1Nzeru idamanga nyumba yake,
idaimika nsanamira zake zisanu ndi ziŵiri.
2Idapha ziŵeto zake, idakonza vinyo wake,
nkuyala tebulo lake.
3Idatuma adzakazi ake
kuti akakhalire pa malo apamwamba mu mzinda
ndipo akalengeze kuti,
4“Munthu wamba aliyense abwere kuno!”
Kwa munthu wopanda nzeru imati,
5“Bwera, dzadyeko chakudya changa,
ndipo udzamweko vinyo amene ndakonza.
6Leka kupulukira kwako, kuti ukhale ndi moyo,
uziyenda m'njira ya nzeru.”
7Woyesa kukonza munthu wonyoza, amangonyozekerapo,
wodzudzula munthu woipa, amangopwetekerapo.
8Wonyoza usamdzudzule, angadane nawe.
Koma ukadzudzula munthu wanzeru, adzakukonda.
9Wanzeru ukamlangiza, adzakhala wanzeru koposa.
Munthu wochita chilungamo ukamuphunzitsa,
adzadziŵa zambiri koposa.
10 Yob. 28.28; Mas. 111.10; Miy. 1.7 Kulemekeza Chauta ndiye chiyambi cha nzeru,
kudziŵa Woyera uja nkukhala womvetsa bwino zinthu.
11Chifukwa cha ine nzeru, masiku ako adzachuluka,
ndipo ndidzaonjezera zaka pa moyo wako.
12Ngati ndiwe wanzeru, phindu ndi lako.
Ngati umanyoza ena, udzavutika ndiwe wekha.
13Mkazi wopusa ngwaphokoso,
ngwosachangamuka, ndiponso wosamvetsa zinthu.
14Amakhala pakhomo pa nyumba yake,
pamalo pena pooneka bwino mu mzinda.
15Akatero nkumaitana amene akudutsapo,
amene akungodziyendera, osafuna kupatuka.
16“Amati, inu anthu wamba, tapatukirani muno!”
Tsono kwa wopanda nzeru amati,
17“Madzi akuba ndiwo amatsekemera,
buledi wodya mobisa ndiye amakoma.”
18Koma mwamunayo sadziŵa kuti kumeneko kuli imfa,
kuti alendo ake aloŵa kale m'manda ozama.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.