1 Mbi. 14 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Ntchito za Davide ku Yerusalemu(2 Sam. 5.11-16)

1Hiramu, mfumu ya ku Tiro, adatuma amithenga kwa Davide, pamodzi ndi mitengo ya mkungudza ndiponso amisiri odziŵa kumanga ndi miyala ndi amisiri a matabwa, kuti akammangire nyumba Davideyo.

2Motero Davide adazindikira kuti Chauta wamkhazikitsa kuti akhale mfumu yolamulira Aisraele, ndiponso kuti wakweza ufumu wake chifukwa cha Aisraele, anthu ake.

3Davide adakwatira akazi ena ku Yerusalemu, ndipo adabereka ana enanso aamuna ndi aakazi.

4Ana amene Davide adaberekera ku Yerusalemu ndi aŵa: Samuwa, Sobabu, Natani, Solomoni,

5Ibara, Elisuwa, Elipeleti,

6Noga, Nefegi, Yafiya,

7Elisama, Beeliyada, ndi Elifeleti.

Davide agonjetsa Afilisti(2 Sam. 5.17-25)

8Afilisti atamva kuti Davide wadzozedwa kukhala mfumu yolamulira dziko lonse la Aisraele, adapita onse kukamfunafuna. Davide atamva zimenezo, adatuluka kukamenyana nawo nkhondo.

9Tsono Afilisti adafika nayamba kufunkha m'chigwa cha Refaimu.

10Pamenepo Davide adafunsa kwa Mulungu kuti, “Kodi ndipite kukamenyana nawo nkhondo Afilistiwo? Kodi mudzaŵapereka m'manja mwanga?” Chauta adamuuza kuti, “Inde, pita. Ndidzaŵaperekadi m'manja mwako.”

11Pamenepo Davide adapita ku Baala-Perazimu, ndipo adagonjetsa Afilistiwo kumeneko. Tsono adati, “Ndi dzanja langa Mulungu waŵang'amba pakati adani anga ngati madzi a chigumula.” Nchifukwa chake malo amenewo amatchedwa kuti Baala-Perazimu.

12Afilistiwo adasiya milungu yao kumeneko ndipo Davide adalamula kuti aiyatse moto, ndipo adaitenthadi.

13Nthaŵi ina Afilistiwo adabweranso naloŵa m'chigwa mom'muja.

14Davide atafunsanso Mulungu, Mulungu adamuuza kuti, “Usati uŵalondole. Uchite moŵazungulira, uŵadzere cha kumbuyo, uŵathire nkhondo pa malo oyang'anana ndi mitengo ya mkandankhuku ija.

15Tsono ukakamva phokoso pa nsonga za mitengo ya mkandankhukuyo, pamenepo utuluke kukamenyana nawo. Pakuti Mulungu wakutsogolera kuti ukakanthe gulu lankhondo la Afilistiwo.”

16Davide adachitadi monga momwe Mulungu adaamlamulira, ndipo adagonjetsa gulu lankhondo la Afilistilo kuyambira ku Gibiyoni mpaka ku Gezere.

17Ndipo mbiri ya Davide idawanda ku maiko onse, ndipo Ambuye adachititsa mantha anthu a mitundu yonse kuti azimuwopa Davideyo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help