1Inu Chauta, bwanji osang'amba mlengalenga
kuti mutsike pansi?
Bwanji osati mapiri agwedezeke poona Inu,
2monga momwe moto umatenthera tchire,
ndiponso monga momwe umagadutsira madzi,
kuti adani anu akudziŵeni,
ndipo kuti anthu a mitundu ina anjenjemere pamaso panu.
3Nthaŵi ina yake mudatsika pansi pano
kudzachita zinthu zoopsa zimene sitidaziyembekeze.
Mapiri atakuwonani, adanjenjemera ndi mantha.
4 1Ako. 2.9 Chikhalire palibe ndi mmodzi yemwe
amene adaona kapena kumva za Mulungu wina wonga Inu,
wochitira zotere anthu omkhulupirira.
5Inu mumaŵalandira onse amene
amakondwera pochita zolungama,
amene amayesetsa kuyenda monga Inu mufunira.
Inde mudatikwiyira,
komabe ife tidapitiriza kuchimwa.
Takhala ochimwadi nthaŵi yaitali,
kodi tidzapulumuka kumene?
6Tonsefe tasanduka ngati anthu oipitsidwa,
ndipo ntchito zathu zonse zabwino
zakhala ngati nsanza zauve.
Tonsefe tikufota ngati masamba,
tikuuluzika ndi machimo athu,
ngati tikuuluzika ndi mphepo.
7Palibe amene amatamira dzina lanu popemphera,
kapena amene amatekeseka
nzopempha chithandizo kwa Inu.
Mwatifulatira
ndipo mwatisandutsa akapolo a machimo athu.
8Komabe Inu Chauta, ndinu Atate athu.
Ife tili ngati mtapo,
Inu muli ngati woumba.
Mudatipanga tonse ndi manja anu.
9Motero musatikwiyire kopitirira,
ndipo musakumbukire machimo athu mpaka muyaya.
Tapota nanu mutiganizireko,
tonsefetu ndife anthu anu.
10Mizinda yanu yoyera yasanduka chipululu,
Ziyoni wasanduka thengo,
Yerusalemu wasanduka wamasiye.
11Nyumba yathu yoyera ndi yokongola,
m'mene makolo athu ankakutamandirani,
yapsa ndi moto.
Malo onse amene tinkaŵakonda asanduka bwinja.
12Kodi Inu Chauta, simukuvutika nazo zimenezi?
Monga mudzangokhala chete nkumatizunza mwankhanza?
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.