1Munthu wosauka akakhala wanzeru, amayenda mogundika,
ndipo amaŵerengedwa pakati pa akuluakulu.
2Usatamande munthu chifukwa cha kukongola kwake,
ndipo usadane ndi munthu chifukwa cha maonekedwe chabe.
3Njuchi njaing'ono pakati pa zouluka,
komabe uchi wake ngwotsekemera kupambana
zotsekemera zonse.
4Usanyade chifukwa cha zovala zako zokongola,
kapena kudzitukumula ukalandira ulemu.
Paja ntchito za Ambuye nzodabwitsa,
komabe nzobisika kwa anthu.
5Mafumu ambiri adaŵatsitsa,
woloŵa ufumu nkukhala munthu wosayembekezeka.
6Olamulira ambiri adaŵalanda ulemerero wao,
anthu otchuka adaŵapereka m'manja mwa ena.
7Usayambe nkudzudzula usanafufuze nkhani.
Uyambe waganizira bwino, kenaka ndiye kudzudzula.
8Usanayankhe, yamba wamvetsera bwino,
mnzako akamalankhula, usamdule pakamwa.
9Usatengeke ndi zinthu zosakukhudza,
anthu ochimwa akamakangana, iwe usaloŵerepo.
10Mwana wanga, usatanganidwe ndi zambiri.
Ukachulutsa zochitachita, udzagwa m'mavuto.
Ngakhale ufulumire chotani, sudzazitha,
ngakhale uzithaŵe, sudzapulumuka.
11Ena amagwira ntchito mwamphamvu ndi mofulumira,
komabe amatsalira kumbuyo.
Za kukhulupirira Mulungu yekha12Wina amakhala wopanda nzeru, wosoŵa chithandizo,
wopanda mphamvu ndiponso mmphaŵi zedi,
komabe Ambuye amamuyang'ana ndi diso lachifundo,
ndipo amamchotsera mavuto ake.
13Amamkweza kwambiri,
mpaka anthu onse kumadabwa.
14Zabwino ndi zoipa, moyo ndi imfa, umphaŵi ndi chuma,
zonsezi zimachokera kwa Ambuye.
15Luntha, kumvetsa zinthu, ndi kudziŵa Malamulo,
zonsezi zimachokera kwa Ambuye.
Chikondi ndi kuchita ntchito zabwino
zimenezinso zimachokera kwa Ambuye.
16Kupusa ndi mdima adazilengera anthu ochimwa.
Anthu okondwerera zoipa, adzakalambira m'zoipazo.
17Mphatso zimene Mulungu amapatsa anthu omukonda nzokhalitsa.
Mulungu akakondwera nawe, uzidzakhoza nthaŵi zonse.
18 Mas. 49.10; Lk. 12.16-21 Munthu wina adalemera
chifukwa cha kuchenjera ndi kudzimana,
tsono malipiro ake ndi aŵa:
19Angathe kunena kuti,
“Tsopano nditambalala,
ndikondwerere zimene ndidapata.”
Komabe sangadziŵe kuti chumacho adzakhala nacho
nthaŵi yaitali bwanji.
Adzachisiyira ndithu ena, iyeyo nkufa.
20Uzilimbikira kuchita bwino ntchito yako
nkumaikapo mtima.
Ukalambire pa ntchito yakoyo.
21Usasirire kukhoza kwa anthu ochimwa.
Iwe khulupirira Ambuye ndi kusamala zako.
Kwa Ambuye nchinthu chapafupi,
angathe kulemeretsa mmphaŵi pa kamphindi
ndiponso mwadzidzidzi.
22Madalitso a Ambuye ndiye mphotho ya munthu
wokonda Mulungu.
Pa nthaŵi yosakula Mulungu amaŵapindulitsa madalitsowo.
23Usanene kuti, “Kodi ine ndikusoŵa chiyani?
Nanga m'tsogolo muno ndidzakhala pabwino chotani?”
24Usanene kuti,
“Ine ndine chikwanekwane,
ndi tsoka lanjinso lingandigwere?”
25Munthu zikamamuyendera bwino zonse,
mavuto onse amaiŵalika.
Koma pa nthaŵi ya mavuto,
sakumbukiranso kuti
zinthu zinkamuyendera bwino.
26Pa nthaŵi imene munthu alikufa,
nkwapafupi kwa Ambuye kumlipira
potsata zimene adachita.
27Kanthaŵi kakang'ono ka mavuto
kamaiŵalitsa zokoma zonse.
Pamene munthu akutsirizika,
ndi pamene makhalidwe ake amadziŵika.
28Munthu asanafe, osamutchula wodala,
munthu amadziŵika ndi mathero ake.
Osaŵakhulupirira anthu ochimwa29Usamangoloŵetsa munthu aliyense
m'nyumba mwako,
chifukwa anthu onyenga
ali ndi misampha yambiri.
30Mtima wa munthu wonyada
uli ngati nkhwali yam'chitatanga,
munthuyo ali ngati mzondi
amene akungoyembekeza kugwa kwako.
31Amafunafuna mpata woti apotoze zabwino
kuti zikhale zoipa,
ndipo amadzudzula anthu ochita zabwino.
32Kambaliŵali ka moto kamayatsa makala ambiri,
chonchonso munthu woipa amalalira anthu kuti aŵaphe.
33Uchenjere naye munthu woipa
chifukwa ali ndi zolinga zoipa.
Ukapanda kutero
adzakuwonongera mbiri yako mpaka muyaya.
34Ukaloŵetsa munthu wachilendo m'nyumba mwako,
adzakudzetsera mavuto,
adzakuputira mikangano
pakati pa iwe ndi a m'banja mwako.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.