1Tsiku lakhumi la mwezi wachisanu, chaka chachisanu ndi chiŵiri cha ukapolo, akuluakulu ena a ku Israele adabwera kudzapempha nzeru kwa Chauta. Tsono adakhala pansi pamaso panga.
2Pamenepo Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,
3“Iwe mwana wa munthu, akuluakulu a ku Israele uŵauze mau anga akuti, Kodi mwabwera kudzapempha nzeru kwa Ine? Pali Ine ndemwe, sindilola zotere. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.
4“Iwe mwana wa munthu, kodi ukuvomera kudzaŵaweruza? Kodi udzagamula mlandu wao? Tsonotu uŵafotokozere zonyansa zonse zimene adachita makolo ao.
5 kumene mukupitako nchotani? Choncho dzina lake lakhala ‘Chitunda chachipembedzo’ mpaka lero.”
30“Tsono uŵauze Aisraele kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, Kodi mudzadziipitsa monga momwe makolo anu adachitira ndi kusokera popembedza milungu yao yonyansa?
31Pamene mubwera ndi mphatso zanu, ndi kumapereka ana anu kuti akhale nsembe zopsereza, mumadziipitsa potumikira mafano anu ambirimbiri mpaka lero lino. Kodi Aisraele inu, ndingathe kukulolani bwanji kuti mulandire malangizo kwa Ine? Pali Ine ndemwe Chauta wamoyo, sindidzalola zoterezi.
32Inuyo mukufuna kukhala ngati anthu a mitundu ina, ngati anthu a m'maiko ena amene amapembedza mitengo ndi miyala. Koma zimenezo sizidzachitika konse.
Mulungu alanga Aisraele kenaka nkuŵakhululukira33“Ine Ambuye Chauta ndikuti, Pali Ine ndemwe wamoyo, ndidzakulamulani ndi dzanja langa lamphamvu, nditasamula mkono wanga ndili wokwiya kwambiri.
34Ndi dzanja langa lamphamvu ndi mkono wanga wosamula kuwonetsa mkwiyo, ndidzakuchotsani pakati pa mitundu ina ya anthu ndi kukusonkhanitsani kuchokera kumaiko kumene mudabalalikirako.
35Ndidzakuloŵetsani m'chipululu choyenera akunja. Kumeneko ndidzakuimbani mlandu choonana maso ndi maso.
36Ndidzakulangani monga momwe ndidalangira makolo anu ku chipululu cha ku Ejipito. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.
37“Ndidzakuŵerengani ndi ndodo ya mbusa, ndi kukuloŵetsani m'chigwirizano cha chipangano changa.
38Ndidzakuchotserani anthu amene amandipandukira ndi kundichimwira. Ndidzaŵatulutsa m'dziko limene akukhalamolo, koma sadzapondamo m'dziko la Israele. Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.
39“Koma inu Aisraele, zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Pitani nonsenu mukatumikire mafano anu! Koma ndithu ndikuti pambuyo pake mudzandimveranso, ndipo simudzaipitsanso dzina langa loyera popereka mphatso kwa mafano anu!
40Zoonadi Aisraele onse adzanditumikira m'dziko mwaomo ku phiri langa lalitali, phiri loyera la ku Israele. Kumeneko ndidzaŵalandira moŵakomera mtima. Kumeneko ndidzayembekeza kulandira mitulo yao ndi mphatso zao zopambana, pamodzi ndi zopereka zao zopatulika.
41Inu nomwe ndidzakulandirani ngati nsembe za fungo lokoma, nditakutulutsani pakati pa anthu a mitundu ina, ndi kukusonkhanitsani kuchokera kumaiko kumene mudabalalikira. Pamenepo ndidzaonetsa ungwiro wanga pakati pa inu, ndipo mitundu yonse ya anthu idzaona.
42Apo mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, ndikadzakubwezerani kwanu ku dziko la Israele, dziko limene ndidachita kulumbira kuti ndidzapatsa makolo anu.
43Kumeneko mudzakumbukira makhalidwe anu oipa ndi zonyansa zanu zonse zimene mudadziipitsa nazo. Ndipo mudzamva nyansi ndi inu nomwe chifukwa cha zonse zimene mudachita.
44Tsono inu a m'banja la Israele mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, pamene ndidzakuchitirani zabwino, osakumbukira makhalidwe anu oipa ndi ntchito zanu zopotoka, kuti choncho dzina langa lilemekezeke. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.”
Moto kumwera45Pambuyo pake Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,
46“Iwe mwana wa munthu, tembenuka uyang'ane kumwera, ndipo ulalikire modzudzula anthu akumwera. Uliimbe mlandu dziko lankhalango lakumwera ku Negebu.
47Uliwuze kuti, Chauta akuti mumvere mau ake, Iye akunena kuti, ‘Ndidzakuyatsa moto, ndipo motowo udzapsereza mitengo yako yonse youma ndi yaiŵisi yomwe. Malaŵi ake adzakhala osazimika, ndipo aliyense kuchokera kumwera mpaka kumpoto adzapsa nawo.
48Anthu onse adzadziŵa kuti Ine Chauta ndine amene ndauyatsa motowo, ndipo sudzazimidwadi.’ ”
49Tsono ndidati, “A! Inu Ambuye Chauta, anthu akundinena, akuti, ‘Suja amangonena nthano chabe ameneyu!’ ”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.