1Mwana wanga, mvera mau anga,
malamulo anga akhale chuma chako.
2Utsate malamulo anga, ndipo udzakhala ndi moyo.
Usamale malangizo anga monga umachitira ndi maso ako.
3Achite ngati waŵamangirira ku chala,
ngati waŵadinda mumtima mwako.
4Nzeru uiwuze kuti,
“Iwe ndiwe mlongo wanga,”
ndipo khalidwe la kumvetsa zinthu ulitchule kuti,
“Bwenzi langa lapamtima.”
5Zikuteteze kwa mkazi wadama,
ku mau oshashalika a mkazi wosakhala wako.
6Tsiku lina pa windo la nyumba yanga,
ndidasuzumira pa made,
7ndipo pakati pa anthu opusa, pakati pa achinyamata,
ndidaona wachinyamata mmodzi wopanda nzeru.
8Ankayenda m'njira pafupi ndi nyumba ya mkaziyo,
ankaphera mu mseu wa kunyumba kumeneko.
9Inali nthaŵi ya chisisira, madzulo,
nthaŵi yausiku, kuli mdima.
10Ndiye mkazi adadzakumana naye,
atavala ngati mkazi wadama, wa mtima wonyenga.
11Mkaziyo ndi wosakhazikika ndi wopanda manyazi,
kamwendom'njira wosakhala pakhomo.
12Mwina umpeza pa mseu, mwina pa msika,
amachita kukhalizira munthu pa mphambano iliyonse.
13Tsono amamgwira mnyamata uja, nkumumpsompsona,
amalankhula naye ndi nkhope yopanda manyazi kunena kuti,
14“Ndinayenera kupereka nsembe,
ndipo lero ndachita zimene ndidazilumbirira.
15Motero tsopano ndabwera kuti ndidzakumane nawe,
ndinkakufunafuna, tsono ndakupeza.
16Pabedi panga ndayalapo zofunda zabwino,
pali nsalu zabafuta zamaŵangamaŵanga za ku Ejipito.
17Pomweponso ndawazapo zonunkhira za mure,
ndi mankhwala a fungo lokoma a aloyi, ndi a sinamoni.
18Bwera tsono, tikhale malo amodzi mpaka m'maŵa,
tisangalatsane ndi chikondi.
19Mwamuna wanga kulibe,
ali pa ulendo wautali.
20Adatenga thumba la ndalama,
adzabwerako mwezi utakhwima.”
21Amamkopa mnyamatayo ndi mau onyengerera,
amamkakamiza ndi mau ake oshashalika.
22Pamenepo mnyamatayo amatsatira mkaziyo
monga momwe ng'ombe imapitira kokaphedwa,
kapena monga momwe mbaŵala imakodwera mu msampha,
23mpaka muvi kuilasa m'mimba mwake.
Amakhala ngati mbalame yothamangira m'khwekhwe,
osadziŵako kuti aferapo.
24Ndiye tsopano ana inu, mundimvere ine,
mutchere khutu pa zimene ndinene ine.
25Musatengeke mtima ndi njira za mkazi ameneyo,
musasokere potsata njira zakezo.
26Paja iye uja adagwetsa amuna ambiri,
anthu amene adaŵaphetsa ngosaŵerengeka.
27Nyumba yake ndi njira yakumanda,
yotsikira ku dziko la anthu akufa.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.