Owe. 7 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Gideoni agonjetsa Amidiyani.

1Choncho Yerubaala (ndiye kuti Gideoni) ndi anthu onse amene anali naye, adadzuka m'mamaŵa nakamanga zithando zankhondo pambali pa kasupe wa ku Harodi. Zithando za Amidiyani zinali m'chigwa kumpoto kwao, pafupi ndi phiri la More.

2Chauta adauza Gideoni kuti, “Anthu uli nawoŵa andichulukira kwambiri, kuti ndigonjetse Amidiyani, chifukwa Aisraele angamandipeputse Ine ndi kumanena kuti, ‘Tadzipulumutsa ndi mphamvu zathu.’

3Deut. 20.8 Tsono ulengeze kwa anthu kuti, ‘Aliyense amene akuchita mantha ndi kunjenjemera, abwerere kwao.’ ” Ndiye anthu okwanira 22,000 adabwerera, natsala 10,000.

4Chauta adauzanso Gideoni kuti, “Anthuŵa akundichulukirabe kwambiri. Uŵatenge, upite nawo ku madzi, ndipo ndikaŵayesa ndine m'malo mwako kumeneko. Amene ndikuuze kuti, ‘Uyu apite nao,’ adzapita nao. Ndipo amene ndikuuze kuti, ‘Uyu asapite nao,’ sadzapita nao.”

5Choncho Gideoni adapita nawo anthu aja kumadziko. Ndipo Chauta adamuuza kuti, “Onse amene akhathire madzi pakumwa ndi lilime, monga m'mene amachitira galu, uŵaike paokha. Ndipo onse amene agwade kuti amwe madzi, uŵaikenso paokha.”

6Tsono chiŵerengero cha anthu amene adakhathira madzi pakumwa ndi manja chinali anthu 300. Koma anthu ena onse otsala adagwada pansi kuti amwe madzi.

7Ndipo Chauta adauza Gideoni kuti, “Ndidzakupulumutsani ndi anthu 300 okhaŵa amene adakhathira pakumwa madzi, ndipo ndidzapereka Amidiyani m'manja mwako. Koma ena onsewo apite kwao.”

8Choncho Gideoni adatumiza onse kwao kupatula anthu 300 aja. Tsono osankhidwawo adatenga chakudya ndi malipenga a anthuwo. Zithando zankhondo za Amidiyani zinali chakumunsi m'chigwa.

9Usiku womwewo Chauta adauza Gideoni kuti, “Dzuka, pita ukazithire nkhondo zithandozo, pakuti ndazipereka m'manja mwako.

10Koma ngati ukuwopa, uyambe wapita kuzithandoko pamodzi ndi Puri mtumiki wako.

11Udzamva zimene akulankhula, kenaka udzalimba mtima ndipo udzapita kukazithira nkhondo zithandozo.” Pomwepo Gideoni, pamodzi ndi Puri mtumiki wake, adapita ku mbali ina ya zithandozo, kumene kunali ankhondo.

12Amidiyani ndi Aamaleke ndi anthu akuvuma adaaphimba chigwa chonse ngati dzombe chifukwa cha kuchuluka kwao. Ndipo ngamira zao zinali zosaŵerengeka ngati mchenga wa m'mbali mwa nyanja.

13Tsono atafika pafupi, Gideoni adamva munthu akufotokozera mnzake maloto ake. Ankati, “Ine ndalota maloto. Ndinangoona mtanda wa buledi wabarele ukugubuduzika kutsikira ku zithando za Amidiyani ndipo unafika mpaka ku chithando china nuchigunda, kotero kuti chinagwa ndipo nkuphwasukaphwasuka.”

14Ndipo mnzake uja adayankha kuti, “Zimenezi si kanthu kena koma nkhondo ya Gideoni, mwana wa Yoasi, munthu wa ku Israele. Mulungu wapereka Midiyani pamodzi ndi ankhondo ake onse m'manja mwake.”

15Gideoni atamva kufotokoza kwa malotowo pamodzi ndi kumasulira kwake, adagwada pansi nathokoza Mulungu, ndipo adabwerera ku zithando za Aisraele naŵauza kuti, “Dzukani, Chauta wapereka Amidiyani m'manja mwanu.”

16Adaŵagaŵa anthu 300 aja m'magulu atatu, napereka malipenga ndi mbiya m'manja mwa onsewo, ndipo m'mbiyamo onse adaikamo nsakali zoyaka.

17Tsono adauza anthuwo kuti, “Muzindiyang'ana ine, ndipo muchite chimodzimodzi. Ndikafika ku malire a zithando, muchite zomwe ndichite ine.

18Ndikaimba lipenga, ineyo pamodzi ndi onse amene ali ndi ine, inunso muimbe malipenga ku mbali zonse za zithando zonse, ndipo mufuule kuti, ‘Lupanga la Chauta ndi la Gideoni.’ ”

19Choncho Gideoni, pamodzi ndi anthu 100 amene anali naye aja, adafika ku malire a zithando pakati pa usiku, alonda atangosinthana chatsopano apa. Tsono adaimba malipenga, naswa mbiya zimene zinali m'manja mwao zija.

20Apo magulu ena aŵiri aja nawonso adaimba malipenga, naswa mbiya zija, onse atatenga nsakali zija m'dzanja lakumanzere, ndi malipenga oti aziimba m'dzanja lamanja. Ndipo adafuula kuti, “Lupanga la Chauta ndi la Gideoni.”

21Aliyense adaima pamalo pake mozungulira zithandozo, ndipo ankhondo a m'zithando zija adayamba kuthaŵa akufuula.

22Ankhondo 300 aja a Gideoni ataimba malipenga, Chauta adamenyanitsa ankhondo aja a Midiyani. Onse adasokonezeka, mwakuti ankamenyana okhaokha. Ankhondowo adathaŵira ku Betesita cha ku Zerera, mpaka ku malire a Abele-Mehola pafupi ndi Tabati.

23Aisraele a fuko la Nafutali, a fuko la Asere ndi a fuko la Manase lonse, adaitanizana ndipo adapirikitsa Amidiyaniwo.

24Gideoni adatuma amithenga m'dziko lonse lamapiri la Efuremu kuti akanene kuti, “Tsikani mudzalimbane ndi Amidiyani, ndipo mulande madooko ao oolokera mpaka Betebara ndiponso mtsinje wa Yordani.” Choncho Aefuremu onse adasonkhana, nalanda madooko mpaka ku Betebara ndiponso mtsinje wa Yordani.

25Adagwira mafumu aŵiri a Midiyani, Orebu ndi Zebu. Adapha Orebu ku thanthwe la Orebu, ndipo Zebu adamuphera ku malo ofinyira mphesa ku Zebu, pamene ankapirikitsa Amidiyani. Tsono adabwera ndi mutu wa Orebu ndi wa Zebu kwa Gideoni kutsidya kwa Yordani.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help