Ndidzauzira mpweya mwa inu, ndipo mudzakhalanso ndi moyo. Tsono mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.”

7Pamenepo ndidayamba kulalika monga momwe adandilamulira. Ndikulalika choncho ndidangomva kuti gogobedegogobede! Mafupa aja kuyamba kulumikizana.

8Ine ndiyang'ane, ndidaona kuti pali mitsempha, kenaka mnofu ukuwonekanso, potsiriza nkubwera khungu pamwamba pake, koma munalibe mpweya mwa iwo.

9Tsono Chauta adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, ulalike ndi kuuza mpweya mau a Ine Ambuye Chauta, akuti, ‘Mpweya iwe, bwera kuno, bwera kuchokera ku mphepo zinai, dzaŵauzire anthu ophedwaŵa, kuti akhalenso ndi moyo.’ ”

10Chiv. 11.11Motero ndidayamba kulalika monga adandilamulira. Tsono mpweya udaloŵa mwa iwo, ndipo akufa aja adakhala ndi moyo, naimirira. Linali gulu lalikulu kwambiri la ankhondo.

11Kenaka Chauta adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, mafupa ameneŵa ndi Aisraele onse. Iwo amanena kuti, ‘Mafupa athu ndi ouma, chiyembekezo chathu chidataika, taonongekeratu.’

12Nchifukwa chake uŵalalikire ndi kuŵauza kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, Inu anthu anga, ndidzafukula manda anu, ndipo ndidzakutulutsanimo. Ndidzakubwezerani ku dziko la Israele.

13Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, ndikadzafukula manda anu ndi kukutulutsanimo, inu anthu anga.

14Tsono ndidzaika mzimu wanga mwa inu ndipo mudzakhalanso ndi moyo, pambuyo pake ndidzakukhazikani m'dziko lanu. Choncho mudzadziŵa kuti Ine Chauta ndalankhula zimenezi, ndipo ndidzazichitadi. Ndikutero Ine Chauta.”

Yuda ndi Israele akhala mu ufumu umodzi

15Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,

16“Iwe mwana wa munthu, tenga ndodo, ulembepo kuti, ‘Ya Ayuda ndi Aisraele ogwirizana nawo.’ Tsono utenge ndodo ina, ulembepo kuti, ‘Ya Aefuremu, ndiye kuti fuko la Yosefe, ndi Aisraele ogwirizana nawo.’

17Tsono utenge ndodo ziŵirizo ndi kuzilumikiza kuti zikhale ngati ndodo imodzi.

18Anthu akwanu akakufunsa tanthauzo lake la zimenezi,

19uŵauze kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, Ndili pafupi kutenga ndodo ya Yosefe, imene ili m'manja mwa Efuremu, pamodzi ndi Aisraele ogwirizana nawo, ndiilumikiza ndi ndodo ya Yuda kuti zikhale ndodo imodzi. Ndipo zidzakhaladi imodzi m'manja mwanga.

20Ndodo zimene ukulembapozo zikadzakhala m'manja mwako, pamaso pa anthu onse,

21pamenepo udzaŵauze kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, Ndidzaŵaitana Aisraele kuchokera ku malo ao aukapolo pakati pa anthu a mitundu ina. Ndidzaŵasonkhanitsa kuchokera ku mphepo zinai ndi kuŵabwezera ku dziko lao.

22Ndidzaŵasandutsa mtundu umodzi m'dzikomo, ku mapiri a Israele, ndipo adzakhala ndi mfumu imodzi yokha. Sadzakhalanso mitundu iŵiri ya anthu kapena kugaŵikana maufumu aŵiri.

23Sadzadziipitsanso ndi mafano ao ndi zinthu zina zonyansa, kapena ndi zochimwa zao zina zilizonse. Ndidzaŵapulumutsa ku machimo ao onse, ndipo ndidzaŵayeretsa. Motero iwowo adzakhala anthu anga, ndipo Ineyo ndidzakhala Mulungu wao.

24 Ezek. 34.24 “Mtumiki wanga Davide adzakhala mfumu yao, motero onsewo adzakhala ndi mbusa mmodzi. Adzatsata malamulo anga, adzamvera mosamala malangizo anga.

25Adzakhala m'dziko limene ndidapatsa mtumiki wanga Yakobe, kumene ankakhala makolo anu. Iwowo, pamodzi ndi ana ao ndi zidzukulu zao, adzakhala kumeneko mpaka muyaya. Ndipo mtumiki wanga Davide adzakhala mtsogoleri wao mpaka muyaya.

26Ndidzachita nawo chipangano chamtendere. Chipangano chimenechi chidzakhala chao mpaka muyaya. Ndidzaŵakhazikitsa ndi kuŵachulukitsa, ndipo ndidzaika Nyumba yanga pakati pao mpaka muyaya.

272Ako. 6.16; Chiv. 21.3 Nyumba yanga idzakhala pakati pao. Ineyo ndidzakhala Mulungu wao, ndipo iwowo adzakhala anthu anga.

28Apo anthu a mitundu ina adzadziŵa kuti Ine Chauta Aisraele ndimaŵasandutsa oyera, chifukwa chakuti Nyumba yanga ili pakati pao mpaka muyaya.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help