1“Ndidalonjezana ndi maso anga,
ndikadatha bwanji kupenyetsetsa namwali?
2Kodi Mulungu kumwamba akadandisungira zotani?
Kodi Mphambe kumwamba akadandikonzera zabwino zanji?
3Wosalungama tsoka limamgwera,
wochita zoipa amaonongeka.
4Koma Mulungu amaona zochita zanga,
amadziŵa mayendedwe anga onse.
5“Sindidachite zachiphamaso,
sindidayesepo kunyenga anthu.
6Mulungu andiyese pa sikelo ya chilungamo,
adziŵe kuti ndine wangwiro.
7Ngati mayendedwe anga asempha njira,
ngati mtima wanga wakhumbira zinthu molakwa,
ndipo ngati ndachita choipa chilichonse,
8pamenepo zimene ine ndidabzala adye ndi ena,
zomera zanga zizulidwe.
9“Ngati mtima wanga udanyengedwapo ndi mkazi,
ndipo ngati ndidalalira pa khomo la mnansi wanga,
10pamenepo mkazi wanga aphikire mwamuna wina chakudya,
ndipo azigona naye.
11Pakuti limenelo likadakhala tchimo loopsa zedi,
ukadakhala mlandu umene oweruza
amaperekapo chilango chachikulu.
12Kuipa kwake kukadakhala ngati moto woonongeratu,
ukadapsereza zinthu zanga zonse.
13“Ngati ndidapondereza mlandu wa mtumiki wanga,
wamwamuna kapena wamkazi,
pamene adabwera kwa ine ndi madandaulo ake,
14ndidzatani ine pamene Mulungu adzadzambatuke?
Nanga akadzandifunsa, ndidzayankha chiyani?
15Kodi amene adapanga ine m'mimba mwa amai anga
si yemwe adapanganso iyeyo?
Kodi si mmodzi yemweyo amene adatilenga tonsefe?
16 Tob. 4.7-11, 16 “Ngati amphaŵi ndidaŵamana zimene ankakhumba,
kapena kuŵagwiritsa mwala mwankhanza akazi amasiye,
17ngati chakudya ndidadya ndekha,
ana amasiye osachilaŵa,
18pakuti anawo ndidaŵalera ngati bambo wao
ndi kuŵasamalira bwino chibadwire chao,
19ngati ndidaona wina aliyense
akuzunzika ndi usiŵa,
kapena munthu wosauka alibe chofunda,
20ngati iyeyo sadanditamande
chifukwa chomupatsa chovala,
ndipo ngati sindidamfunditsa
ndi nsalu za ubweya wa nkhosa,
21ngati ndidaopsezapo mwana wamasiye,
podziŵa kuti ku bwalo lamilandu sadzanditsutsa,
22pamenepo phewa langa lipokonyoke,
mkono wanga ukonyoke m'maluma mwake.
23Pakutitu tsoka lochokera kwa
Mulungu ndimachita nalo mantha,
sindikadatha kuchita kanthu
kalikonse koipa pamaso pake.
24 Mphu. 31.5-10 “Sindidaike mtima pa chuma,
kapena kudalira golide wabwino kwambiri.
25Zedi, sindidakondwere chifukwa choti
chuma changa chinali chambiri,
kapena chifukwa choti manja anga adapata zambiri.
26Poona dzuŵa likuŵala,
kapena mwezi ukuwonetsa kukongola kwake,
27mtima wanga ukadakopeka nazo,
dzanja langa nkuliika pakamwa mozilemekeza,
28bwenzi limeneli lili tchimo loti
aweruzi andilange nalo,
chifukwa ndikadakhala wonama kwa Mulungu wakumwamba.
29“Sindidakondwerere kuwonongeka kwa mdani wanga.
Sindidasekere tsoka litamgwera.
30Sindidachimwe ndi pakamwa panga,
potemberera mdani wanga kuti aonongeke.
31Amene ndimakhala nawo amadziŵa kuti
ine ndimalandira alendo
ndi kuŵapatsa chakudya chokwanira.
32Alendo sindidaŵasiye panja m'miseu.
Aliyense wofika pakhomo panga ndidampatsa malo ogona.
33Anthu ena amabisa zoipa zao,
koma ine sindidabise cholakwa chilichonse.
34Sindidaope zokambakamba za anthu
kapena zonyoza za banja lina lililonse,
sindidakhale chete kapena kubindikira
m'nyumba chifukwa choopa iwowo.
35“Ha, pakadakhala wina wondimva!
Ndikulumbira kuti ndikulankhula zoona.
Mphambe andiyankhe.
Mdani wanga akadachita kulemba pa kalata
mau ake ondineneza,
36ndikadachita kuipachika kalatayo
paphewa panga monyadira,
ndikadaivalanso kumutu ngati chisoti chaufumu.
37Ndikadamsimbira Mulungu zonse zimene ndachita,
ndikadafika pamaso pake ngati kalonga.
38“Ngati ndidalanda minda ya anthu ena osagula,
ngati ndikulima pa minda ya eniake,
39ngati ndidadya zam'minda osagula,
ngati ndidaphetsa eni mindayo,
40m'mindamo mumere minga m'malo mwa tirigu
mumere namsongole m'malo mwa barele.”
Mau a Yobe athera pano.
Elihu adzudzula Yobe ndi abwenzi aja.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.