Deut. 18 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Gawo la ansembe

1Ansembe Achilevi, ndiye kuti fuko lonse la Alevi, asalandireko gawo m'dziko la Israele ngati choloŵa chao. Iwoŵa azidya zoperekedwa nsembe kwa Chauta ndi zina zoyenera Iyeyo.

2Num. 18.20 Asakhale ndi choloŵa ngati mafuko ena. Choloŵa chao ndi Chauta amene, potsata malonjezo a Mulungu yemweyo.

3Mwa zopereka za anthu, zoyenera kuzilandira ansembeŵa, ndi izi: ng'ombe kapena nkhosa zodzaperekera nsembe, mwendo wamwamba, nyama yam'chibwano ndi chifu.

4Ansembe azilandiranso gawo lanu loyambayamba la tirigu, la vinyo, la mafuta aolivi ndiponso la ubweya.

5Pa mafuko anu onseŵa Chauta adasankhulapo anthu a fuko la Levi ndi ana ao, kuti azigwira ntchito zaunsembe nthaŵi zonse.

6Mlevi aliyense atafuna, angathe kubwera ku malo osankhidwa ndi Chauta kuchokera m'mudzi wina uliwonse ku Israele kumene akukhala.

7Ndipo kumeneko atumikire Chauta, Mulungu wake, pa unsembe, monga momwe achitira Alevi ena onse amene akutumikira kumeneko.

8Ayenera kulandira chakudya molingana ndi ansembe ena, ngakhale ali ndi ndalama chifukwa chogulitsa za m'banja mwake.

Chenjezo pa zochitachita zachikunja

9Mukadzaloŵa m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsanilo, musakatsate machitidwe onyansa a mitundu ya anthu akumeneko.

10Lev. 19.26; Eks. 22.18 Pakati panu pasadzapezeke wopereka mwana wake wamwamuna kapena wamkazi pa moto ngati nsembe. Pasaoneke munthu woombeza kapena woyeseza kulosa zam'tsogolo, kapena wogwiritsa ntchito nyanga kapena zithumwa.

11Lev. 19.31 Pasapezekenso munthu wopempha nzeru kwa mizimu ya anthu akufa.

12Chauta, Mulungu wanu, amadana nawo anthu ochita zoipa zimenezi. Chimene Mulungu akupirikitsira anthuŵa pamene inu mukufika ndi chifukwa chakuti anthuwo ankachita zoipa zoterezi.

13Mt. 5.48 Inu mukhale okhulupirika kwathunthu kwa Chauta, Mulungu wanu.

Mulungu alonjeza kuti adzatumiza mneneri

14Anthu amene mukukaŵalanda dziko limene mukakhalemolo, amatsata ndi kumvera amatsenga ndi oombeza. Koma inuyo Chauta, Mulungu wanu, sakulolani kuchita zimenezi.

15Ntc. 3.22; 7.37 Iye adzakutumizirani mneneri wonga ine wochokera mwa inu amene, ndipo mudzayenera kumumvera iyeyo.

16Pa tsiku lija mudaasonkhana pa phiri la Horebuli, mudaapempha kuti, “Tisamvenso Chauta, Mulungu wathu, akulankhula, ngakhale kuwonanso moto waukulu choterewu, kuti tingafe.”

17Apo Chauta adaandiwuza kuti, “Zonse zimene apemphazi anena mwanzeru.

18Ndidzaŵatumizira mneneri wonga iwe, wochokera mwa iwo amene. Ndidzamuuza zoti anene, ndipo iyeyo azidzauza anthu zonse zimene ndikumlamula.

19Ntc. 3.23 Mneneriyo akalankhula m'dzina langa, Ine ndidzalanga aliyense wosamvera mau angawo.

20Koma mneneri wina aliyense woyerekeza kulankhula m'dzina langa, Ine osamulamula kuti atero, aphedwe. Ndipo ayeneranso kuphedwa mneneri wina aliyense wolankhula m'dzina la milungu ina.”

21Mwina mwake munganene kuti, “Kodi munthu angadziŵe bwanji kuti mau a mneneri wakutiwakuti sakuchokera kwa Chauta?”

22Munthu akati akulankhula m'dzina la Chauta, ndipo ngati zolankhula zakezo sizichitika, pomwepo dziŵani kuti si mau a Chauta amenewo. Mneneri ameneyo wongolankhula zakezake modzikhulupirira, musamuwope ai.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help