Yer. 30 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Lonjezo la kubwereranso ku Yerusalemu

1Chauta adauza Yeremiya kuti,

2“Ine Chauta, Mulungu wa Israele, ndikunena kuti, Lemba m'buku zonse zimene ndakuuza.

3Nthaŵi ikubwera yoti ndidzaŵabwezere anthu anga, Israele ndi Yuda, ku dziko limene ndidapatsa makolo ao, ndipo lidzakhaladi lao.”

4Mau amene akunena za Israele ndi Yuda ndi aŵa:

5“Tamva kulira kwankhaŵa, kufuula kwamantha,

ndipo palibe mtendere paliponse.

6Funsani kuti muzindikire,

Kodi munthu wamwamuna angathe kubala mwana?

Nanga nchifukwa chiyani ndikuwona munthu

wamwamuna aliyense atagwira manja pa mimba

ngati mkazi pa nthaŵi yake yochira?

Chifukwa chiyani nkhope zonse zagwa?

7Kalanga ine!

Tsiku limenelo nlalikulu kwambiri,

sipadzakhala lina lofanana nalo.

Idzakhala nthaŵi yamavuto kwa Yakobe,

komabe adzapulumuka ku mavutowo.”

8Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Tsiku limenelo ndidzathyola goli laukapolo m'khosi mwao, ndidzadula zingwe zoŵamanga. Aisraele sadzakhalanso akapolo a alendo.

9Azidzangotumikira Chauta, Mulungu wao, ndi Davide, mfumu yao, amene ndidzaŵasankhulira.

10 Yer. 46.27, 28 “Nchifukwa chake musachite mantha

inu a m'banja la Yakobe, mtumiki wanga,

musataye mtima inu Aisraele,”

akuterotu Chauta.

“Ndithu ndidzakupulumutsani kuchokera ku dziko lakutali.

Ndidzapulumutsanso zidzukulu zanu

kuchokera kudziko kumene ali mu ukapolo.

Nonsenu mudzabwereranso,

ndipo mudzakhala ndi mtendere popanda okuwopsani.

11Ine ndili nanu, ndipo ndidzakupulumutsani,”

akuterotu Chauta.

“Ndidzaononga mitundu yonse ya anthu

kumene ndidakubalalitsani,

koma inu sindidzakuwonongani kotheratu.

Ndidzakulangani potsata chilungamo,

sindingakulekerereni osakulangani konse.”

12Chauta akunena kuti,

“Chilonda chanu nchosachizika,

bala lanu nlonyeka.

13Palibe amene angathe kukutetezani pa mlandu wanu.

Palibe mankhwala opoletsa chilonda chanu.

Palibe mankhwala ochiza nthenda yanu.

14Abwenzi anu onse akuiŵalani,

sakulabadiraninso.

Ndakulangani mwankhanza,

poti mlandu wanu ndi waukulu,

machimo anu ndi ambiri.

15Chifukwa chiyani mukudandaula nacho chilonda chanu?

Bala lanu silingapole ai.

Mlandu wanu ndi waukulu,

machimo anu ngambiri,

nchifukwa chake ndakuchitani zimenezi.

16Tsono onse amene adakuwonongani inu,

ndidzaŵaononga iwonso.

Onse okuzunzani adzatengedwa ukapolo.

Onse ofunkha zinthu zanu,

nawonso zao zidzafunkhidwa.

Ndipo onse okusakazani,

ndidzachita zoti nawonso aŵasakaze.

17Koma inuyo, ndidzachiza matenda anu,

ndidzapoletsa mabala anu,

chifukwa anthu ena amati ndinu otayika,

amati,

‘Ndi anthu a ku Ziyoni aŵa, opanda oŵasamala,’ ”

akuterotu Chauta.

18Chauta akunena kuti,

“Ndidzabwezeranso a banja la Yakobe ku dziko lao.

Ndidzaonetsanso chikondi changa ku malo ake onse.

Mzinda wa Yerusalemu uja udzamangidwanso

pabwinja pake pompaja.

Nyumba yaufumu idzamangidwanso pamalo pake.

19Anthuwo adzaimba nyimbo zoyamika Chauta,

ndipo padzamveka phokoso la chisangalalo.

Ndidzaŵachulukitsa, sadzakhalanso oŵerengeka ai.

Ndidzaŵapatsa ulemerero, ena sadzaŵanyozanso.

20Ana ao adzakhalanso monga m'mene adaaliri kale.

Mpingo wao wonse ndidzaukhazikitsanso Mwiniwakene.

Ndidzalanga onse oŵazunza.

21Wodzaŵalamulira adzakhala mmodzi mwa iwo.

Mtsogoleri wao adzachokera pakati pao.

Ineyo ndidzamkokera pafupi nane,

ndipo iye adzayandikana nane.

Ndanitu angalimbe mtima payekha

kuti ayandikane ndi Ine?”

Akutero Chauta.

22“Motero inu mudzakhala anthu anga,

ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wanu.

23“Onani, mphepo yamkuntho ya Chauta!

Mkuntho wamphamvu wa kamvulumvulu,

ukuwomba pa mitu ya anthu olakwa.

24Mkwiyo wa Chauta sudzachoka

mpaka utatsiriza kuchita zonse

zimene mtima wa Chautayo ukufuna.

Mudzamvetsa zimenezi masiku akubwerawo.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help