Aro. 9 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mulungu ndi Aisraele, anthu ake osankhidwa

1Ndithudi ndikunena zoona ine amene ndili wake wa Khristu, ndipo sindikunama ai. Mtima wanga, umene Mzimu Woyera amautsogolera, ukundichitira umboni kuti

2ndili ndi chisoni chachikulu. Ndipo ukundipweteka kosalekeza chifukwa cha abale anga, anthu a mtundu wangaŵa.

3Ndikadakonda kuti m'malo mwao, ineineyo ndikhale wotembereredwa, osakhalanso wake wa Khristu.

4Eks. 4.22 Iwoŵa ndi Aisraele, amene Mulungu adaŵasankha kuti akhale ana ake, ndipo adaŵapatsa ulemerero. Mulungu adachita nawo mapangano, ndipo adaŵapatsa Malamulo ake. Adaŵaphunzitsa mwambo wachipembedzo, ndipo adaŵapatsa malonjezo ake.

5Iwoŵa ndi zidzukulu za makolo athu akale aja, ndipo Mpulumutsi wolonjezedwa uja ndi wa mtundu wao, kunena za umunthu wake. Mulungu amene amalamulira zonse, alemekezeke mpaka muyaya. Amen.

6Sindiye kutitu Mulungu sadasunge malonjezo ai. Pakuti si anthu onse obadwa mu mtundu wa Aisraele amene ali Aisraele enieni.

7Gen. 21.12 Ndiye kuti si zidzukulu zonse za Abrahamu zimene zili ana a Mulungu. Koma Mulungu adauza Abrahamu kuti, “Ana a Isaki okha ndiwo adzatchedwa zidzukulu zako.”

8Ndiye kuti, si ana onse a Abrahamu amene ali ana a Mulungu ai. Zidzukulu zake zenizeni ndi ana okhawo amene adabadwa potsata lonjezo la Mulungu.

9Gen. 18.10 Paja Mulungu adalonjeza pakunena kuti, “Ndidzabwera pa nthaŵi yake ndipo Sara adzakhala ndi mwana.”

10Ndipo si pokhapo ai. Ana aŵiri a Rebeka aja bambo wao anali mmodzi, kholo lathu Isaki.

11Gen. 25.23Ngakhale anawo asanabadwe, ndiye kuti tsono asanachite chilichonse chabwino kapena choipa, Mulungu adaafunabe kuti cholinga chake chosankhira munthu aliyense chipitirire. Izi adachita osati chifukwa cha ntchito za munthu koma chifukwa chakuti Mulungu adamuitana munthuyo.

12Motero Mulungu adauza Rebeka kuti, “Wamkuluyu adzatumikira wamng'onoyu.”

13Mal. 1.2, 3 Paja Malembo akuti, “Yakobe ndidaamukonda, koma Esau ndidaadana naye.”

14Pamenepo tinganene chiyani tsono? Kodi tinganene kuti Mulungu ngwosalungama? Iyai, sitingatero.

15Eks. 33.19 Pajatu Iye adaauza Mose kuti,

“Ndidzachitira chifundo

amene ndifuna kumchitira chifundo,

ndidzamvera chisoni

amene ndifuna kumumvera chisoni.”

16Motero chachikulu si zimene munthu azifuna, kapena zimene munthu amayesetsa kuchita, koma chachikulu ndi chifundo cha Mulungu.

17Eks. 9.16 Ndi monga m'Malembo timaŵerenga kuti Mulungu adaauza Farao kuti, “Ndidakulonga ufumu, kuti mwa iwe ndiwonetse mphamvu zanga, ndiponso kuti ndimveketse dzina langa pa dziko lonse lapansi.”

18Motero timaona kuti Mulungu amachitira chifundo munthu amene Iye afuna kumchitira chifundo, ndipo amamsandutsa wokanika munthu amene Iye afuna kumsandutsa wokanika.

Mulungu amakwiya ndiponso amachita chifundo

19Tsono kapena wina nkundifunsa kuti, “Ngati zili choncho, chifukwa chiyani Mulungu akuŵadzudzulabe anthu? Nanga ndani angaletse Mulungu kuchita zimene Iye afuna?”

20Yes. 29.16; 45.9; Lun. 12.12Koma iwe, munthu chabe, ndiwe yani kuti nkumatsutsana ndi Mulungu? Kodi mbiya nkufunsa woiwumba kuti, “Bwanji mwandiwumba motere?”

21Lun. 15.7; Mphu. 33.13Kodi kapena woumba sangathe kuumba mbiya ziŵiri ndi dothi lomwelo, ina ya masiku apadera ina ya masiku onse?

22 Lun. 12.20, 21 Mulungunso ndi momwemo. Adaafuna kuwonetsa mkwiyo wake, nafunanso kuti mphamvu zake zidziŵike. Komabe adapirira moleza mtima kwambiri zochita za anthu amene Iye adaaŵakwiyira, ndipo amene adaayeneradi kuwonongedwa.

23Mulungu adaafunanso kuti udziŵike ulemerero wake waukulu pa ife, amene Iye adatichitira chifundo, natikonzeratu kuti tilandire ulemerero.

24Pajatu ife ndife amene Mulungu adatiitana, osati kuchokera kwa Ayuda okha ai, komanso kuchokera kwa anthu a mitundu ina.

25Hos. 2.23 Ndi monga momwe Mulungu akunenera m'buku la mneneri Hoseya kuti,

“Amene sanali anthu anga,

ndidzaŵatcha ‘Anthu anga’.

Mtundu umene sindinkaukonda,

ndidzautcha ‘Wokondedwa wanga’.

26 Hos. 1.10 Ndipo kumalo komwe iwo adauzidwa kuti,

‘Sindinu mtundu wanga’,

kumeneko adzatchedwa ‘Ana a Mulungu wopatsa moyo.’ ”

27 Yes. 10.22, 23 Ndipo mneneri Yesaya adaanena mokweza mau za Aisraele kuti, “Ngakhale Aisraele achuluke ngati mchenga wakunyanja, koma oŵerengeka okha adzapulumuka.

28Pakuti Ambuye adzagamula milandu ya anthu pa dziko lapansi. Ndipo adzachita zimenezi mofulumira ndi mwachidule.”

29Yes. 1.9 Izi zili monga momwe Yesaya adaaneneratunso kale kuti,

“Ambuye amphamvuzonse

akadapanda kutisiyirako zidzukulu zina,

tikadafafanizidwa ngati Sodomu ndi Gomora.”

Za Aisraele ndi Uthenga Wabwino

30Tsono pamenepo tinene chiyani? Tinene kuti anthu a mitundu ina, amene sankalabadira zoti akhale olungama pamaso pa Mulungu, adachilandira chilungamocho pakukhulupirira.

31Koma Aisraele amene ankayesetsa kukhala olungama pamaso pa Mulungu pakusunga Malamulo a Mose, adalephera.

32Chifukwa chiyani? Chifukwa ankafuna kupezeka kuti ngolungama pamaso pa Mulungu, osati pakukhulupirira, koma pakudalira ntchito zabwino. Adaphunthwa pa mwala wophunthwitsa anthu,

33Yes. 28.16monga Malembo anenera kuti,

“Inetu ndikuika m'Ziyoni mwala wodzakhumudwitsa anthu,

thanthwe limene lidzaŵagwetsa.

Koma wokhulupirira Iyeyo, sadzachita manyazi.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help