Mla. 12 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Uzikumbukanso Mlengi wako pa masiku a unyamata wako, masiku oipa asanafike, zisanafikenso zaka zoti uzidzati, “Moyowu wandikola.”

2Nthaŵi ya ukalamba wako, dzuŵa, kuŵala, mwezi, nyenyezi, zonse zidzakudera, ndipo mitambo idzabweranso mvula itagwa.

3Nthaŵi imeneyo miyendo yako izidzanjenjemera, manja ako adzafooka. Mano ako oŵerengekawo azidzalephera nkutafuna komwe, ndipo maso ako adzayamba kuchita chidima.

4Makutu ako adzatsekeka ndipo sudzamva phokoso lakunja. Sudzamvanso kusinja kwapamtondo kapena kulira kwa mbalame m'mamaŵa.

5Udzaopa kukwera pa malo apamwamba, ndipo nkuyenda komwe kudzakhala koopsa. Kumutu kudzangoti mbu, udzalephera nkuyenda kodziguza komwe, ndipo chilakolako chilichonse chidzakuthera. Tonse tikupita kwathu kokakhala mpaka muyaya, ndipo titapita kudzakhala kulira m'miseu yonse.

6Nthambo yasiliva idzamasuka, mbale yagolide idzasweka, mtsuko udzaphwanyika ku kasupe, ndipo mkombero udzathyoka ku chitsime.

7Pamenepo thupi lidzabwerera ku dothi monga m'mene lidaaliri, ndipo mzimu udzabwerera kwa Mulungu amene adaupereka.

8Nkuwonatu Mlaliki akuti, “Zonse nzopanda phindu. Ndithudi, zonse nzopandapake.”

Mau otsiriza

9Chifukwa chakuti Mlalikiyo anali waluntha, adaphunzitsa anthu zambiri. Ankasinkhasinkha, kufufuzafufuza ndi kulongosola malangizo mosamala kwambiri.

10Mlalikiyo ankafunafuna mau ogwira mtima, ndipo adalemba mau oona ndi mtima wolungama.

11Mau a anthu anzeru ali ngati zisonga, ndipo zokamba zao zimene adasonkhanitsa zili ngati misomali yokhomerera kwambiri. Zolankhula zonsezo amapereka ndi Mbusa mmodzi yekha.

12Mwana wanga, uchenjere ndi kalikonse kobzola pamenepa. Kulemba mabuku sikutha, ndipo kuphunzira kwambiri kumatopetsa thupi.

13Basi, zonse zamveka. Mfundo yeniyeni ya zonsezi ndi iyi: Uzimvera Mulungu, ndipo uzitsata malamulo ake, pakuti umenewu ndiwo udindo wake wonse wa munthu.

14Pajatu Mulungu adzaweruza zonse zimene timachita, zabwino kapena zoipa, ngakhale ndi zam'chinsinsi zomwe.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help