1Usachite choipa,
ndipo choipa sichidzakugwera.
2Pewa choipa,
ndipo choipa chidzakulambalala.
3Mwana wanga, usabzale mbeu za kusalungama,
kuti ungadzakolole zipatso zoipa kasanunkaŵiri.
4Usapemphe Ambuye kuti akupatse udindo waukulu,
kapena mfumu kuti ikupatse malo aulemu.
5Usadziwonetse kuti ndiwe wolungama pamaso pa Ambuye,
kapena kuti ndiwe wanzeru pamaso pa mfumu.
6Usafune kukhala woweruza,
kuwopa kuti nkudzalephera kuthetsa zosalungama,
kuwopanso kuti mwina nkudzakondera akuluakulu ena,
nulephera kukhala wachilungamo potero.
7Usachimwire gulu lonse la anthu amumzinda
ndi kutaya choncho ulemu wako pamaso pa onse.
8Usachite kubwereza kaŵiri kuchimwa.
Pajatu ngakhale utachimwa kamodzi kokha
sungalephere kulangidwa.
9Usanene kuti, “Mulungu adzaŵerengera mphatso
zanga zochulukazi;
ndikadzapereka chinthu kwa Mulungu Wopambanazonse,
ndithu adzachilandira.”
10Usatope ndi kupemphera, usaleke kuthandiza osauka.
11Usaseke munthu amene ali ndi chisoni mu mtima,
chifukwa wotsitsa anthu Uja amathanso kuŵakweza.
12Usaganizire zonamizira mbale wako,
kapena kunamizira bwenzi lako.
13Usanene zabodza nthaŵi ina iliyonse,
chifukwa bodza silipindulitsa.
14Usalankhule zambiri pakati pa akulu,
usabwerezebwereze mau m'mapemphero ako.
15Usadane ndi ntchito yamanja kapena yolima,
chifukwa adaifuna ndi Mulungu Wopambanazonse.
16Usakhale nawo m'magulu a anthu ochimwa,
kumbukira kuti chilango chidzafika msanga.
17Udzichepetse mtima kwambiri,
chifukwa anthu osalabadira za Mulungu
amalangidwa ndi moto ndi mphutsi.
Za abwenzi ndi achibale18Usalekane ndi bwenzi lako chifukwa chofuna ndalama,
usalekane ndi mbale wako weniweni chifukwa
chofuna golide wa ku Ofiri.
19Usalekane naye mkazi wanzeru ndi wabwino,
chifukwa chikoka chake nchopambana golide.
20Usazunze kapolo amene akugwira ntchito mokhulupirika,
kapena wantchito amene akuikapo mtima pa ntchito.
21 Eks. 21.2; Deut. 15.12-15 Kapolo wabwino umkonde ndi mtima wako wonse,
kapolo wotere usamletse kupeza ufulu wake.
22Kodi uli ndi zoŵeta? Uzisamale bwino.
Ngati zimakupindulitsa, uzisunge.
23Ngati uli ndi ana aamuna,
uŵaphunzitse kusunga mwambo akadali aang'ono.
24Ngati uli ndi ana aakazi,
uwone kuti adzisunge, usamaŵasasatitsa.
25Ukwatitse mwana wako wamkazi.
Ukatero wamaliza ntchito yaikuludi.
Koma tsono umkwatitse ndi mwamuna wanzeru.
26Ngati uli ndi mkazi amene umamkonda, usamsudzule.
Koma ngati sumukonda, usamkhulupirire.
27 Eks. 20.12 Uzilemekeza bambo wako ndi mtima wako wonse,
ndipo usaiŵale mavuto a mai wako pokubala.
28Kumbukira kuti ndiwo amene adakubereka.
Kodi ungaŵabwezere chiyani pa zimene adakuchitira?
Za ansembe29Uziwopa Ambuye ndi mtima wako wonse,
ndipo uzilemekeza ansembe ake.
30Uzikonda Mlengi wako ndi mphamvu zako zonse,
ndipo usatayane nawo atumiki ake.
31Uziwopa Ambuye, ndipo uzilemekeza wansembe
ndi kumpatsa zimene zimuyenera monga adakulamulira,
monga zipatso zoyamba kucha, nsembe zopepesera kupalamula,
mwendo wamwamba wa nyama, nsembe yoyeretsera,
ndi zipatso zoyamba za zinthu zoyera.
Za anthu osauka32Uzithandizanso mwaufulu anthu osauka,
kuti udale kwenikweni.
33Umchitire zaufulu aliyense wamoyo,
ndi anthu akufa omwe usaŵamane zachifundo.
34Olira usaŵafulatire,
koma umve nawo chisoni amene ali pa chisoni,
35Usagwere ulesi kuyendera odwala,
poti adzakukonda chifukwa cha chifundo chakocho.
36Pa zonse zimene ukuchita
ukumbukire mathero ako;
ukatero sudzachimwa pa moyo wako wonse.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.