Neh. 12 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mndandanda wa ansembe ndi Alevi

1Ansembe ndi Alevi, amene adabwerera pamodzi ndi Zerubabele mwana wa Sealatiele, ndiponso ndi Yesuwa, anali aŵa: Seraya, Yeremiya, Ezara,

2Amariya, Maluki, Hatusi,

3Sekaniya, Rehumu, Meremoti,

4Ido, Ginetoyi, Abiya,

5Miyamini, Maadiya, Biliga,

6Semaya, Yoyaribu, Yedaya,

7Salu, Amoki, Hilikiya, ndi Yedaya. Ameneŵa anali atsogoleri pakati pa ansembe ndi achibale ao pa nthaŵi ya Yesuwa.

8Alevi anali aŵa: Yesuwa, Binuyi, Kadimiyele, Serebiya ndi Yuda. Panalinso Mataniya, amene ankayang'anira za maimbidwe a nyimbo zachiyamiko, pamodzi ndi anzakewo.

9Abale ao, Bakibukiya ndi Uni, ankaimba molandizana nawo pa nthaŵi ya chipembedzo.

Zidzukulu za Yesuwa mkulu wa ansembe onse

10Yesuwa adabereka Yoyakimu, Yoyakimu adabereka Eliyasibu, Eliyasibu adabereka Yoyada,

11Yoyada adabereka Yonatani ndipo Yonatani adabereka Yaduwa.

Atsogoleri a mafuko a ansembe

12Pa nthaŵi ya Yoyakimu, mkulu wa ansembe, atsogoleri a mabanja a ansembe anali aŵa: Mtsogoleri wa fuko la Seraya anali Meraya. Wa fuko la Yeremiya, anali Hananiya.

13Wa fuko la Ezara anali Mesulamu, wa fuko la Amariya anali Yehohanani.

14Wa fuko la Maluki anali Yonatani, wa fuko la Sebaniya anali Yosefe.

15Wa fuko la Harimu anali Adina, wa fuko la Meraiyoti anali Helikai.

16Wa fuko la Ido anali Zekariya, wa fuko la Ginetoni anali Mesulamu.

17Wa fuko la Abiya anali Zikiri, wa fuko la Miniyamini, wa fuko la Mowadiya anali Pilitai.

18Wa fuko la Biliga anali Samuwa, wa fuko la Semaya anali Yehonatani.

19Wa fuko la Yoyaribu anali Matenai, wa fuko la Yedaya anali Uzi.

20Wa fuko la Salai anali Kalai, wa fuko la Amoki anali Eberi.

21Wa fuko la Hilikiya anali Hasabiya ndipo wa fuko la Yedaya anali Netanele.

Maina a mabanja a ansembe ndi a Alevi

22Pa nthaŵi ya Eliyasibu, Yoyada, Yohanani ndi Yaduwa, amene anali akulu a ansembe, padalembedwa maina a atsogoleri a mabanja a Alevi ndi a ansembe, mpaka pa nthaŵi imene mfumu Dariusi wa ku Persiya ankalamulira.

23Adzukulu a Levi, makamaka atsogoleri a mabanja ao, adalembedwa m'buku la Mbiri, mpaka pa nthaŵi ya Yohanani mwana wa Eliyasibu.

Kugaŵa ntchito za ku Nyumba ya Mulungu

24Atsogoleri a Alevi, Hasabiya, Serebiya ndi Yesuwa mwana wa Kadimiyele, ankathandizana ndi abale ao poimba nyimbo zotamanda ndi zothokoza, monga momwe Davide, munthu wa Mulungu, adaaŵalamulira kuti gulu liziimba molandizana ndi gulu linzake.

25Mataniya, Bakibukiya, Obadiya, Mesulamu, Talimoni ndi Akubu, anali olonda nyumba zosungiramo chuma pa zipata za ku Nyumba ya Mulungu.

26Ameneŵa ndiwo adaalipo pa nthaŵi ya Yoyakimu mwana wa Yesuwa, mwana wa Yozadaki, ndiponso pa nthaŵi ya bwanamkubwa Nehemiya ndi wansembe Ezara amene analinso katswiri wa malamulo.

Kuperekedwa kwa khoma lozinga mzinda

27Pamene anthu adati apereke kwa Mulungu khoma lozinga mzinda wa Yerusalemu, adaitana Alevi kuchokera konse kumene ankakhala, kuti abwere ku Yerusalemu kudzachita mwambo wopereka khomalo mokondwera, mothokoza ndiponso poimba pamodzi ndi ziwaya zamalipenga, azeze ndi mapangwe.

28Tsono anthu a m'mabanja a Levi oimba nyimbo, adasonkhana pamodzi, kuchokera ku malo onse ozungulira Yerusalemu, ndiponso ku midzi ya Anetofati.

29Kudabwera enanso ochokera ku Betegiligala, ku Geba, ndi ku Azimaveti, pakuti oimba nyimbo anali atamanga midzi yao pozungulira Yerusalemu.

30Tsono ansembe ndi Alevi adachita mwambo wa kudziyeretsa. Mwambowu adachitiranso anthu, ndiponso zipata ndi khoma la mzinda.

31Ineyo ndidadza nawo akuluakulu a ku dziko la Yuda ndipo ndidakwera nawo pa khoma. Ndidasankha magulu aŵiri mwa iwo, kuti aziyenda mu mdipiti ndi kumathokoza Mulungu. Mdipiti wina unkadzera cha ku dzanja lamanja pa khoma mpaka kukafika ku Chipata cha Kudzala.

32Pambuyo pao pankadza Hosaya ndi theka la akuluakulu aja,

33ndiponso Azariya, Ezara, Mesulamu,

34Yuda, Benjamini, Semaya ndi Yeremiya.

35Ena mwa ana a ansembe amene ankaimba malipenga anali aŵa: Zekariya mwana wa Yonatani, mwana wa Semaya, mwana wa Mataniya, mwana wa Mikaya, mwana wa Zakuri, mwana wa Asafu.

36Panali achibale ao aŵa: Semaya, Azarele, Milalai, Gilalai, Maai, Netanele, Yuda, ndi Hanani. Iwowo ankanyamula zoimbira zopangidwa ndi Davide, munthu wa Mulungu uja. Mlembi Ezara ndiye ankaŵatsogolera.

37Kuchokera ku Chipata cha Kasupe, adakwera pa makwerero opita ku mzinda wa Davide, pa njira yotsatira khoma, chakumtunda kwa nyumba ya Davide, mpaka kukafika ku Chipata cha Madzi, kuvuma kwa mzinda wa Yerusalemu.

38Mdipiti wina wa anthu othokoza Mulungu udadzera chakumanzere kwa khomalo, ndipo ine ndidautsata pambuyo, poyenda pa khoma pamodzi ndi theka lina la akuluakulu. Tidapitirira Nsanja ya Ng'anjo, kukafika ku Khoma Lotambasuka.

39Tidadzeranso pa Chipata cha Efuremu, pa Chipata Chakale, pa Chipata cha Nsomba, pa Nsanja ya Hananele, pa Nsanja ya Zana, mpaka kukafika ku Chipata cha Nkhosa. Ndipo potsiriza tidakaima ku Chipata cha Mlonda.

40Choncho magulu othokoza aŵiri onsewo adakaimirira pafupi ndi Nyumba ya Mulungu. Pamodzi ndi ine ndi theka la akuluakulu aja,

41panali ansembe aŵa akuimba malipenga: Eliyakimu, Maaseiya, Miniyamini, Mikaya, Eliyoenai, Zekariya ndi Hananiya.

42Panalinso ansembe aŵa: Maaseiya, Semaya, Eleazara, Uzi, Yehohanani, Malikiya, Elamu ndi Ezero. Yezeraya ndiye ankatsogolera oimba nyimbo.

43Pa tsiku limenelo anthu adapereka nsembe zochuluka, ndipo adakondwa kwakukulu, popeza kuti Mulungu ndiye adaŵakondwetsa. Akazi nawonso, pamodzi ndi ana, adakondwa, ndipo kukondwa kwa anthu a ku Yerusalemu kudamveka patali.

Kupereka zothandiza popembedza m'Nyumba ya Mulungu

44Tsiku limenelo padasankhidwa anthu oyang'anira zipinda zosungiramo zopereka zaufulu, zipatso zoyamba kucha, ndi zopereka zachikhumi. Anthuwo ankasonkhanitsa zopereka potsata Malamulo a Mose, kuti azipereka kwa ansembe ndi Alevi, kuchokera ku minda ya midzi yonse. Pakuti Ayuda ankakondwera nawo ansembe ndi Alevi otumikirawo,

451Mbi. 25.1-8; 1Mbi. 26.12 chifukwa ankachita zimene Mulungu wao adaalamula, makamaka mwambo wopatulira zinthu. Oimba nyimbo ndiponso alonda a ku Nyumba ya Mulungu nawonso ankagwira ntchito zao potsata lamulo la Davide ndi Solomoni mwana wake.

46Pa nthaŵi ya Davide ndi Asafu, panali mtsogoleri wa anthu oimba nyimbo, ndiponso panali nyimbo zotamanda ndi zothokoza Mulungu.

47Pa nthaŵi ya Zerubabele ndi Nehemiya, anthu a m'dziko lonse la Israele ankapereka tsiku ndi tsiku mphatso zofunika kwa anthu oimba nyimbo ndiponso kwa alonda a ku Nyumba ya Mulungu. Ankaikanso padera chigawo cha Alevi, ndipo Aleviwo nawonso ankaika padera chigawo cha ansembe, adzukulu a Aroni.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help