1Yesu adatuluka m'Nyumba ya Mulungu, ndipo pamene ankachoka, ophunzira ake adabwera nkumamuwonetsa kamangidwe ka Nyumbayo.
2Koma Yesu adaŵauza kuti, “Nanga simukuziwona zonsezi? Ndithu ndikunenetsa kuti sipadzatsala konse mwala ndi umodzi womwe pamwamba pa mwala unzake: yonse adzaigumula.”
Za mavuto ndi mazunzo(Mk. 13.3-13; Lk. 21.7-19)3 2Es. 4.51—5.19 Tsono Yesu atakhala pansi, pa Phiri la Olivi, ophunzira ake adadza kwa Iye paokha. Adamufunsa kuti, “Tatiwuzani, zimenezi zidzachitika liti? Tidzaonera chiyani kuti nthaŵi yakwana ya kubweranso kwanu, ndiponso ya kutha kwa dziko lapansi?”
4Yesu adaŵayankha kuti, “Chenjerani kuti wina aliyense asadzakusokezeni.
5Chifukwa kudzafika anthu ambiri m'dzina langa namadzanena kuti, ‘Mpulumutsi wolonjezedwa uja ndine,’ ndipo adzasokeza anthu ambiri.
6Mudzamva phokoso la nkhondo za kufupi kuno ndi mphekesera za nkhondo zakutali. Ndiye inu musadzade nkhaŵa. Zimenezi zidzayenera kuchitika, koma sindiye kuti chimalizo chija chafika kale ai.
72Es. 13.31Mitundu yosiyanasiyana idzaukirana, maiko osiyanasiyana adzamenyana nkhondo. Kudzakhala njala, ndipo kudzachita zivomezi ku malo osiyanasiyana.
8Tsono zonsezitu nkuyamba chabe kwa mavuto.
9 Mt. 10.22 “Pambuyo pake anthu adzakuperekani kuti mukazunzidwe, kenaka adzakuphani. Anthu a mitundu yonse ya anthu adzadana nanu chifukwa cha Ine.
10Pa nthaŵi imeneyo ambiri adzataya chikhulupiriro chao, azidzaperekana nkumadana.
11Kudzaoneka aneneri onama ambiri, amene azidzasokeza anthu ambiri.
12Tsono popeza kuti zoipa zizidzachulukirachulukira, chikondi chizidzacheperachepera pakati pa anthu.
13Mt. 10.22Koma yemwe adzalimbikire mpaka potsiriza, ameneyo ndiye adzapulumuke.
14Ndipo Uthenga Wabwinowu wonena za ufumu wa Mulungu udzalalikidwa pa dziko lonse lapansi, kuti anthu a mitundu yonse apezepo umboni. Pamenepo ndiye chimalizo chidzafike.”
“Chosakaza chonyansa”(Mk. 13.14-23; Lk. 21.20-24)15 Dan. 9.27; 11.31; 12.11; 1Am. 1.54; 6.7 “Mudzaona ‘Chosakaza chonyansa chija’ chimene mneneri Daniele adaanena, atachiimika m'Nyumba ya Mulungu. (Amene ukuŵerengawe, umvetse bwino.)
16Pamenepo amene ali ku Yudeya athaŵire ku mapiri.
17Lk. 17.31Amene ali padenga pa nyumba yake, asatsike nkuloŵanso m'nyumba mwake kuti akatenge katundu.
18Yemwe ali ku munda, asabwererenso ku nyumba kuti akatenge mwinjiro.
19Ali ndi tsoka azimai amene adzakhale ndi pathupi, ndiponso azimai oyamwitsa ana masiku amenewo.
20Pempherani kuti nthaŵi pamene muzidzathaŵa, isadzakhale nyengo yachisanu, kapena pa tsiku la Sabata.
21Dan. 12.1; Chiv. 7.14Chifukwa masautso amene adzaoneka masiku amenewo, sanaonekepo chilengedwere dziko lapansi mpaka pano, ndipo sadzaonekanso.
22Masiku amenewo, akadapanda kuŵachepetsa, sakadapulumukapo munthu ndi mmodzi yemwe. Koma Mulungu adzaŵachepetsa masikuwo chifukwa cha anthu amene Iye adaŵasankha.
23“Pa nthaŵi imeneyo wina akadzakuuzani kuti, ‘Ali panotu Khristu uja! Uyo ali apoyo!’ musadzakhulupirire.
24Chifukwa kudzaoneka anthu onama omanena kuti ‘Ndine Khristu uja,’ kapena kuti, ‘Ndine mneneri.’ Anthuwo azidzachita ntchito zamphamvu ndiponso zinthu zozizwitsa, kuti ngati nkotheka asokeze ngakhale osankhidwa a Mulungu.
25Mvetsetsani, Ine ndiye ndakuuziranitu zimenezi.
26 Lk. 17.23, 24 “Nchifukwa chake, anthu akadzakuuzani kuti, ‘Inu, Khristu ali ku chipululu,’ musadzapiteko. Kapena akadzati, ‘Ali m'kati mwa nyumba,’ musadzakhulupirire.
27Mwana wa Munthutu kubwera kwake kudzakhala monga muja mphezi imang'animira ndi kuŵala kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe.
28 Lk. 17.37 “Paja adati, Kulikonse kumene kwafera chinthu, miphamba imasonkhana kumeneko.”
Za kubwera kwa Mwana wa Munthu(Mk. 13.24-27; Lk. 21.25-28)29 Yes. 13.10; Yow. 2.10, 31; 3.15; Chiv. 6.12; Yes. 13.10; Ezek. 32.7; Yow. 2.10; 3.15; Yes. 34.4; Chiv. 6.13 “Akadzangotha mavuto a masiku amenewo, dzuŵa lidzada, mwezi udzaleka kuŵala, nyenyezi zidzagwa kuchokera ku thambo, ndipo mphamvu zamumlengalenga zidzagwedezeka.
30Dan. 7.13; Zek. 12.10-14; Chiv. 1.7Pamenepo chizindikiro cha Mwana wa Munthu chidzaoneka ku thambo. Anthu a mitundu yonse ya pansi pano adzayamba kulira, ndipo adzaona Mwana wa Munthu akubwera pa mitambo ali ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu.
31Kudzamveka lipenga lamphamvu, ndipo Iye adzatuma angelo ake, kuti akasonkhanitse osankhidwa ake kuchokera ku mbali zonse, kuyambira ku malekezero ena a dziko lapansi mpaka ku malekezero ake enanso.”
Phunziro la mkuyu(Mk. 13.28-31; Lk. 21.29-33)32“Yang'anani mkuyu kuti mutengerepo phunziro. Mukamaona kuti nthambi zake zayamba kukhala zanthete, ndipo masamba akuphuka, mumadziŵa kuti chilimwe chayandikira.
33Momwemonso, mukadzaona zonse ndanena zija, mudzadziŵe kuti Mwana wa Munthu ali pafupi, ali pakhomo penipeni.
34Ndithu ndikunenetsa kuti zonsezi zidzaoneka anthu a mbadwo unoŵa asanamwalire onse.
35Thambo ndi dziko lapansi zidzatha, koma mau anga sadzatha mphamvu konse.”
Tsiku lomaliza silidziŵika(Mk. 13.32-37; Lk. 17.26-30, 34-36)36“Koma za tsiku lake kapena nthaŵi yake, palibe amene amadziŵa. Angelo omwe akumwamba sadziŵa. Ngakhale Ineyo Mwanane sindidziŵa; amadziŵa ndi Atate okha basi.
37Gen. 6.5-8 Kudza kwa Mwana wa Munthu kudzakhala monga momwe zinthu zidaayendera pa nthaŵi ya Nowa.
38Masiku amenewo, chisanafike chigumula, anthu ankangodya ndi kumwa, ankakwatira ndi kukwatiwa, mpaka tsiku limene Nowa adaloŵa m'chombo.
39Gen. 7.6-24Sadazindikire kanthu mpaka chigumula chidafika nkuŵaononga onse. Zidzateronso pamene Mwana wa Munthu adzabwera.
40Pa nthaŵi imeneyo anthu aŵiri adzakhala ali m'munda, mmodzi adzamtenga, winayo nkumusiya.
41Azimai aŵiri adzakhala akusinja, mmodzi adzamtenga, winayo nkumusiya.
42“Nanunso tsono, khalani maso, chifukwa simudziŵa tsiku limene Ambuye anu adzabwere.
43Lk. 12.39, 40Koma dziŵani kuti mwini nyumba akadadziŵa nthaŵi yofika mbala, bwenzi atakhala maso, osalola kuti mbala imuthyolere nyumba.
44Choncho inunso muzikhala okonzeka, pakuti Mwana wa Munthu adzabwera pa nthaŵi imene inu simukuyembekeza.”
Za wantchito wokhulupirika ndi wina wosakhulupirika(Lk. 12.41-48)45“Tsono wantchito wokhulupirika ndi wanzeru ndani, amene mbuye wake adamuika kuti aziyang'anira onse a m'nyumba mwake, nkumaŵagaŵira chakudya chao pa nthaŵi yake?
46Ngwodala wantchito ameneyo, ngati mbuye wake pofika adzampeza akuchitadi zimenezi.
47Ndithu ndikunenetsa kuti adzamuika woyang'anira chuma chake chonse.
48Koma ngati ndi wantchito woipa, mumtima mwake azidzati, ‘Mbuye wanga akuchedwa.’
49Ndiye adzayamba kumenya antchito anzake, ndiponso kumadya ndi kumamwa pamodzi ndi zidakwa.
50Tsono mbuye wake adzangoti mbwe mwadzidzidzi, pa tsiku limene iye sakumuyembekeza.
51Choncho adzamlanga koopsa, ndipo adzamtaya ku malo a anthu achiphamaso. Kumeneko adzalira ndi kukukuta mano.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.