Eks. 39 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Apanga zovala za ansembe(Eks. 28.1-14)

1Tsono adapanga zovala zokongola kwambiri za ansembe, zovala potumikira m'malo oyera. Adapanga zovalazo ndi nsalu yobiriŵira, yofiirira ndi yofiira. Adapanga zovala za Aroni monga momwe Chauta adalamulira Mose.

Za chovala cha efodi

2Adapanga chovala chopatulika cha efodi ndi nsalu yagolide ndiponso ndi nsalu yobiriŵira, yofiirira ndi yofiira, ndi ya bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino.

3Ndipo adasula golide mwaphanthiphanthi, namlenzalenza, kuti amlukire kumodzi ndi thonje lobiriŵira, lofiirira ndi lofiira, ndiponso la bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino, ntchito yaumisiri.

4Tsono adapanga tizikwewo tam'mapewa ta chovala cha efodi chija, tolumikizika ku chovalacho pa mbali zake ziŵiri.

5Panalinso lamba woluka mwaluso, womangira efodi, wolukira kumodzi ndi efodiyo. Lambayo nayenso anali wa nsalu yagolide, ndi wa nsalu yobiriŵira, yofiirira ndi yofiira, ndiponso wa bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino, monga momwe Chauta adalamulira Mose.

6Kenaka adakonza miyala yakongola ya mtundu wa onikisi, naikhazika m'zoikamo zake zagolide. Tsono adaizokota monga amachitira pa chidindo, nalembapo mozokota bwino maina onse a ana aamuna a Israele.

7Yonseyo adaiika pa tizikwewo tam'mapewa ta chovala cha efodi chija, kuti iziŵakumbutsa ana a Israele, monga momwe Chauta adalamulira Mose.

8Pambuyo pake adapanga chovala chapachifuwa mwaluso kwambiri, monga chovala cha efodi chija. Adachipanga ndi nsalu yagolide, ndi nsalu yobiriŵira, yofiirira, ndi yofiira, ndiponso ya bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino.

9Kutalika kwake kwa chovala chapachifuwacho kunali masentimita 23, muufupi mwakenso masentimita 23, ndipo chinali chopinda paŵiri.

10Tsono adaikapo mizere inai ya miyala yokongola. Pa mzere woyamba adaika miyala ya rubi, topazi ndi garaneti.

11Pa mzere wachiŵiri adaika miyala ya emeradi, safiro ndi daimondi.

12Pa mzere wachitatu adaika miyala ya opela, agate ndi ametisiti,

13ndipo pa mzere wachinai adaika miyala ya berili, onikisi ndi yasipara. Miyalayo adaiika m'zoikamo zagolide.

14Panali miyala khumi ndi iŵiri imene adalembapo maina a mafuko a Israele. Inali miyala khumi ndi iŵiri yozokotedwa ngati zidindo, ndipo mwala uliwonse unali ndi dzina la fuko limodzi.

15Adapanga timaunyolo ta chovala chapachifuwa ta golide wabwino kwambiri, topota mwaluso ngati maukufu.

16Adapanganso zoikamo zake ziŵiri zagolide zonga maluŵa, ndiponso mphete ziŵiri, ndipo adalumikiza mphete ziŵirizo ku nsonga zake zapamwamba za chovala chapachifuwacho.

17Tsono zingwe ziŵiri zagolide adazilumikiza ku mphete ziŵiri zija,

18ndi kulumikiza nsonga ziŵiri zina za zingwezo m'zoikamo zake ziŵiri zija. Motero adazilumikiza patsogolo pa tizikwewo tam'mapewa ta chovala cha efodi chija.

19Adapanga mphete ziŵiri zagolide, nazilumikiza ku nsonga ziŵiri za chovala chapachifuwa cham'mphepete, m'kati mwake, pafupi ndi chovala cha efodi chija.

20Adapanganso mphete ziŵiri zagolide, nazilumikiza ku mbali yam'munsi, kutsogolo kwa tizikwewo tam'mapewa ta chovala cha efodi chija, pafupi ndi msoko, ndiponso pamwamba pa lamba woluka mwaluso uja wa efodiyo.

21Ndipo adalumikiza mphete za chovala chapachifuwa zija ku mphete za efodi. Adalumikiza ndi kamkuzi kobiriŵira, kuti chovala chapachifuwacho chikhale pamwamba pa lamba woluka mwaluso uja, ndipo chisalekane ndi efodi ija, monga momwe Chauta adalamulira Mose.

22Adapanga mkanjo wake wa efodi, woombedwa ndi nsalu yobiriŵira.

23Mkanjowo unali ndi popisa mutu, ndipo maonekedwe ake anali ngati popisa mutu pa malaya. M'mbali mwake kuzungulira, munali mosokerera bwino, kuti ungang'ambike.

24Pa mpendero wake wapansi, adalumikizapo zithunzi za makangaza zopangidwa ndi nsalu yobiriŵira, yofiirira ndi yofiira, ndiponso ya bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino.

25Adapanganso timabelu ta golide wabwino kwambiri, mopakiza pakati pa makangazawo, kuzungulira mpendero wonse wam'munsiwo.

26Tsono panali khangaza limodzi ndi kabelu kamodzi, khangaza limodzi ndi kabelu kamodzi, kuzungulira mpendero wonse wa mkanjo, umene ansembe ankavala pogwira ntchito zaunsembe, monga momwe Chauta adalamulira Mose.

27Tsono Aroni ndi ana ake, amisiri aja adaŵapangira miinjiro,

28nduŵira, makofiya ndi akabudula, zonsezo zopangidwa ndi nsalu ya bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino.

29Adapanganso lamba wa bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino ndi wa thonje lobiriŵira, lofiira ndi lofiirira, ndipo adamkongoletsa ndi zopetapeta, monga momwe Chauta adalamulira Mose.

30Ndipo adapanga duŵa la golide wabwino kwambiri. Limenelo linali chizindikiro chopatulika, ndipo mofanizira ndi mazokotedwe a chidindo, adazokotapo mau akuti, “Chopereka kwa Chauta.”

31Kenaka adatenga kamkuzi kobiriŵira namangirira duŵa limenelo ku nsalu ya nduŵira ija, monga momwe Chauta adalamulira Mose.

Kutha kwake kwa ntchitoyo(Eks. 35.10-19)

32Tsono ntchito yonse yomanga chihema chamsonkhano idatha. Aisraele aja adachitadi zonse, monga momwe Chauta adalamulira Mose.

33Pambuyo pake zonsezo adabwera nazo kwa Mose: chihema chija chodzakhala Nyumba ya Mulungu, pamodzi ndi zipangizo zake zonse, ngoŵe zake zokoŵera, mafulemu ake, mitanda yake, nsanamira zake ndi masinde ake omwe.

34Adabweranso ndi chophimbira cha chikopa chankhosa chonyika mu utoto wofiira, chophimbira cha chikopa chambuzi, nsalu zochingira,

35bokosi loikamo miyala yaumboni pamodzi ndi nsanamira zake, ndiponso chivundikiro cha bokosilo.

36Adabweranso ndi tebulo, pamodzi ndi zipangizo zake, ndipo adaika buledi woperekedwa kosalekeza kwa Mulungu;

37choikaponyale cha golide wabwino kwambiri, nyale zake pamodzi ndi zipangizo zake, mafuta anyale;

38guwa lagolide, mafuta odzozera, lubani wa fungo lokoma, nsalu yotsekera pa chipata choloŵera m'chihema,

39guwa lamkuŵa, pamodzi ndi chitsulo cha sefa, mphiko zake, pamodzi ndi zipangizo zake zonse, ndiponso beseni losambira ndi phaka lake.

40Adabweranso ndi nsalu zochingira bwalo pamodzi ndi nsanamira zake ndi masinde ake, nsalu yochingira pa chipata choloŵera m'bwalolo, pamodzi ndi zingwe zake ndi zikhomo zake, ndiponso zipangizo zonse zotumikira nazo m'chihema cha Chauta chija.

41Adabweranso ndi zovala zokongola kwambiri zoyenera kuvala ansembe potumikira m'malo oyera, zovala zopatulika za wansembe Aroni, ndiponso zovala za ana ake aamuna, zoyenera kuzivala pogwira ntchito zaunsembe.

42Motero Aisraele adachitadi ntchito zonse, monga momwe Chauta adalamulira Mose.

43Tsono Mose adaona zonse zimene zidapangidwazo, ndipo adatsimikiza kuti adazipangadi monga momwe Chauta adalamulira. Pamenepo Mose adaŵadalitsa anthu onsewo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help