Yer. 27 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Zakuti Ayuda adzakhala akapolo a mfumu ya ku Babiloni

1 2Maf. 24.18-20; 2Mbi. 36.11-13 Pamene Zedekiya, mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda adayamba kulamulira, Chauta adalankhula ndi Yeremiya namuuza kuti,

2“Tenga nsinga zachikopa ndi mitengo ya goli, uzimange m'khosi mwako.

3Tsono utumize uthenga kwa mafumu a ku Edomu, Mowabu, Amoni, Tiro ndi Sidoni, kudzera mwa amithenga amene abwera ku Yerusalemu kwa Zedekiya, mfumu ya ku Yuda.

4Uŵauze kuti akadziŵitse atsogoleri ao kuti Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akuuza atsogoleriwo kuti:

5Ndidalenga dziko lapansi ndi mphamvu zanga ndi nyonga zanga. Ndidalenga anthu ndi nyama pa dziko lapansi, ndipo ndimalipereka kwa amene ndimamuwona kuti ndi woyenera.

6Bar. 3.16, 17Tsopano ndapereka maiko onseŵa kwa Nebukadinezara mtumiki wanga, mfumu ya ku Babiloni. Ndampatsanso nyama zonse zakuthengo kuti zizimtumikira.

7Anthu a mitundu yonse adzamtumikira iyeyo, mwana wake ndi mdzukulu wake, mpaka itakwana nthaŵi yoti dziko lake liwonongedwe. Pamenepo anthu a mitundu yambiri ndi mafumu amphamvu adzagonjetsa ufumu wakewo.

8“Koma ngati anthu a mtundu wina uliwonse kapena a dziko lina lililonse adzakana kutumikira Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, kapena kugonjera ulamuliro wake, Ineyo ndidzaŵalanga ndi nkhondo, njala ndi mliri, mpaka nditaŵapereka m'manja mwake kotheratu,” akuterotu Chauta.

9“Nchifukwa chake musaŵamvere aneneri anu, oombeza anu, otanthauza maloto, amaula ndi amatsenga anu, akamakuuzani kuti musadzatumikire mfumu ya ku Babiloni.

10Ndithudi, amakuloserani zabodza, kotero kuti adani adzakuchotsani m'dziko lanu, kupita nanu kutali. Ndidzakupirikitsani ndipo mudzaonongeka.

11Koma mtundu wina uliwonse umene udzagonjera mfumu ya ku Babiloni ndi kumaitumikira, ndidzausiya kuti ukhale m'dziko lake, kuti uzilima ndi kumakhala kumeneko,” akuterotu Chauta.

12“Mau okhaokhawo ndidauzanso Zedekiya mfumu ya ku Yuda, ndidati: Mugonjere ulamuliro wa mfumu ya ku Babiloni ndi kumaitumikira iyoyo pamodzi ndi anthu ake. Mukatero mudzapulumutsa moyo wanu.

13Nanga iweyo ndi anthu ako, muferenji ndi nkhondo, njala ndi mliri, zimene Chauta waopsera mtundu wina uliwonse wosatumikira mfumu ya ku Babiloni?

14Musaŵamvere aneneri okuuzani kuti musadzatumikire mfumu ya ku Babiloni. Akukuloserani zabodza.

15Sindidaŵatume ndine, ngakhale iwowo akuti amalosa m'dzina langa. Motero ndidzakupirikitsani, ndipo mudzaonongeka inuyo pamodzi ndi aneneri amene amakuloseraniwo.

16“Pambuyo pake ndidauza ansembe pamodzi ndi anthu ena onse kuti Chauta akunena kuti: Musaŵamvere aneneri anu amene amakuuzani kuti, ‘Ziŵiya za ku Nyumba ya Chauta adzazibwezanso mwamsanga kuchokera ku Babiloni.’ Iwowo akungokuloserani zabodza.

17Musaŵamvere, muzitumikira mfumu ya ku Babiloni ndipo mupulumutse moyo wanu. Chifukwa chiyani mzindawu usanduke bwinja?

18Ngati iwo ndi aneneridi ndipo ngati ali ndi mau a Chauta, apemphere kwa Chauta Wamphamvuzonse kuti ziŵiya zimene zidatsala m'Nyumba ya Chauta ndiponso m'nyumba ya mfumu ku Yerusalemu zisatengedwe kupita ku Babiloni.

19Chauta Wamphamvuzonse ndiye akunena za mizati, chimbiya, maphaka ndi ziŵiya zonse zimene zidatsala mumzindamu.

20Zimenezi Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni sadazitenge pa nthaŵi imene ankatenga ukapolo Yehoyakini mwana wa Yehoyakimu mfumu ya ku Yuda, kuchoka naye ku Yerusalemu kupita naye ku Babiloni pamodzi ndi atsogoleri a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu.

21Zoonadi, ameneŵa ndiwo mau a Chauta Wamphamvuzonse onena za ziŵiya zimene zidatsala m'Nyumba ya Chauta, m'nyumba ya mfumu ya ku Yuda ndiponso mu Yerusalemu, akuti,

22‘Zidzatengedwa kupita ku Babiloni. Ndipo zidzakhala kumeneko mpaka tsiku limene ndidzazikumbukenso. Apo ndidzazitenganso ndi kudzazibwezanso ku malo ano,’ ” akuterotu Chauta.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help