1Tsono Abimeleki, mwana wa Yerubaala, adapita ku Sekemu kwa achibale a mai wake, nakaŵauza iwowo ndi fuko la banja la mai wake kuti,
2“Funsani nzika zonse za ku Sekemu kuno kuti, ‘Chabwino koposa nchiti kwa inu, kuti ana onse 70 a Yerubaala azikulamulirani, kapena kuti mmodzi yekha azikulamulirani? Muzikumbukiratu kuti paja ine ndine mbale wanu weniweni.’ ”
3Achibale a mai wakewo adamlankhulirako kwa anthu onse a ku Sekemu ndipo mitima yao ya anthuwo inali pa Abimeleki pakuti ankati, “Ameneyu ndi mbale wathu.”
4Adampatsa ndalama zasiliva 70 za m'nyumba yachipembedzo ya Baala wa Chipangano. Ndalama zimenezo Abimeleki uja adaalembera anthu aganyu achabechabe ndi osasamala ntchito kuti azimtsata.
5Adapita ku nyumba ya bambo wake ku Ufura, nakaŵaphera pa mwala umodzi abale ake 70, ana a Yerubaala. Koma Yotamu, mzime wa Yerubaala, sadaphedwe nao chifukwa adaabisala.
6Tsono nzika zonse za ku Sekemu zidasonkhana ndi anthu a ku nyumba ya Betemilo, nkupita ku mtengo wa thundu pafupi ndi chipilala chachipembedzo cha ku Sekemu, kukalonga Abimeleki ufumu.
Fanizo la Yotamu.7Yotamu atamva zimenezi, adapita kukaima pamwamba pa phiri la Gerizimu, ndipo adafuula kwambiri kuti, “Tamverani inu anthu a ku Sekemu, kuti nanunso Mulungu akumvereni.
8Padangotere: mitengo idapita kukalonga mfumu yoti iziilamulira. Ndiye mitengoyo idauza mtengo wa olivi kuti, ‘Iwe ukhale mfumu yathu.’
9Koma mtengo wa oliviwo udalandula, udati, ‘Ine sindingasiye mafuta angaŵa amene amalemekezera milungu ndi anthu omwe, kuti ndizikalamulira mitengo.’
10Apo mitengoyo idauza mkuyu kuti, ‘Bwera ndiwe, ukhale mfumu yathu.’
11Koma mkuyuwo udalandula, udati, ‘Ine sindingasiye zipatso zanga zokomazi nkuzuna kwakeku, kuti ndizikalamulira mitengo.’
12Tsono mitengo ija idauza mtengo wamphesa kuti, ‘Bwera ndiwe, ukhale mfumu yathu.’
13Koma mtengo wamphesawo udalandula, udati, ‘Ine sindingasiye kupereka vinyo amene amasangalatsa milungu ndi anthu omwe, kuti ndizikalamulira mitengo.’
14Apo mitengo yonse ija idauza mkandankhuku kuti, ‘Bwera ndiwe ukhale mfumu yathu.’
15Mkandankhukuwo udayankha kuti, ‘Ngati mukundidzoza ndi mtima wonse kuti ndikhale mfumu yanu, bwerani mudzabisale mumthunzi mwangamu. Mukapanda kutero, moto utuluke mwa ine ndi kupsereza mikungudza ya ku Lebanoni.’ ”
16Yotamu popitiriza adati, “Kodi tsono mudachita ndi mtima wonse ndiponso mokhulupirika pakumdzoza Abimeleki kuti akhale mfumu? Kodi mwamchitira ulemu Yerubaala ndi banja lake, poyang'anira ntchito zimene adachita?
17Suja bambo wanga adakumenyerani nkhondo naika moyo wake m'zoopsa, kuti akupulumutseni kwa Amidiyani?
18Koma lero inu mwaukira banja la bambo wanga. Mwapha ana ake 70 pa mwala umodzi, ndipo mwalonga ufumu Abimeleki, mwana wa mzikazi wake, kuti azilamulira nzika za ku Sekemu, chifukwa chakuti ngwapachibale wanu.
19Tsono ngati zimene lero mwachitira Yerubaala ndi banja lake mwazichita ndi mtima wonse ndiponso mokhulupirika, mukondwere naye Abimelekiyo ndipo nayenso akondwere nanu.
20Koma ngati sizili choncho, moto utuluke mwa Abimeleki, upsereze nzika za ku Sekemu pamodzi ndi anthu a ku nyumba ya Betemilo. Ndipo moto utuluke mwa nzika za ku Sekemu ndiponso mwa anthu a ku nyumba ya Betemilo ndi kupsereza Abimeleki.”
21Tsono Yotamu adathaŵa napita ku Beere ndipo adakakhala komweko, kuwopa Abimeleki mbale wake.
22Abimeleki adalamulira Aisraele zaka zitatu.
23Mulungu adaika chidani pakati pa Abimeleki ndi anthu a ku Sekemu, ndipo anthu a ku Sekemuwo adamuukira Abimeleki.
24Izi zidachitika kuti zoipa zimene iye adaŵachita ana 70 a Yerubaala aja zimubwerere, ndipo kuti magazi ao akhale pa Abimeleki mbale wao amene adaŵaphayo, ndiponso pa anthu a ku Sekemu amene adamulimbitsa mtima kuti aphe abale ake.
25Motero anthu a ku Sekemu adaika anthu pamwamba pa mapiri kuti abisalire Abimeleki, ndipo ankaŵalanda zinthu zao anthu onse odzera njira imeneyo. Abimeleki zimenezi adazimva.
26Tsiku lina Gaala, mwana wa Ebedi, adasamukira ku Sekemu pamodzi ndi achibale ake. Ndipo anthu a ku Sekemu adamkhulupirira iyeyo.
27Anthuwo adapita ku munda kukathyola mphesa, nafinya mphesazo. Kenaka adachita chikondwerero nakaloŵa m'nyumba ya milungu yao. M'menemo adadya ndi kumwa ndipo adayamba kutukwana Abimeleki.
28Pambuyo pake Gaala, mwana wa Ebedi, adati, “Kodi ife ndife anthu otani m'Sekemu muno? Chifukwa chiyani tikutumikira Abimeleki? Ndipo kodi ndaninso amene uja? Ha, si mwana wa Gideoni! Zebuli amalamulidwa ndi iye uja, koma nanga ife kuti tizimtumikira nchifukwa chiyani? Tiyeni tikhale pambuyo pa kholo lathu Hamori, tate wa fuko lathu.
29Anthu amumzindamu akadakhala pansi pa ulamuliro wanga, bwenzi nditamchotsa Abimelekiyo, ndipo ndikadamuuza kuti, ‘Onjezera ankhondo ako ndipo bwera, timenyane nkhondo.’ ”
30Pamene Zebuli, munthu wolamulira mzindawo, adamva mau a Gaala mwana wa Ebedi, adapsa mtima.
31Adatuma amithenga kwa Abimeleki ku Aruma kukanena kuti, “Gaala, mwana wa Ebedi, pamodzi ndi achibale ake, abwera ku Sekemu, akuutsa mitima ya anthu mu mzinda kuti akuukireni.
32Nchifukwa chake, mupite usiku inuyo ndi anthu amene muli nawo, kukabisala m'minda.
33Tsono m'maŵa dzuŵa likamatuluka, mudzuke msanga, mukauthire nkhondo mzindawo. Pamene Gaalayo ndi anthu ake azibwera kudzalimbana nanu, muŵakanthe monga m'mene mungathere.”
34Choncho Abimeleki ndi anthu onse amene anali naye adadzuka usiku nakabisalira mzinda wa Sekemu m'magulu anai.
35Gaala mwana wa Ebedi adatuluka nakaima pa khomo la chipata cha mzinda. Ndipo Abimeleki ndi anthu ake adavumbuluka kumene adabisala kuja.
36Gaala ataŵaona anthuwo, adauza Zebuli kuti, “Ona, anthu akutsika kuchokera pamwamba pa mapiri.” Zebuli adayankha kuti, “Si anthu amenewo, ndi zithunzithunzi chabe zapamapiri zonga anthu.”
37Gaala adalankhulanso nati, “Ona, anthu akutsika kuchokera pakati penipeni pa phiri, ndipo gulu limodzi likuchokera mbali ya ku mtengo wa thundu wa amaula.”
38Tsono Zebuli adamufunsa kuti, “Pakamwa pako paja pali kuti tsopano, iweyo amene unkati, ‘Abimeleki ndaninso kuti ife tizimtumikira?’ Kodi si ameneŵa anthu aja unkaŵanyozaŵa? Tulukatu tsopano ukamenyane nawo nkhondo.”
39Gaala adatuluka akutsogolera anthu a ku Sekemu nakamenyana naye nkhondo Abimeleki.
40Koma Abimelekiyo adampirikitsa ndipo Gaalayo adathaŵa. Anthu ake ambiri adavulala njira yonse mpaka ku khomo la chipata.
41Abimeleki adakhazikika ku Aruma, ndipo Zebuli adapirikitsa Gaala pamodzi ndi achibale ake, kotero kuti sadathenso kukhala ku Sekemu.
42M'maŵa mwake anthu a ku Sekemu adapangana kuti apite ku minda, ndipo Abimeleki adazimva zimenezi.
43Iye adatenga anthu ake, adaŵagaŵa m'magulu atatu, nakabisala m'minda. Ataona anthu akutuluka mu mzinda, pompo adapita kukalimbana nawo, naŵapha onsewo.
44Abimeleki pamodzi ndi gulu lake adathamangira kutsogolo, nakakhalira pa khomo la chipata cha mzinda, ndipo nthaŵi yomweyo magulu aŵiri ena aja adaŵathamangira anthu onse amene anali m'minda aja, naŵapha.
45Nkhondo idakhala tsiku lathunthu. Abimeleki adalanda mzindawo, naŵapha anthu amene anali m'menemo. Adauwonongeratu mzinda wonsewo, nauwaza mchere.
46Anthu onse a ku nsanja ya Sekemu atamva zimenezo, adakaloŵa m'linga la nyumba yachipembedzo ya Baala wa Chipangano.
47Abimeleki adazimva zakuti anthuwo asonkhana kumeneko.
48Tsono adapita ku phiri la Zalimuna ndi anthu ake onse. Kumeneko adatenga nkhwangwa m'manja mwake nadula nthambi za mtengo, ndipo adazinyamula nazisenza pa phewa. Tsono adauza anthu akewo kuti, “Zimene mwaona ndikuchitazi, fulumirani inunso muchite chimodzimodzi, monga momwe ndachitira inemu.”
49Choncho aliyense adadula mtolo wake natsatira Abimeleki, nakayedzeka mtolo wakewo pa linga lija ndipo adaliyatsa moto, kotero kuti anthu onse a ku nsanja ya Sekemu adafa. Analipo anthu ngati chikwi chimodzi, amuna ndi akazi.
50Pambuyo pake, Abimeleki adapita ku Tebezi. Adauzinga mzindawo naulanda.
51Mumzindawo munali nsanja yolimba, ndipo anthu onse amumzindamo, amuna onse ndi akazi omwe, adathaŵira m'nsanjamo, nadzitsekera m'kati. Ndipo adakwera ku tsindwi la nsanjayo.
52Abimeleki adabwera ku nsanja ija, naithira nkhondo, ndipo adakafika pafupi ndi chitseko cha nsanjayo kuti achitenthe.
532Sam. 11.21 Koma mkazi wina wake adaponya mwala wa mphero pa mutu wa Abimeleki, nautswanya.
54Apo Abimeleki uja adaitana msangamsanga mnyamata wake womunyamulira zida zake zankhondo namuuza kuti, “Solola lupanga lako, unditsirize, sindifuna kuti anthu azikati, ‘Mkazi ndiye amene adamupha.’ ” Apo mnyamata wakeyo adambayadi ndi lupanga, mpaka kutulukira kunja lupangalo, naafa.
55Aisraele ataona kuti Abimeleki wafa, onse adapita kwao.
56Umu ndimo m'mene Mulungu adalipsirira tchimo la Abimeleki limene adachitira bambo wake, pakupha abale ake 70 aja.
57Mulungu adaŵalanganso anthu a ku Sekemu chifukwa cha kuipa kwao, ndipo matemberero aja a Yotamu, mwana wa Yerubaala, adaŵagweradi.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.