1Pambuyo pake Chauta adalamula Mose kuti, “Pita kwa Farao ukamuuze kuti, Chauta akuti, ‘Uŵalole anthu anga apite akandipembedze.
2Ukakana kuŵalola, dziko lako lonse ndidzalilanga polidzaza ndi achule.
3Mtsinje uja udzakhala wodzaza ndi achule. Adzachokera mumtsinjemo namakaloŵa m'chipinda mwako mogona, pabedi pako, m'nyumba za nduna zako ndi za anthu ako, m'malo onse ophikira ndi mophikira buledi momwe.
4Azidzakulumphira iwe, pamodzi ndi anthu ako, ndi nduna zako zonse.’ ”
5Chauta adauzanso Mose kuti, “Uza Aroni kuti, ‘Uloze ndodo yako ku mitsinje, ku ngalande ndi ku zithaphwi ndipo pakhale achule pa dziko lonse la Aejipito.’ ”
6Choncho Aroni adaloza ndodo yake pa madzi, ndipo achule adatuluka, nadzaza dziko lonselo.
7Koma amatsenga aja nawonso adapanga ao achule ndipo adayamba kukwera pa mtunda.
8Pomwepo Farao adaitana Mose ndi Aroni naŵauza kuti, “Pempherani kwa Chauta kuti achuleŵa andichoke ine ndi anthu angaŵa, ndipo ndidzaŵalola anthu anu kuti apite kukapereka nsembe kwa Chauta.”
9Tsono Mose adauza Farao kuti, “Chabwino, mungondiwuza nthaŵi yoti ndikupempherereni inu, nduna zanu ndi anthu anu omwe, kuti achuleŵa akuchokeni, achokenso m'nyumba mwanu, ndipo kuti akakhale mumtsinje mokha.”
10Farao adati, “Maŵa.” Apo Mose adati, “Zidzachitika monga momwe mwaneneramu, ndipo mudzadziŵa kuti palibe Mulungu wina wofanafana ndi Chauta, Mulungu wathu.
11Achulewo adzakuchokani, adzachokanso m'nyumba zanu, m'nyumba za nduna zanu, ndipo azidzangokhala mumtsinje mokha.”
12Pamenepo Mose ndi Aroni adachoka kwa Farao kuja, ndipo adakapempha Chauta kuti achotse achule amene adaatumiza kwa Farao aja.
13Tsono Chauta adachitadi monga momwe Mose adapemphera. Motero achule onse aja amene adaali m'nyumba, pa bwalo ndi m'minda momwe, adafa.
14Aejipito aja adaŵaunjika achulewo milumilu, ndipo dziko lonse lidadzaza ndi chivunde chokhachokha.
15Farao ataona kuti zinthu zayamba kukhala bwino, adaumitsa mtima wake, ndipo sadafunenso kumvera Mose ndi Aroni monga momwe Chauta adaanenera muja.
Nthata16Pamenepo Chauta adalamula Mose kuti, “Uza Aroni asamule ndodo yake ndipo amenye nthaka, motero fumbi lonse lidzasanduka nthata m'dziko lonse la Ejipito.”
17Iwowo adachitadi momwemo. Aroni adasamula ndodo yake ija namenya nthaka. Tsono fumbi lonse lidasanduka nthata, ndipo zidabalalikira pa anthu ndi pa nyama zomwe. Motero fumbi lonse la ku Ejipito lidangokhala nthata zokhazokha.
18Amatsenga aja adayesanso momwemo mwa matsenga ao kuti apange zao nthata, koma adalephera. Ndipo nthatazo zidabalalikira pa anthu ndi nyama zomwe.
19Lk. 11.20 Tsono amatsenga aja adauza Farao kuti, “Zimenezi wachita ndi Mulungu ndithu.” Koma Farao adakhala wokanikabe, ndipo sadamvere zimene Mose ndi Aroni ankanena monga momwe Chauta adaanenera muja.
Mizaza20Apo Chauta adauza Mose kuti “Maŵa m'maŵa ndithu, upite ukakumane ndi Farao pamene akupita ku mtsinje, ukamuuze kuti, ‘Chauta akunena kuti uŵalole anthu anga apite, akandipembedze Ine.
21Ukapanda kulola anthu anga kuti apite, ndidzatumiza mizaza pa iwe, nduna zako, anthu ako ndi m'nyumba mwako. M'nyumba zonse za Aejipito, ngakhalenso pa nthaka yonse imene akukhalapo, padzakhala mizaza yokhayokha.
22Pa tsiku limenelo ndidzapatula dziko la Goseni lokhalamo anthu anga, mwakuti lokhalo lidzakhala lopanda mizaza, kuti iweyo udziŵe kuti Ine ndine Chauta ndipo kuti ndikulamulira pa dziko lapansi.
23Ndidzasiyanitsa ndithu pakati pa anthu anga ndi anthu ako. Chozizwitsa chimenechi chichitika maŵali.’ ”
24Choncho Chauta adachitadi zimenezi, ndipo magulu a mizaza adaloŵa m'nyumba ya Farao, m'nyumba za nduna zake, ndiponso m'dziko lonse la Ejipito. Dziko lonselo lidaipiratu ndi mizazayo.
25Tsono Farao adaitana Mose ndi Aroni naŵauza kuti, “Pitani mukapereke nsembe kwa Mulungu wanu m'dziko mommuno.”
26Koma Mose adayankha kuti, “Sikungakhale bwino konse kuchita zimenezo, chifukwa Aejipito zidzaŵaipira nsembe zimene timapereka kwa Chauta, Mulungu wathu. Tikadzapereka nsembe zimene Aejipito zimaŵanyansa m'maso mwao, kodi iwo sadzatiponya miyala mpaka kutipha?
27Tiyenera kuyenda ulendo wa masiku atatu m'chipululu, kuti tikapereke nsembe kwa Chauta, Mulungu wathu, monga adatilamulira.”
28Farao adati, “Ndidzakulolani kuti mupite mukapereke nsembe kwa Chauta, Mulungu wanu, ku chipululu, koma musapite kutali kwambiri. Tsono mundipempherere.”
29Apo Mose adati, “Malinga ndikachoka pano, ndikukapempha kwa Chauta, ndipo maŵa mizaza ikuchokani inu, nduna zanu ndiponso anthu anu. Koma musatinyengenso ndi kuŵaletsa anthu kupita kuti akapereke nsembe kwa Chauta.”
30Mose atachoka kwa Faraoko, adakapemphera kwa Chauta.
31Motero Chauta adachitadi monga momwe Mose adapemphera. Pomwepo mizaza idamchoka Farao ndi nduna zake ndi anthu ake omwe. Sudatsalepo ndi umodzi omwe.
32Koma ngakhale pa nthaŵi imeneyinso, Farao adakhala wokanikabe, ndipo sadalole kuti Aisraele apite.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.