Num. 33 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Ulendo wa ku Mowabu kuchokera ku Ejipito

1Pamene Aisraele adatuluka m'dziko la Ejipito m'magulu a mafuko ao, Mose ndi Aroni akuŵatsogolera,

2Mose adalemba maina a malo onse oyambira ulendo ndi chigono chilichonse, monga Chauta adamlamula. Zigono zake potsata malo oyambira ulendo wao zinali motere:

3Adanyamuka ku Ramsesi pa mwezi woyamba, pa tsiku la 15 la mweziwo. M'maŵa mwake, litapita tsiku la Paska, Aisraele adatuluka m'dziko la Ejipito mokondwa, anthu onse a ku Ejipito akupenya.

4M'menemo nkuti Aejipitowo akuika maliro a ana ao achisamba amene Chauta adaaŵapha pakati pao. Choncho Chauta adalipsira milungu ya Aejipito.

5Pambuyo pake Aisraele adanyamuka ku Ramsesi nakamanga mahema ku Sukoti.

6Adanyamuka ku Sukoti nakamanga mahema ku Etamu, mzinda umene uli m'mbali mwa chipululu.

7Adanyamuka ku Etamu, nabwerera ku Pihahiroti, mzinda umene uli kuvuma kwa Baala-Zefoni. Ndipo adamanga mahema patsogolo pa Migidoli.

8Adanyamuka ku Pihahiroti naoloka pakatimpakati pa nyanja, ndipo adaloŵa m'chipululu. Tsono adayenda ulendo wa masiku atatu m'chipululu cha Etamu, nakamanga mahema ku Mara.

9Adanyamuka ku Mara nakafika ku Elimu. Ku Elimuko kunali akasupe khumi ndi aŵiri ndi mitengo ya migwalangwa makumi asanu ndi aŵiri, ndipo adamanga mahema ao kumeneko.

10Adanyamuka ku Elimu, nakamanga mahema ao m'mbali mwa Nyanja Yofiira.

11Adanyamuka ku Nyanja Yofiira, nakamanga mahema ao ku chipululu cha Sini.

12Adanyamuka ku chipululu cha Sini, nakamanga mahema ao ku Dofika.

13Adanyamuka ku Dofika, nakamanga mahema ao ku Alusi.

14Adanyamuka ku Alusi, nakamanga mahema ao ku Refidimu kumene kunalibe madzi akumwa.

15Adanyamuka ku Refidimu, nakamanga mahema ao ku chipululu cha Sinai.

16Adanyamuka ku chipululu cha Sinai, nakamanga mahema ao ku Kibroti-Hatava.

17Adanyamuka ku Kibroti-Hatava, nakamanga mahema ao ku Haseroti.

18Adanyamuka ku Hazeroti, nakamanga mahema ao ku Ritima.

19Adanyamuka ku Ritima, nakamanga mahema ao ku Rimoni-Perezi.

20Adanyamuka ku Rimoni-Perezi, nakamanga mahema ao ku Libina.

21Adanyamuka ku Libina, nakamanga mahema ao ku Risa.

22Adanyamuka ku Risa, nakamanga mahema ao ku Kehelata.

23Adanyamuka ku Kehelata, nakamanga mahema ao ku phiri la Sefera.

24Adanyamuka ku phiri la Sefera, nakamanga mahema ao ku Harada.

25Adanyamuka ku Harada, nakamanga mahema ao ku Makeloti.

26Adanyamuka ku Makeloti, nakamanga mahema ao ku Tahati.

27Adanyamuka ku Tahati, nakamanga mahema ao ku Tera.

28Adanyamuka ku Tera, nakamanga mahema ao ku Mitika.

29Adanyamuka ku Mitika, nakamanga mahema ao ku Hasimona.

30Adanyamuka ku Hasimona, nakamanga mahema ao ku Meseroti.

31Adanyamuka ku Meseroti, nakamanga mahema ao ku Beneyakana.

32Adanyamuka ku Beneyakana, nakamanga mahema ao ku Horo-Hagidigadi.

33Adanyamuka ku Horo-Hagidigadi, nakamanga mahema ao ku Yotibata.

34Adanyamuka ku Yotibata, nakamanga mahema ao ku Aborona.

35Adanyamuka ku Aborona, nakamanga mahema ao ku Eziyoni-Gebere.

36Adanyamuka ku Eziyoni-Gebere, nakamanga mahema ao m'chipululu cha Zini (ndiye kuti Kadesi).

37Adanyamuka ku Kadesi, nakamanga mahema ao ku phiri la Hori m'mbali mwa dziko la Edomu.

38 Num. 20.22-28; Deut. 10.6; 32.50 Chauta atamlamula, wansembe Aroni adakwera phiri la Hori nakafera komweko, chaka cha 40 Aisraele atatuluka m'dziko la Ejipito, pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu.

39Aroniyo anali wa zaka 123 za kubadwa, pamene adamwalira pa phiri la Hori.

40 Num. 21.1 Mfumu ya ku Aradi, Mkanani amene ankakhala m'dziko la Kanani, adamva kuti Aisraele akubwera.

41Pambuyo pake iwo adanyamuka ku phiri la Hori, nakamanga mahema ao ku Zalimona.

42Adanyamuka ku Zalimona, nakamanga mahema ao ku Punoni.

43Adanyamuka ku Punoni, nakamanga mahema ao ku Oboti.

44Adanyamuka ku Oboti, nakamanga mahema ao ku Iyeabarimu, m'dziko la Mowabu.

45Adanyamuka ku Iyimu, nakamanga mahema ao ku Dibonigadi.

46Adanyamuka ku Dibonigadi, nakamanga mahema ao ku Alimoni-dibulataimu.

47Adanyamuka ku Alimoni-dibulataimu, nakamanga mahema ao ku mapiri a Abarimu patsogolo pa Nebo.

48Adanyamuka ku mapiri a Abarimu, nakamanga mahema ao ku zigwa za ku Mowabu, pafupi ndi mtsinje wa Yordani ku Yeriko.

49Adamanga mahema ao pafupi ndi mtsinje wa Yordani kuyambira ku Beteyesimoti mpaka ku Abele-Sitimu, m'zigwa za Mowabu.

Aisraele apirikitsa nzika za dziko la Kanani

50Chauta adauza Mose m'zigwa za Mowabu pafupi ndi mtsinje wa Yordani, kuti,

51“Uza Aisraele kuti, Pamene muwoloka mtsinje wa Yordani kuti muloŵe m'dziko la Kanani,

52mudzapirikitse nzika zonse za m'dzikomo pamene mukufika, ndipo mudzaononge miyala yao yozokota ndi kuwononganso mafano ao osungunula. Mudzasakaze akachisi ao onse ku mapiri.

53Mudzalande dzikolo kuti likhale lanu, ndipo mudzakhale m'menemo, poti ndakupatsani kuti likhale lanu.

54Num. 26.54-56 Mudzalandira dzikolo kuti likhale choloŵa chanu mwamaere, potsata mabanja anu. Fuko lalikulu lilandire choloŵa chachikulu, ndipo fuko laling'ono lilandire choloŵa chaching'ono. Dziko lililonse limene maere agwere munthu, likhale lake la munthuyo. Mudzalandire choloŵa chanu potsata mafuko a makolo anu.

55Koma mukapanda kupirikitsa nzika zam'dzikomo pamene mukufika, amene mwaŵalola kuti atsalirewo adzakhala ngati zisonga zokubayani m'maso, ndiponso ngati minga m'mbali mwanu, ndipo adzakuvutani m'dziko m'mene mukakhalemo.

56Tsono ndidzakuchitani inuyo zimene ndinkaganiza kuti ndiŵachite iwowo.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help