1Pambuyo pake Eliyasibu, mkulu wa ansembe, adayamba kugwira ntchito pamodzi ndi ansembe anzake, ndipo adamanga Chipata cha Nkhosa. Adachipatulira Mulungu naika zitseko zake. Khoma limene adapatulalo lidafika ku Nsanja ya Zana, mpakanso ku Nsanja ya Hananele.
2Anthu a ku Yeriko adamanga chigawo china pambalipa, ndipo Zakuri, mwana wa Imuri, adamanga chigawo chinanso kuyandikana ndi chimenechi.
3A fuko la Hasena adamanga Chipata cha Nsomba. Iwowo adayala mitanda yake naikira zitseko zake, zotsekera zake, ndi mipiringidzo yake.
4Pambali pa iwowo Meremoti, mwana wa Uriya, mwana wa Hakozi, adakonza chigawo china. Pambali pa iwowo Mesulamu, mwana wa Berekiya, mwana wa Mesezabele, adakonza chigawo china. Pambali pa iwowo Zadoki, mwana wa Baana, adakonza chigawo china.
5Pambali pa iwowo Atekowa adakonza chigawo china, koma atsogoleri ao adakana kugwira ntchito imene akuluakulu ao adaŵapatsa.
6Yoyada, mwana wa Paseya, ndi Mesulamu mwana wa Besodeiya, adakonza Chipata Chakale. Adayala mitanda yake naikira zitseko zake, zotsekera zake ndi mipiringidzo yake.
7Pambali pa iwowo, Melatiya Mgibiyoni ndi Yadoni Mmeronoti, ndiponso anthu a ku Gibiyoni ndi a ku Mizipa, adakonza chigawo chao mpaka ku nyumba ya bwanamkubwa wa chigawo cha Patsidya pa Yufurate.
8Pambali pa iwowo Uziyele, mwana wa Haraiya, wa m'gulu la amisiri osula golide, adakonza chigawo china. Pambali pa iyeyo Hananiya, mmodzi mwa anthu oyenga mafuta onunkhira, adakonza chigawo china. Onsewo adakonza Yerusalemu mpaka ku Khoma Lotambasuka.
9Pambali pa iwowo Refaya, mwana wa Huri, wolamulira theka la dera la mzinda wa Yerusalemu, adakonza chigawo china.
10Pambali pa iwowo Yedaya, mwana wa Harumafa, adakonza chigawo choyang'anana ndi nyumba yake. Pambali pa iyeyo Hatusi, mwana wa Hasabuneiya, adakonza chigawo china.
11Malikiya, mwana wa Harimu, ndiponso Hasubu mwana wa Pahatimowabu, adakonza chigawo china pamodzi ndi Nsanja ya Ng'anjo.
12Pambali pa iyeyo Salumu, mwana wa Halohesi, wolamulira theka lina la dera la mzinda wa Yerusalemu, adakonza chigawo china, iyeyo pamodzi ndi ana ake aakazi.
13Hanuni pamodzi ndi nzika za ku Zanowa adakonza Chipata cha ku Chigwa. Adachimanganso naikira zitseko zake, zotsekera zake ndi mipiringidzo yake. Adakonzanso khoma mamita 400 mpaka kukafika ku Chipata cha Zinyalala.
14Malakiya, mwana wa Rekabu, wolamulira dera la Betehakeremu, adakonza Chipata cha Zinyalala. Adachimanganso, naikira zitseko zake, zotsekera zake ndi mipiringidzo yake.
15Salumu mwana wa Kolihoze wolamulira dera la Mizipa, adakonza Chipata cha Kasupe. Adachimanganso, naikira denga lake, zitseko, zotsekera ndi mipiringidzo yake. Adamanganso khoma la Dziŵe la Sela pafupi ndi munda wa mfumu, mpaka ku makwerero otsikira potuluka mu mzinda wa Davide.
16Pambali pa iyeyo Nehemiya, mwana wa Azibuki, wolamulira theka la dera la Betezuri, adakonza chigawo china mpaka ku malo oyang'anana ndi manda a Davide, ndi kukafika ku dziŵe lokumba ndiponso ku nyumba ya ankhondo.
Alevi amene ankagwira ntchito pa khoma17Pambali pa Nehemiyayo Alevi adakonza chigawo china. Mtsogoleri wao anali Rehumu mwana wa Bani. Pambali pa iyeyo Basabiya, wolamulira theka la dera la Keila, adakonza chigawo chake.
18Pambali pa iyeyo abale ao adapitiriza kukonza. Mtsogoleri wao anali Bavai mwana wa Henadadi, wolamulira theka la dera lina la Keila.
19Pambali pa iyeyo Ezere mwana wa Yesuwa wolamulira Mizipa, adakonza chigawo china choyang'anana ndi chikweza chofikira ku malo osungira zida zankhondo pa Ndonyo.
20Pambali pa iyeyo Baruki mwana wa Zabai adakonza chigawo kuyambira pa Ndonyo mpaka ku chitseko cha nyumba ya Eliyasibu, mkulu wa ansembe.
21Pambali pa iyeyo Meremoti mwana wa Uriya, mwana wa Hakozi, adakonza chigawo china kuyambira ku chitseko cha nyumba ya Eliyasibu mpaka ku mathero a nyumbayo.
Ansembe ogwira ntchito pa khoma22Pambali pa Meremoti, ansembe okhala ku chidikha adakonza chigawo china.
23Pambali pa iwowo Benjamini ndi Hasubu adakonza chigawo china choyang'anana ndi nyumba zao. Pambali pa iwowo Azariya, mwana wa Maaseiya, mwana wa Ananiya, adakonza chigawo china pafupi ndi nyumba yake.
24Pambali pa iyeyo Binuyi, mwana wa Henadadi, adakonza chigawo china, kuyambira ku nyumba ya Azariya mpaka kukafika ku Ndonyo,
25ndiponso mpaka ku ngodya. Palala, mwana wa Uzai, adakonza chigawo china choyang'anana ndi Ndonyo ndiponso ndi nsanja yotuluka pa nyumba yapamwamba ya mfumu ku bwalo la alonda. Pambali pa iyeyo Pedaya, mwana wa Parosi,
26ndi atumiki a ku Nyumba ya Mulungu, amene ankakhala pa khoma la Ofele, adakonza chigawo china mpaka ku malo oyang'anana ndi Chipata cha Madzi kuvuma, ndiponso nsanja yaitali ija.
Anthu ena ogwira ntchito pa khoma27Pambali pa Pedaya ndi anzake, Atekowa adakonza chigawo china choyang'anana ndi nsanja ija yaikulu ndi yaitali mpaka kukafika ku khoma la Ofele.
28Kuyambira ku Chipata cha Akavalo, ansembe ena ankakonza khoma, aliyense moyang'anana ndi nyumba yake.
29Pambali pa iwowo Zadoki, mwana wa Imeri, adakonza chigawo china choyang'anananso ndi nyumba yake. Pambali pa iyeyo Semaya, mwana wa Sekaniya, amene ankasunga Chipata chakuvuma, adakonza chigawo china.
30Pambali pa iyeyo Hananiya, mwana wa Selemiya, ndiponso Hanuni, mwana wachisanu ndi chimodzi wa Zalafi, adakonza chigawo china. Pambali pa iwowo Mesulamu, mwana wa Berekiya, adakonza chigawo choyang'anana ndi chipinda chake.
31Pambali pa iyeyo Malikiya, mmodzi mwa amisiri a golide, adakonza chigawo china mpaka kukafika ku nyumba ya atumiki a ku Nyumba ya Mulungu, ndiponso ku nyumba ya anthu amalonda. Chigawo chimenechi chidaayang'anana ndi Chipata cha Mifikada, kufikira ku chipinda chapamwamba chapangodya.
32Ndipo pakati pa chipinda chapamwamba chapangodya ndi Chipata cha Nkhosa, amisiri a golide ndi anthu amalonda adakonza chigawo chao.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.