Num. 32 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mafuko a kuvuma kwa Yordani(Deut. 3.12-22)

1Ana a Rubeni ndi ana a Gadi anali ndi ng'ombe zambiri. Adaona dziko la Yazere ndi dziko la Giliyadi kuti linali ndi malo oyenera kuŵeterako ng'ombe.

2Choncho ana a Gadi ndi ana a Rubeni aja adabwera kwa Mose, kwa wansembe Eleazara ndi kwa atsogoleri a mpingo, naŵauza kuti,

3“Midzi ya Ataroti, Diboni, Yazere, Nimira, Hesiboni, Eleyale, Sibima, Nebo ndi Beoni,

4dziko limene Chauta adagonjetsera Aisraele, ndi dziko loyenera kuŵeterako ng'ombe, ndipo atumiki anufe tili ndi ng'ombe.

5Ngati mwatikomera mtima, mutipatse dzikoli atumiki anufe, kuti likhale lathu. Musatipititse patsidya pa Yordani.”

6Koma Mose adafunsa ana a Gadi ndi ana a Rubeni kuti, “Kodi abale anu azikamenya nkhondo, inu mutangokhala kuno?

7Chifukwa chiyani mufuna kuŵatayitsa mtima Aisraele, kuti asakaloŵe m'dziko limene Chauta adaŵapatsa?

8Num. 13.17-33 Makolo anu adachita zotero, pamene ndidaŵatuma kuchokera ku Kadesi-Baranea, kuti akaone dziko.

9Iwo atapita ku chigwa cha Esikolo, nakaona dzikolo, adatayitsa mtima Aisraele, pakuŵauza kuti asakaloŵe m'dziko limene Chauta adaŵapatsa.

10Num. 14.26-35 Tsono pa tsiku limenelo Chauta adapsa mtima, ndipo adalumbira kuti,

11‘Ndithudi palibe ndi mmodzi yemwe mwa anthu otuluka m'dziko la Ejipito, kuyambira wa zaka makumi aŵiri ndi wopitirirapo, amene adzaone dziko limene ndidalonjeza kuti ndidzapatsa Abrahamu, Isaki ndi Yakobe, chifukwa sadanditsate kwathunthu.

12Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaone dzikolo, kupatula Kalebe yekha mwana wa Yefune, Mkenizi uja, ndi Yoswa mwana wa Nuni, chifukwa iwoŵa ndiwo adatsata Chauta kwathunthu.’

13Chauta adaŵapsera mtima Aisraele, ndipo adaŵayendetsa m'chipululu muja zaka makumi anai, mpaka udatha mbadwo wonse umene udachimwira Chauta.

14Tsopano inu mwaloŵa m'malo mwa makolo anu, inu mbadwo watsopano wa anthu ochimwa, ndipo mukufuna kuti muwonjezere mkwiyo woopsa wa Chauta pa Aisraele.

15Pakuti ngati muleka kumtsata, Iye adzasiyanso anthu m'chipululu, ndipo inu mudzaonongetsa anthu onseŵa.”

16Tsono iwo adasendera kwa Mose namuuza kuti, “Poyamba mutilole kuti timange kuno makola a nkhosa zathu, ndi mizinda yoti ana athu azikhalamo.

17Pambuyo pake tidzatenga zida zankhondo ndi kutsogolera Aisraele mpaka titakaŵafikitsa ku malo ao. Koma ana athu adzakhala m'mizinda yamalinga, chifukwa choopa anthu a m'dziko muno.

18Sitidzabwerera kwathu mpaka Mwisraele aliyense atalandira choloŵa chake.

19Ife ndiye sitidzalandira nao choloŵa chathu patsidya pa Yordanipo kapena patsogolo pake, chifukwa choti talandira choloŵa chathu tsidya lino la Yordani, kuvuma kuno.”

20Choncho Mose adauza anthuwo kuti, “Muchite izi: mutenge zida pamaso pa Chauta ndi kupita ku nkhondo.

21Aliyense mwa inu atenge zida, ndipo aoloke mtsinje wa Yordani pamaso pa Chauta ndi kupirikitsa adani ake patsogolo pake,

22mpaka kugonjetsa dzikolo pamaso pa Chauta. Mukatero, pambuyo pake mudzabwerera kuno, chifukwa mudzakhala mutagwirira ntchito Chauta ndi Aisraele. Pamenepo dziko lino lidzakhala lanu pamaso pa Chauta.

23Koma ngati simuchita choncho, mwachimwira Chauta, ndipo dziŵani kuti tchimo lanu lidzakutsatani.

24Mangani mizinda ya ana anu, ndi makola a nkhosa zanu, koma muchitedi zimene mwalonjeza.”

25Tsono ana a Gadi ndi ana a Rubeni adayankha Mose kuti, “Atumiki anu adzachitadi monga momwe inu mbuyathu mwalamulira.

26Ana athu ndi akazi athu atsala ku mizinda ya Giliyadi, pamodzi ndi nkhosa zathu ndi ng'ombe zathu zomwe.

27Koma atumiki anufe, tiwoloka aliyense atatenga zida, kukamenya nkhondo pamaso pa Chauta, monga momwe inu mbuyathu mwalamulira.”

28 Yos. 1.12-15 Choncho Mose adalamula wansembe Eleazara, Yoswa mwana wa Nuni, ndi atsogoleri a mabanja a mafuko a Aisraele kuti,

29“Ngati ana a Gadi ndi a Rubeni onse amene angathe kutenga zida kuti akamenye nkhondo pamaso pa Chauta. Adzaoloka nanu mtsinje wa Yordani, nadzagonjetsa dziko lili patsogolo panulo, mudzaŵapatse dziko la Giliyadi kuti likhale lao.

30Koma akapanda kuwoloka nanu, atatenga zida zankhondo, adzalandira chuma chao pakati panu m'dziko la Kanani.”

31Ndipo zidzukulu za Gadi ndi za Rubeni zidayankha kuti, “Ife atumiki anu tidzachita zomwe Chauta watiwuza.

32Tidzaoloka titatenga zida zankhondo pamaso pa Chauta, ndi kuloŵa m'dziko la Kanani, koma chuma cha choloŵa chathu chidzatsala ndi ife konkuno ku tsidya lino la Yordani.”

33Pomwepo Mose adapatsa ana a Gadi ndi a Rubeni ndiponso theka la fuko la Manase, mwana wa Yosefe, dziko la Sihoni mfumu ya Aamori, ndi dziko la Ogi mfumu ya Basani, dziko lonse pamodzi ndi mizinda ndi milaga yake, ndiye kuti mizinda yonse ya m'dziko lonselo.

34Ana a Gadi adamanga mizinda ya Diboni, Ataroti, Aroere,

35Atiroti-Sofani, Yazere, Yogobeha,

36Betenimira ndi Beteharani. Yonseyo inali yozingidwa ndi malinga. Ndipo adamanganso makola a nkhosa.

37Ana a Rubeni adamanga mizinda ya Hesiboni. Eleyale, Kiriyataimu,

38Nebo, Baala-Meoni (dzina ili lidasinthidwa) ndi Sibima. Mizinda imene adamangayo adaitcha maina ena.

39A fuko la Makiri, mwana wa Manase, adapita kukalanda dziko la Giliyadi napirikitsa Aamori amene ankakhala m'dzikomo.

40Mose adapatsa Makiri mwana wa Manase dziko la Giliyadi, ndipo Makiriyo adakhala m'dziko limenelo.

41Yairi wa fuko la Manase adapita kukalanda midzi ina naitcha Havoti-Yairi.

42Noba adapita kukalanda mzinda wa Kenati pamodzi ndi midzi yake, ndipo adautcha Noba, kutengera dzina lake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help