1“Munthu akaitanidwa ku bwalo la milandu, namlumbiritsa kuti achite umboni wa zinthu zimene adaziwona kapena adazidziŵa, iyeyo nakana kupereka umboniwo, munthu ameneyo ndi woyenera kumlanga.
2Munthu akakhudza chinthu chilichonse chonyansa pa zachipembedzo, monga nyama yakufa yam'thengo kapena yoŵeta, kapenanso zokwaŵa zakufa, ndipo pokhudzapo adziipitsa mosadziŵa, munthu ameneyo ndi woipitsidwa, ndiponso ndi wopalamula.
3Wina aliyense akakhudza zonyansa za munthu za mtundu uliwonse, ndipo pokhudzapo adziipitsa mosadziŵa, munthu ameneyo akhala wopalamula, akangozindikira pambuyo pake zimene wachita.
4Munthu akalakwa polumbira mofulumira kuti adzachita chinthu choipa kapena chabwino, kulumbira kwake kwa mtundu uliwonse kumene anthu amachita, ndipo polumbirapo sadziŵa vuto lake, munthu ameneyo akhala wopalamula, akangozindikira pambuyo pake zimene wachita.
5Munthu akapalamula pa chilichonse mwa zimene tatchulazi, aulule tchimo lakelo.
6Kenaka abwere kudzapereka nsembe kwa Chauta, chifukwa cha tchimo lakelo. Nsembe yake ikhale ya nkhosa yaikazi kapena ya mbuzi yaikazi. Tsono wansembe achite mwambo wopepesera machimo a wopalamula uja.
7“Koma ngati munthu alibe nkhosa kapena mbuzi, atenge njiŵa ziŵiri kapena nkhunda ziŵiri, kuti zikhale nsembe yopereka kwa Chauta yopepesera machimo ake. Imodzi ikhale nsembe yopepesera machimo, ndipo inayo ikhale nsembe yopsereza.
8Abwere nazo kwa wansembe, ndipo wansembeyo ayambe wapereka mbalame yopepesera machimoyo. Aipotole khosi, koma asaidule mutu,
9ndipo awazeko magazi a mbalameyo m'mbali mwa guwa. Koma magazi ena otsala aŵathire pansi, kuti ayenderere patsinde pa guwalo. Imeneyo ndiyo nsembe yopepesera machimo.
10Ndipo apereke mbalame inayo kuti ikhale nsembe yopsereza, potsata mwambo wake. Wansembe atachita mwambo wopepesera machimo amene munthuyo wachita, wochimwayo adzakhululukidwa.
11“Ngati munthu alibe njiŵa ziŵiri kapena nkhunda ziŵiri, abwere ndi ufa wosalala wokwanira muyeso wa kilogaramu limodzi, kuti ukhale nsembe yopepesera tchimo limene wachita. Asathireko mafuta kapenanso lubani, chifukwa imeneyi ndi nsembe yopepesera machimo.
12Tsono abwere ndi ufa kwa wansembe, ndipo wansembeyo atapeko wa dzanja limodzi ngati chikumbutso ndi kuutenthera pa guwa, pamodzi ndi nsembe zopereka kwa Chauta. Imeneyi ndiyo nsembe yopepesera machimo.
13Umu ndimo m'mene wansembe adzachitire mwambo wopepesera munthu amene adachimwa, ndipo munthuyo adzakhululukidwa. Tsono zotsala zikhale za wansembeyo, monga momwe amachitira ndi chopereka cha chakudya.”
Nsembe zopepesera kupalamula14Chauta adauza Mose kuti,
15“Munthu akachita zinthu mosakhulupirika, nachimwa posapereka kwa Chauta zinthu zopatulika zofunika, koma mosadziŵa, apereke kwa Chauta nsembe yopepesera kupalamula chifukwa cha tchimo lakelo. Nsembe yake ikhale nkhosa yamphongo yopanda chilema, ndipo mtengo wake wa nkhosayo udzakhale wokwana masekeli asiliva, potsata kaŵerengedwe ka ku Nyumba ya Mulungu. Imeneyo ndiyo nsembe yopepesera kupalamula.
16Tsono munthuyo abweze zopatulika zimene sadaperekezo, ndipo aonjezepo chimodzi mwa zigawo zisanu zilizonse, ndipo azipereka kwa wansembe. Apo wansembeyo adzachita mwambo wopepesera machimo a munthuyo, popereka nsembe yopepesera kupalamula ya nkhosa yamphongo ija, ndipo munthuyo adzakhululukidwa.
17“Munthu akachimwa pochita mosadziŵa zimene Chauta amaletsa, ndi wopalamulabe ndithu ameneyo, ndipo ndi woyenera kumlanga.
18Abwere kwa wansembe ndi nkhosa yamphongo yopanda chilema, imene mtengo wake ulingane ndi wa nyama ya nsembe yopepesera kupalamula. Wansembeyo achite mwambo wopepesera machimo amene munthuyo adachita mosadziŵawo, ndipo wochimwayo adzakhululukidwa.
19Imeneyo ndiyo nsembe yopepesera kupalamula, chifukwa munthuyo ndi wopalamula pamaso pa Chauta.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.