1 2Sam. 6.2-4; 1Mbi. 13.5-7 Anthu a ku Kiriyati-Yearimu adadzatenga Bokosi lachipanganolo nakafika nalo ku nyumba ya Abinadabu pa phiri. Ndipo adasankha mwana wake, Eleazara, kuti akhale woyang'anira Bokosilo.
Samuele atsogolera Aisraele.2Kuyambira tsiku limene Bokosi lachipangano lija lidakhala ku Kiriyati-Yearimu, padapita nthaŵi yaitali ya zaka makumi aŵiri. Ndipo Aisraele onse adadandaulira Chauta kuti aŵathandize.
3Pamenepo Samuele adauza mtundu wonse wa Aisraele kuti, “Ngati mukubwerera kwa Chauta ndi mtima wanu wonse, muchotse milungu yachilendo ndi Aasitaroti pakati panu, mtima wanu ukhale pa Chauta ndi kutumikira Iye yekha. Mukatero adzakupulumutsani kwa Afilisti.”
4Choncho Aisraele adachotsa Abaala ndi Aasitaroti, nayamba kutumikira Chauta yekha.
5Tsono Samuele adati, “Sonkhanitsani mtundu wonse wa Aisraele ku Mizipa, ndipo ine ndikupemphererani kwa Chauta.”
6Choncho adasonkhana ku Mizipa, natunga madzi ndi kuŵathira pansi pamaso pa Chauta mopepesera, ndipo adasala chakudya tsiku limenelo, namanena kuti, “Tidachimwira Chauta.” Nku Mizipako kumene Samuele ankaweruza milandu ya Aisraele.
7Afilisti atamva kuti Aisraele adasonkhana ku Mizipa, akalonga a Afilisti adapita kuti akachite nawo nkhondo. Aisraele atamva zimenezi, adachita nawo mantha Afilistiwo,
8ndipo adauza Samuele kuti, “Musaleke kutidandaulira kwa Chauta, Mulungu wathu, kuti atipulumutse kwa Afilistiŵa.”
9Mphu. 46.16-18Choncho Samuele adatenga mwanawankhosa woyamwa, nampereka wathunthu ngati nsembe yopsereza kwa Chauta. Adapempherera Aisraele kwa Chauta, ndipo Chauta adamuyankha.
10Pamene Samuele ankapereka nsembe yopsereza ija, Afilisti adasendera pafupi kuti amenyane ndi Aisraele. Koma Chauta adaŵaopsa Afilistiwo ndi mau onga bingu, naŵasokoneza, mwakuti adamwazikana pamaso pa Aisraele.
11Tsono Aisraele adatuluka ku Mizipa naŵalondola Afilistiwo, mpaka kubzola Betekara, akuŵapha njira yonse.
12Pambuyo pake Samuele adatenga mwala, nauimiritsa pakati pa Mizipa ndi Sene, ndipo adautcha dzina loti Ebenezeri, ndiye kuti “Mwala wachithandizo,” pakuti adati, “Mpaka pano Chauta wakhala akutithandiza.”
13Choncho Afilisti adagonjetsedwa, ndipo sadaloŵenso m'dziko la Aisraele. Chauta ndiye ankalimbana ndi Afilisti nthaŵi yonse Samuele ali moyo.
14Mizinda imene Afilisti anali atalanda idabwezedwanso kwa Aisraele, kuchokera ku Ekeroni mpaka ku Gati. Motero Aisraele adapulumutsa dziko lao kwa Afilisti. Panalinso mtendere pakati pa Aisraele ndi Aamori.
15Samuele adatsogolera Aisraele moyo wake wonse.
16Chaka ndi chaka ankapanga ulendo wozungulira, kupita ku Betele, Giligala ndi ku Mizipa, ndipo ankaweruza milandu ku malo onseŵa.
17Pambuyo pake ankabwerera ku Rama, poti ndiko kunali kwao. Kumenekonso ankaweruza Aisraele, ndipo adamangirako Chauta guwa.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.