2 Mbi. 6 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Tsono Solomoni adapemphera nati,

“Inu Chauta, mudanena kuti

mudzakhala mu mdima waukulu.

2Ndiye ine ndakumangirani nyumba yaulemerero,

malo oti muzikhalamo nthaŵi zonse.”

Solomoni alankhula kwa anthu(1 Maf. 8.12-21)

3Tsono mfumuyo idatembenukira anthu aja, nidalitsa msonkhano wonse wa Aisraele, onsewo ali chiliri.

42Sam. 7.1-13; 1Mbi. 17.1-12 Ndipo mfumuyo idati, “Atamandike Chauta, Mulungu wa Aisraele, amene wachitadi ndi dzanja lake zimene adaalonjeza ndi pakamwa pake kwa Davide bambo wanga.

5Paja adaati, ‘Kuyambira tsiku limene ndidatulutsa anthu anga ku Ejipito, sindidasankhepo mzinda pakati pa mafuko onse a Aisraele woti anthu amangemo nyumba m'mene dzina langa lizimvekamo. Ndipo sindidasankhepo munthu woti nkukhala mfumu yomalamulira Aisraele anthu anga.

6Koma ndidasankha Yerusalemu kuti dzina langa lizimveka kumeneko, ndipo ndidasankha Davide kuti azilamulira anthu anga Aisraele.’

7Tsono mumtima mwake bambo wanga Davide ankaganiza zoti amange nyumba yomveketsa dzina la Chauta, Mulungu wa Aisraele.

8Koma Chautayo adauza Davide bambo wanga kuti, ‘Popeza unkaganiza mumtima mwako zoti undimangire nyumba, udachita bwino kumaganiza zimenezo.

9Komabe si ndiwe udzamange nyumbayo, koma mwana wako wamwamuna amene udzabale, ndiye amene adzandimangire nyumba yomveketsa dzina langa.’

10Tsopano Chauta wachitadi zimene adaalonjeza zija. Pakuti ine ndi amene ndaloŵa ufumu m'malo mwa Davide bambo wanga, ndipo ndikulamulira Aisraele pa mpando wa bambo wanga, monga momwe Chauta adaalonjezera. Ndipo ndinedi amene ndamanga Nyumba yomveketsa dzina la Chauta, Mulungu wa Aisraele.

11Tsono m'menemo ndaikamo Bokosi lija m'mene muli mau a chipangano cha Chauta chimene adachita ndi Aisraele.”

Pemphero la Solomoni(1 Maf. 8.22-53)

12Pambuyo pake Solomoni adaimirira patsogolo pa guwa la Chauta, msonkhano wonse wa Aisraele akuwona, ndipo adatambalitsa manja ake.

13Iyeyo anali atapanga nsanja yamkuŵa, kutalika kwake mamita aŵiri nkanthu, m'mimba mwake mamita aŵiri nkanthu, msinkhu wake mita limodzi ndi theka, ndipo anali ataimanga m'kati mwenimweni mwa bwalo. Adakwera pansanjapo, ndipo adagwada pa maondo ake, msonkhano wonse wa Aisraele ukuwona, iye anakweza manja ake kumwamba.

14Tsono adati, “Inu Chauta, Mulungu wa Aisraele, palibe Mulungu wina wonga inu kumwamba kapena pa dziko lapansi. Mumasunga chipangano ndi kuwonetsa chikondi chosasinthika kwa atumiki anu amene amayenda pamaso panu ndi mtima wao wonse.

15Inu mwachitadi zimene mudaauza Davide bambo wanga, mtumiki wanu. Zimene zija mudaalankhula ndi pakamwa panu, dzanja lanu lazichitadi monga onse akuwoneramu lero lino.

161Maf. 2.4 Tsono Inu Chauta, Mulungu wa Aisraele, mukumbukire zimene zija mudalonjeza bambo wanga, pamene mudati, ‘Sipadzasoŵa munthu pa banja lako wokhala pamaso panga pa mpando waufumu wa Israele; malinga ana ako akamasamala mkhalidwe wao ndi kumayenda motsata malamulo anga monga momwe iweyo wayendera pamaso panga.’

17Nchifukwa chake tsono, Inu Chauta, Mulungu wa Aisraele, zimene mudalankhula ndi Davide mtumiki wanu zichitikedi.

18 2Mbi. 2.6 “Kodi Mulungu angakhale nawodi anthu pa dziko lapansi? Onani kumwamba ndi kumwambamwamba komwe sikukukwanirani kukhala, nanji tsono nyumba imene ndakumangiraniyi.

19Komabe Inu Chauta, Mulungu wanga imvani pemphero la ine mtumiki wanu ndi kupemba kwanga. Mverani kulira kwanga ndiponso pemphero limene ine, mtumiki wanu ndikupemphera pamaso panu.

20Deut. 12.11 Usana ndi usiku maso anu azikhala otsekuka, kuyang'ana Nyumba imeneyi, malo amene Inu mudanena kuti mudzamveketsamo dzina lanu. Imvani pemphero limene mtumiki wanu akupemphera ku malo ano.

21Muzimva mapemphero opemba a mtumiki wanu ndiponso a anthu anu Aisraele, akamapemphera ku malo ano. Ndithu mumve kumwambako kumene mumakhala, ndipo mukamva, mutikhululukire.

22“Tsono munthu akachimwira mnzake, nauzidwa kuti alumbire, akabwera kudzalumbira patsogolo pa guwa lanu m'Nyumba muno,

23pamenepo Inu mumve kumwambako, ndipo muchitepo kanthu ndi kuŵaweruza atumiki anuwo. Wochimwa mugamule kuti ngwolakwa ndipo mumlange chifukwa cha zolakwa zakezo. Koma wosachimwayo mugamule kuti ngwopanda mlandu, ndipo mumpatse mphotho molingana ndi makhalidwe akewo.

24“Anthu anu Aisraele atagonjetsedwa ndi adani ao chifukwa chakuti adakuchimwirani, pambuyo pake nkutembenuka ndi kutamanda dzina lanu, napemphera ndi kupemba kwa Inu okhala m'Nyumba muno,

25pamenepo Inuyo mumve kumwambako, ndipo mukhululukire tchimo la anthu anu Aisraele. Kenaka muŵabwezenso ku dziko limene Inu mudaŵapatsa iwowo ndi makolo ao.

26“Kumwamba kukatsekeka, mvula nkupanda kugwa, chifukwa chakuti anthuwo adakuchimwirani, pambuyo pake nkupemphera choyang'ana ku malo ano ndi kutamanda dzina lanu, natembenuka nkusiya tchimo laolo Inu mukuŵazunza,

27pamenepo Inuyo mumve kumwambako, mukhululukire tchimo la atumiki anu, anthu anu Aisraele. Inu muziŵaphunzitsa njira yabwino yoti aziyendamo, ndipo muzigwetsa mvula pa dziko lanu limene mudapatsa anthu anu kuti likhale choloŵa chao.

28“Mwina mwake m'dzikomo mudzaloŵa njala, mliri, dzimbiri lapambeu kapena chinoni, dzombe kapena kapuchi. Mwina adani ao adzaŵazinga ku mzinda wao wina uliwonse. Mwina padzakhala mliri wamtundu wina kapena matenda a mtundu uliwonse.

29Tsono, chodandaula kapena chopembera chingakhale chotani, pempherolo lingakhale la munthu m'modzi kapena la anthu anu onse Aisraele wina aliyense akapemphera mopemba, akuzindikira zovuta za mumtima mwake, natambalitsa manja choloza ku Nyumba ino,

30pamenepo Inuyo mumve kumwambako kumene mumakhala. Mukhululuke ndipo muchitepo kanthu. Muchitire aliyense potsata makhalidwe ake onse pakuti Inu mukudziŵa mtima wake. Inu nokha ndinu amene mumadziŵa mitima ya anthu.

31Motero anthuwo azikuopani ndi kumayenda m'njira zanu masiku onse a moyo wao pomakhala m'dziko limene Inu mudapatsa makolo athu.

32“Chimodzimodzinso mwina mlendo amene sali mmodzi wa Aisraele anthu anu, adzabwera kuchokera ku dziko lakutali, atamva za dzina lanu lotchuka ndiponso dzanja lanu lamphamvu ndi lochita zazikulu. Iyeyo akadzabwera kudzapemphera ku Nyumba ino,

33Inu mumve kumwambako kumene mumakhala, ndipo mumchite mlendoyo zonse zimene wakupemphani. Muchite zimenezi kuti anthu onse a pa dziko lapansi adziŵe dzina lanu, ndipo azikumverani monga m'mene amachitira Aisraele anthu anu, ndipo adziŵe kuti Nyumba imene ndaimangayi imadziŵika ndi dzina lanu.

34“Anthu anu akamapita ku nkhondo kukamenyana ndi adani ao, kulikonse kumene mungaŵatume, akapemphera kwa Inu choyang'ana ku mzinda uno umene Inu mudausankha, ndiponso ku Nyumba imene ndakumangiraniyi yomveketsa dzina lanu,

35pamenepo Inuyo mumve kumwambako pemphero lao ndi kupemba kwao, ndipo muŵapambanitse.

36“Mwina anthuwo adzakuchimwirani, poti palibe munthu amene sachimwa, ndiye Inuyo nkudzaŵakwiyira ndi kuŵapereka kwa adani, kuti aŵatenge ukapolo kupita nawo ku dziko lakutali kapena lakufupi.

37Tsono, ali akapolo kuchilendoko akazindikira kuchimwa kwao natembenuka mtima ndi kupemphera kwa Inu modzichepetsa m'dziko laukapololo nkumanena kuti, ‘Tachimwa, tachita zosayenera, tapalamula ndithu,’

38anthuwo akabwerera kwa Inu ndi maganizo ao onse ndi mtima wao wonse, m'dziko laukapolo kumene iwo aja adaŵatengera, ndipo akapemphera choloza ku dziko lao limene Inu mudapatsa makolo ao, ku mzinda umene Inu mudausankha, ndiponso ku Nyumba imene ine ndakumangiraniyi yomveketsa dzina lanu,

39pamenepo Inuyo kumwambako, kumene mumakhala, mumve pemphero lao ndi kupemba kwao. Muŵachitire zolungama, ndipo muŵakhululukire anthu anu okuchimwiraniwo.

40Tsopano, Inu Mulungu wanga, tsekulani maso anu, ndipo makutu anu amve pemphero ili la ku malo ano.

41 Mas. 132.8-10 “Inu Chauta, dzambatukani tsopano,

mupite ku malo anu kumene mumapumulako,

Inuyo ndi bokosi la mphamvu zanu.

Inu Chauta, ansembe anu avale chilungamo,

anthu okutumikirani akondwe nazo zabwino zanu.

42Inu Chauta musati mumfulatire wodzozedwa wanu.

Kumbukirani chikondi chanu chosasinthika

kwa mtumiki wanu Davide.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help