Yon. 3 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Anthu a ku Ninive alapa, Mulungu nkuŵakhululukira

1Chauta adalankhula ndi Yona kachiŵiri, namuuza kuti,

2“Nyamuka, pita ku Ninive, mzinda waukulu uja, ukaulalikire uthenga umene ndikukuuza.”

3Yona adanyamuka, napita ku Niniveko, potsata mau a Chauta. Mzindawo unali waukulu kwambiri, wofunika masiku atatu kuudutsa.

4Mt. 12.41; Lk. 11.32 Yona adaloŵa mumzindamo, nayenda ulendo wa tsiku limodzi. Adayamba kulalika kuti, “Pakapita masiku makumi anai, Ninive aonongeka!”

5Anthu a ku Ninive adakhulupirira Mulungu. Adalengeza kuti aliyense, wamkulu ndi wamng'ono yemwe, asale zakudya, ndipo avale chiguduli.

6Mfumu ya ku Ninive itamva zimenezo, idatsika pa mpando wake waufumu, nivula mkanjo wake. Idavala chiguduli, nikakhala nao pa dzala.

7Tsono mfumuyo idalengeza ku Ninive, kuti, “Nali lamulo lochokera kwa mfumu ndi akalonga ake: ‘Munthu aliyense asadye kanthu, ndiponso ziŵeto zonse zikuluzikulu ndi zing'onozing'ono zomwe zisadye kanthu. Zisadyetu kanthu, nkumwa madzi komwe zisamwe.

8Anthu avale ziguduli, nyamanso aziveke ziguduli. Anthuwo azifuula kwa Mulungu ndi mphamvu zao zonse. Ndithu aliyense asiye makhalidwe ake oipa ndi ntchito zake zankhanza.

9Nkudziŵanji, mwina Mulungu nkutikhululukira, naleka kutikwiyira, ifeyo osaonongeka.’ ”

10Mulungu adaona zimene anthuwo adachita, ndi m'mene adasiyira makhalidwe ao oipa. Choncho adakhululuka, osaŵapatsa chilango chimene adaati adzaŵapatsa.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help