1 Ako. 6 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za milandu pakati pa akhristu

1Ngati wina ali ndi mlandu ndi mkhristu mnzake, angathe bwanji kukauzengetsa kwa oweruza amene ali akunja, osati kwa akhristu anzake?

2Kodi simukudziŵa kuti akhristu ndiwo adzaweruza anthu onse? Tsono ngati inu mudzaweruza anthu onse, kodi simungathe kuweruza ngakhale ndi timilandu tating'ono tomwe?

3Kodi simukudziŵa kuti tidzaweruza angelo? Nanji zinthu za moyo wapansipano?

4Tsono ngati muli ndi milandu pa zinthu zotere, bwanji mumaika anthu amene mpingo suŵayesa kanthu kuti aiweruze?

5Ndikunena zimenezi kuti ndikuchititseni manyazi. Kodi mwa inu palibe ndi mmodzi yemwe wanzeru, amene angathe kuweruza mlandu pakati pa akhristu anzake?

6Bwanji mkhristu akuimba mlandu mkhristu mnzake, mlanduwo nkuupereka kwa anthu akunja kuti auzenge?

7Chokha chakuti mumaimbana milandu inu nokhanokha, chatsimikiza kale kuti mwalephereratu. Bwanji osangopirira pamene ena akulakwirani? Bwanji osangolola kuti inuyo akubereni?

8Koma inuyo ndi amene mukulakwira ena, ndipo mukuŵabera, ngakhale iwowo ndi akhristu anzanu!

9Kani simudziŵa kuti anthu osalungama sadzaulaŵa Ufumu wa Mulungu? Musadzinyenge: anthu adama, opembedza mafano, achigololo, ochimwa ndi amuna anzao,

10mbala, aumbombo, zidakwa, augogodi, kapena achifwamba, ameneŵa sadzaulaŵa Ufumu wa Mulungu.

11Enanu munali otere kale, koma mudayeretsedwa, mudasanduka anthu a Mulungu, ndipo mudapezeka olungama pamaso pake. Zimenezi zidachitika m'dzina la Ambuye Yesu Khristu, ndiponso mwa Mzimu wa Mulungu wathu.

Thupi la mkhristu ndi nyumba yopatulika ya Mzimu Woyera

12 1Ako. 10.23 Zinthu zonse nzololedwa kwa ine, koma si zonse zili ndi phindu. Zonse nzololedwadi kwa ine, koma sindingalole kuti chilichonse chindigonjetse.

13Chakudya, kwake nkuloŵa m'mimba, ndipo mimba, kwake nkulandira chakudya. Koma Mulungu adzaononga ziŵiri zonsezo. Thupi la munthu si lochitira dama, koma ndi la Ambuye, ndipo Ambuye ndiwo mwiniwake thupilo.

14Mulungu adaukitsa Ambuye kwa akufa, ndipo mwa mphamvu yake adzatiwukitsa ifenso.

15Kodi inu simudziŵa kuti matupi anu ndi ziwalo za Khristu? Monga tsono ine nkutenga ziwalo za Khristu nkuzisandutsa ziwalo za mkazi wadama? Chosatheka!

16Gen. 2.24 Kaya simudziŵa kuti munthu amene amadzipereka kwa mkazi wadama, iyeyo ndi mkaziyo amasanduka thupi limodzi? Paja Malembo akuti, “Aŵiriwo adzasanduka thupi limodzi.”

17Koma amene amadzipereka kwa Ambuye, iyeyo ndi Ambuye amakhala mzimu umodzi.

18Thaŵani dama. Tchimo lina lililonse limene munthu amachita, siliipitsa thupi lake, koma munthu wadama amachimwira thupi lake lomwe.

191Ako. 3.16; 2Ako. 6.16Kodi simudziŵa kuti thupi lanu ndi nyumba ya Mzimu Woyera? Mulungu adakupatsani Mzimuyo kuti akhale mwa inu. Nchifukwa chake moyo umene muli nawo si wanunso.

20Mulungu adakugulani ndi mtengo wapatali, tsono muzimlemekeza ndi matupi anu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help