Mphu. 43 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Dzuŵa

1Lisatero kukongola thambo lakumwamba!

Ngokongoladi kwambiri maonekedwe a mlengalenga!

2Dzuŵa likamatuluka limalalika kuti,

“Ntchito za Wopambanazonse nzododometsa kwambiri.”

3Masana limaumitsa dziko,

ndani angapirire kutentha kwake?

4Munthu ayenera kuvukuta, akafuna kuti ng'anjo itenthe.

Koma kutentha kwa dzuŵa pa mapiri, nkopambana

kutentha kwa ng'anjo katatu.

Limamwaza mpweya wotentha kwambiri ndipo

limathobwa m'maso ndi kuŵala kwake.

5Ambuye amene adalenga dzuŵalo ngaakulu,

mau ao amalifulumiza pa njira yake.

Mwezi

6Adalenganso mwezi umene sulephera kukhala,

umene uli chizindikiro choonetsa zigawo za

nthaŵi mpaka muyaya.

7Timalondola masiku achikondwerero potsata mwezi.

Mwezi umaŵala kwambiri kenaka nkuzimirira.

8Mwezi udapatsako dzina lake kwa miyezi,

ndipo umanka nukongolerakongolera pamene ukusinthika.

Uli ngati mbendera ya miyuni yamumlengalenga,

imene imaŵala ku thambo lakumwamba.

9Kunyezimira kwa nyenyezi kumakongoletsa

mlengalenga,

kuŵala kwake kumakometsa thambo la Ambuye.

10Akazilamulira Woyera uja,

zimaima kuti njo pamene adaziikapo,

iliyonse silephera pa ulonda wake.

Utawaleza

11Yang'ana utawaleza ndipo tamanda Mlengi wake.

Kuŵala kwake nkokongola kwabasi.

12Umakhala mu mlengalenga ngati uta wochezimira,

manja a Wopambanazonse ndiwo amaukoka.

Zodabwitsa za dziko lapansi

13Mulungu amalamula chisanu chambee kuti chigwe,

amachititsa mphezi kuti zitsimikize chiweruzo chake.

14Mosungira chuma chake mumatsekuka,

ndipo mitambo imauluka ngati mbalame.

15Amaunjika mitambo ndi mphamvu zake zazikulu,

kenaka nkuiphwanya naisandutsa matalala.

16Pakumva liwu la bingu lake, dziko limanjenjemera.

Ndipo Iye akaoneka, chivomezi chimagwedeza mapiri.

17Iye akalamula, mphepo yakumwera imaomba,

monganso mkuntho wakumpoto ndi kamvulumvulu.

Amagwetsa chisanu chambee ngati kutera kwa mbalame,

chimagwa pansi ngati thenje ya dzombe.

18Kuyera kwake maso amadodoma nako,

ndipo pamene chikugwa, mtima umachita chidwi.

19Ambuye amawaza pa dziko lapansi chisanu

chonga mchere,

chikalimba ndi mphepo yozizira, chimasanduka

ngati minga.

20Mphepo yozizira yakumpoto ikaomba,

pamwamba pa madzi pamalimba ndi chisanu.

Padziŵe paliponse madzi amalimba choncho,

naphimbapo ngati malaya ankhondo apachifuwa.

21Mwina Iye amapsereza mapiri ndi kutentha chipululu,

amafotetsa udzu ngati ndi moto.

22Koma nkhungu yam'mitambo imachiritsa zonse msanga,

ndipo zikafota ndi chitungu,

mame amazitsitsimutsanso.

23Ndi nzeru zake adagonjetsa nyanja

ndipo adaikamo zilumba.

24Amene amayenda pa nyanja amakamba za kuwopsa kwake,

ndipo nkhani zao zimatichititsa chidwi.

25M'nyanjamo muli zolengedwa zachilendo ndi zodabwitsa,

muli zamoyo zosiyanasiyana ndi zilombo zikuluzikulu,

26Ndi mphamvu za Mulungu, atumiki onsewo amafika

komwe alinga,

zonse zimayenda potsata malamulo ake.

27Tingasimbe zambirimbiri, komabe sitingazithe.

Mwachidule tingonena kuti, “Ambuye ndiwo Zonse.”

28Tingazipeze kuti mphamvu zoŵatamandira,

pakuti Iwowo ngaakulu kupambana ntchito zao zonse.

29Ambuye ngoopsa ndiponso ngaakulu,

mphamvu zao nzodabwitsa.

30Tamandani Ambuye monga mungathere,

chifukwa amapambana matamando onse.

Tamandani ukulu wa Ambuye ndi mphamvu zanu zonse,

musatopere, chifukwa simungafikepo.

31Kodi alipo amene adaona Ambuye

kuti angathe kufotokoza m'mene aliri?

Kodi ndani angaŵalemekeze

monga momwe kufunikira?

32Ntchito zao timangoziwona pang'ono chabe,

zikalipo zina zambiri zobisika zoposa izo.

33Ambuye adapanga zinthu zonse

ndipo amapereka nzeru kwa anthu

oŵapembedza.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help