Tob. 2 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Tobiti achita khungu

1 Eks. 23.16 Tsono Asaradoni ataloŵa ufumu, ine ndidabwerera kunyumba kwanga, ndipo adandibwezera Hana mkazi wanga ndi Tobiyasi mwana wanga. Pa chikondwerero cha Pentekoste, chotchedwanso chikondwerero cha masabata, adandikonzera phwando lalikulu, ine nkukonzekera kuti ndidye.

2Adayala tebulo naikapo zakudya zambiri. Pamenepo ndidauza mwana wanga Tobiyasi kuti, “Pita, ndipo mwa akapolo a mtundu wathu ukakapeza wina wosauka, wokhulupirira Mulungu, ukabwere naye kuti adzadye nafe. Ndidzadikira mpaka iwe mwana wanga utabwerako.”

3Tobiyasi adapita kukafunafuna munthu wosauka mwa abale athu. Koma adabwerera nati, “Atate!” Ine ndidati, “Tanena, mwana wanga.” Iye adati, “Mmodzi wa mtundu wathu amupha, achita kumpotola khosi, ndipo amtaya pa bwalo lapamsika, tikukamba pano akali komweko.”

4Ndidanyamuka nthaŵi yomweyo, chakudya osachikhudza nkomwe. Ndidakamtenga m'bwalomo munthuyo ndi kumkhazika m'chipinda china, kuti nthaŵi yamadzulo ndimuike m'manda.

5Num. 19.11-13Nditabwerako, ndidasamba, kenaka ndidadya chakudya changa, koma ndi mtima wachisoni.

6Amo. 8.10Pamenepo ndidakumbukira mau amene mneneri Amosi adaaŵanenera anthu a ku Betele, akuti,

“Zikondwerero zanu zidzasanduka maliro,

nyimbo zanu zonse zidzasanduka madandaulo.”

Choncho ndidaliradi misozi.

7Dzuŵa litaloŵa, ndidapita kukakumba manda, nkuikamo mtembo wa munthu uja.

8Anzanga adayamba kundiseka, adati, “Tamuwonani! Watha mantha tsopano. Kale adaafuna kumupha chifukwa cha zomwezi, mwai nkuti adaathaŵa. Koma tsopano wayambanso kuika anthu akufa.”

9Usiku womwewo ndidasamba kuti ndidziyeretse, kenaka ndidapita ku bwalo, nkugona pafupi ndi khoma. Sindidafunde kumaso chifukwa cha kutentha.

10Sindinkadziŵa kuti pa khoma pomwepo, pamwamba pa mutu wanga, panali timba. Ndiye zitosi zake zotentha zidandigwa m'masomu, nkuchita timatuza toyera. Ndidanka kwa asing'anga aŵa ndi aŵa, kuti mwina nkundichiza. Adayesa kuthiramo mankhwala osiyanasiyana m'masomu, koma timatuzato tinkapitirapitira. Potsiriza pake ndidasandukiratu wakhungu. Ndidakhala wosapenya pa zaka zinai. Abale anga onse adandimvera chisoni, ndipo Ahikare adandisamalira pa zaka ziŵiri, asanapite ku Elimaisi.

11Pa nthaŵi imeneyo mkazi wanga Hana ankagwira ntchito ya azimai, yoomba nsalu kuti apeze malipiro.

12Ankati akaomba, ankazipereka kwa amene ankaziitanitsa ndipo iwo ankamulipira. Tsiku la chisanu ndi chiŵiri la mwezi wa Disitoro, atatha kuwomba nsalu ina, adaipereka kwa eniake. Iwo adampatsa malipiro ake, naonjezerapo mwanawambuzi ngati mphatso.

13Atabwera naye kunyumba kwanga, mwanawambuziyo adayamba kulira. Ndidaitana mkazi wanga, nkumfunsa kuti, “Kodi mwanawambuziyu wachokera kuti? Ngatitu ndi wakuba, kamubwezere kwa eniake, chifukwa ife sitiyenera kudya zinthu zakuba.”

14Adandiyankha kuti, “Ai, achita kundipatsa ngati mphatso kuwonjezera pa malipiro anga.” Koma ine sindidamkhulupirire, motero ndidamuuza kuti akabwezere kwa eniake. Ndipo ndidachita manyazi chifukwa cha zimene mkaziyo adachita. Koma iye adandifunsa kuti, “Kodi ndalama zanu zothandizira ena zili kuti? Ntchito zanu zabwino zili kuti? Aliyense tsopano akudziŵa bwino za inu.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help