Yer. 10 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za mafano ndi za chipembedzo choona

1Inu Aisraele, imvani mau

amene Chauta akukuuzani,

2Chauta akuti,

“Musatsate makhalidwe a anthu a mitundu ina.

Musachite mantha ndi zizindikiro zozizwitsa

zamumlengalenga,

ngakhale anthu a mitundu ina

amachita nazo mantha zimenezi.

3Ndithudi, miyambo ya anthu a mitundu inayo

nzopanda pake.

Iwo aja amakadula mtengo ku nkhalango,

munthu waluso namausema ndi nsompho.

4Anthu ena amakongoletsa chosemacho

ndi siliva ndi golide,

kenaka nkuchikhomerera ndi misomali,

kuti chisagwedezeke.

5Mafano aowo ali ngati kangamunthu

woopsera mbalame m'munda wa minkhaka,

sangathe nkulankhula komwe.

Ayenera kuŵanyamula, poti sangayende okha.

Musaŵaope, chifukwa sangakuchiteni choipa.

Alibenso mphamvu zochitira zabwino.”

6Palibe wolingana nanu, Inu Chauta.

Inu ndinu aakulu,

dzina lanu lili ndi mphamvu yaikulu.

7 Chiv. 15.4 Ndani amene angaleke kukuwopani,

Inu mfumu ya mitundu ya anthu?

Paja kukuwopaniko nkokuyenerani.

Pakati pa anthu anzeru onse

ndiponso pakati pa maufumu onse a pansi pano

palibe wina wolingana nanu.

8Onsewo ndi opusa ndi opanda nzeru.

Nzeru zao amaphunzira ku mafano

achabechabe opanga ndi mitengo.

9Siliva wosula wokutira mafanowo

ndi wochokera ku Tarisisi,

ndipo golide wake ndi wochokera ku Ufazi.

Mafano aowo ndi ntchito ya anthu aluso

ndi anthu odziŵa kuzokota golide.

Amaveka mafanowo nsalu zonyezimira ndi zofiirira.

Zonsezo ndi ntchito ya anthu aluso chabe.

10Koma Chauta ndiye Mulungu woona,

Iyeyo ndiye Mulungu wamoyo ndiponso Mfumu yamuyaya.

Dziko lapansi limagwedezeka ndi ukali wa Chauta.

Anthu a mitundu ina sangathe kupirira ukali wakewo.

11Anthuwo mukaŵauze kuti, “Milungu imene sidalenge dziko lakumwamba ndi dziko lapansi, idzaonongeka ponseponse, pa dziko lapansi ndi pansi pa thambo.”

Nyimbo Yotamanda Mulungu

12Chauta ndiye amene adalenga dziko lapansi

ndi mphamvu zake.

Ndiye amene adapanga zonse ndi nzeru zake

ndipo ndi umisiri wake adayala thambo lakumwamba.

13Iye akalankhula, kumamveka mkokomo wa madzi kumwamba,

ndiye amene amadzetsa mitambo

kuchokera ku malekezero a dziko lapansi.

Amang'animitsa mphezi za mvula,

amakunthitsa mphepo kuchokera kumene amaisunga.

14Anthu onse ndi opusa, alibe nzeru.

Mmisiri aliyense wosula amachita manyazi ndi mafano ake.

Mafano amene amapangawo ngabodza

mwa iwo mulibe konse moyo.

15Mafanowo ngachabechabe, ayenera kuŵaseka,

ndipo pamene anthuwo adzalangidwe, mafanowo adzaonongeka.

16Koma Iye uja amene ali choloŵa cha Yakobe

sali ngati mafanowo,

Iye ndiyedi Mlengi wa zonse.

Aisraele ndi anthu ake amene Iye adaŵasankha,

dzina lake ndi Chauta Wamphamvuzonse.

Ulosi wonena za ukapolo

17Tolatolani katundu wanu, osamsiyanso pansi,

inu amene adani akuzingani ndi zithando zankhondo.

18Chauta akunena kuti,

“Tsopano ndichotsa anthu onse a m'dziko lino.

Ndidzaŵagwetsa m'mavuto,

mpaka aŵamve ndithu.”

19Ali apa amvekere, “Kalanga ine

chifukwa cha kupweteka koopsa!

Bala langa ndi lomvetsa chisoni.

Kale ndinkati chimenechi ndi chilango changa,

ndingochipirira basi.”

20Hema langa laonongeka,

zingwe zake zonse zaduka.

Ana anga andisiya ndipo kulibenso.

Palibenso wina woti nkundikhomera hema,

kapena woti nkufunyulula nsalu zake.

21Paja abusa ndi opusa,

sapempha nzeru kwa Chauta.

Nchifukwa chake zinthu sizidaŵayendere bwino,

ndipo nkhosa zao zidabalalika.

22Tamvani, kukubwera mphekesera.

Kumpoto kukuchokera chinamtindi chosokosa

chodzasakaza mizinda ya Yuda,

kuti isanduke bwinja,

mokhala nkhandwe basi.

23Inu Chauta, ndikudziŵa kuti

moyo umene ali nawo munthu si wake.

Munthu sangathe kudzitsogolera yekha.

24Langizeni, Inu Chauta, koma mwachilungamo.

Musandikwiyire kuti mungandiwononge.

25Ukali wanu uyakire mitundu imene sikudziŵani,

ndiye kuti anthu amene satama dzina lanu mopemba.

Iwo adasakaza anthu anu

ndi kuŵaononga kotheratu

ndipo dziko lao adalisandutsa bwinja.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help