1Muziyesetsa kukhala nacho chikondi, komanso muike mtima pa mphatso zimene Mzimu Woyera amapereka, makamaka mphatso ya kulankhula mau ochokera kwa Mulungu.
2Munthutu wolankhula chilankhulo chosadziŵika, salankhula ndi anthu ai, koma ndi Mulungu. Palibe munthu womvetsa zimene iyeyo akunena, Mzimu Woyera ndiye amamlankhulitsa zachinsinsi.
3Koma wolankhula mau ochokera kwa Mulungu, amalankhula ndi anthu, ndipo amaŵathandiza, amaŵalimbitsa mtima ndi kuŵasangalatsa.
4Munthu wolankhula chilankhulo chosadziŵika, amangothandizidwa yekha, koma wolankhula mau ochokera kwa Mulungu, amathandiza mpingo.
5Ndikadakonda kuti nonsenu mukhale nayo mphatso ya kulankhula zilankhulo zosadziŵika, koma makamaka ndikadakonda kuti nonsenu mukhale ndi mphatso ya kulankhula mau ochokera kwa Mulungu. Pakuti munthu wolankhula mau ochokera kwa Mulungu, ndiye wofunika kwambiri kuposa wolankhula zilankhulo zosadziŵika, ngati palibe munthu wotanthauzira zilankhulo, kuti mpingo upindulepo.
6Abale, mudzapindulanji ngati ndibwera kwa inu nkumadzalankhula m'zilankhulo zosadziŵika? Simudzapindula konse ndi kulankhula kwangako, ngati m'mau angawo mulibe zina zimene Mulungu wandiwululira, kapena zina zopatsa nzeru, kapena zina zimene Mulungu andipatsa kuti ndinene, kapenanso phunziro lina.
7Ndi ngati zipangizo zopanda moyo zimene zili ndi liwu, monga toliro kapena zeze. Woziliza akapanda kusiyanitsa bwino maliwu ake, womvera sangadziŵe nyimbo imene ikuimbidwa.
8Ndiponso woliza lipenga akapanda kuliliza momveka bwino, ndani angakonzekere nkhondo?
9Inunso chimodzimodzi: munthu angadziŵe bwanji zimene mukulankhula, ngati polankhula simunena mau omveka bwino? Pamenepo mudzangotaya mau anu pachabe.
10Mosapeneka konse pali zilankhulo zamitundumitundu pa dziko lapansi, ndipo palibe ndi chimodzi chomwe chimene mau ake alibe tanthauzo.
11Koma ngati ine sindidziŵa tanthauzo la mau a m'chilankhulo, ndidzakhala mlendo kwa amene akulankhula, ndipo iyenso adzakhala mlendo kwa ine.
12Inunso chimodzimodzi: popeza kuti mwaika mtima pa mphatso za Mzimu Woyera, muziyesetsa kuzigwiritsa ntchito, makamaka mphatso zolimbikitsa mpingo.
13Nchifukwa chake munthu wolankhula chilankhulo chosadziŵika, apemphere kuti alandirenso mphatso ya kuchitanthauzira.
14Ngati ndipemphera m'chilankhulo chosadziŵika, mtima wanga ukupemphera inde, koma nzeru zanga sizipindulapo kanthu pamenepo.
15Nanga pamenepa nkutani? Ndidzapemphera ndi mtima wanga, komanso ndi nzeru zanga. Ndidzaimba ndi mtima wanga, komanso ndi nzeru zanga.
16Mukayamika Mulungu ndi mtima wanu wokha, nanga munthu amene ali nanu pamodzi, koma sadziŵa zamumtimazo, angavomereze bwanji kuti, “Amen!” pa pemphero lanu lothokoza Mulungu, pamene sakudziŵa zimene inuyo mukunena.
17Ngakhale inu muthokoze Mulungu bwinobwino, koma munthu winayo sapindulapo konse.
18Ndikuthokoza Mulungu kuti ine ndimalankhula m'zilankhulo zosadziŵika kuposa nonsenu.
19Komabe mu msonkhano wa mpingo, m'malo molankhula mau ochuluka m'chilankhulo chosadziŵika, ndingakonde kwambiri kunena mau asanu okha omveka bwino, kuti ndiphunzitsire anthu.
20Abale, musamaganiza zachibwana. Pa zoipa, khalani ngati ana osadziŵa, koma pa maganizo anu, mukhale okhwima.
21Yes. 28.11, 12 M'Malembo mudalembedwa kuti,
“Ndidzalankhula ndi mtundu uwu
kudzera mwa anthu a zilankhulo zachilendo,
ndiponso ndi pakamwa pa anthu achilendo.
Koma ngakhale nditero, sadzandimvera,
akutero Chauta.”
22Motero kulankhula m'zilankhulo zosadziŵika, ndi chizindikiro kwa anthu osakhulupirira, osati kwa anthu okhulupirira. Koma kulankhula mau ochokera kwa Mulungu, ndi chizindikiro kwa anthu okhulupirira, osati kwa osakhulupirira.
23Tsono ngati mpingo wonse usonkhana pamodzi, ndipo onse ayamba kulankhula zilankhulo zosadziŵika, nanga mukaloŵa anthu osadziŵa kapena osakhulupirira, kodi iwo sadzayesa kuti ndinu amisala?
24Koma ngati onse alankhula mau ochokera kwa Mulungu, ndipo munthu wosakhulupirira kapena wosadziŵa aloŵa, adzatsutsidwa ndi zonse zimene akumva. Mau onsewo adzamuloŵa mu mtima,
25ndipo zobisika za mumtima mwake zidzaonekera poyera. Pamenepo iye adzadzigwetsa choŵerama pansi ndi kupembedza Mulungu, ndipo adzavomereza kuti Mulungu ali pakati panudi.
Zonse zizichitika molongosoka mu mpingo26Ndiye titani tsono, abale? Pamene musonkhana pamodzi, aliyense angathe kukhala ndi nyimbo, kapena phunziro loti aphunzitse, kapena kanthu kena kamene Mulungu wamuululira, kapena mau oti alankhule m'chilankhulo chosadziŵika, ndipo wina afuna kutanthauzira mauwo. Komatu cholinga cha zonsezi chikhale kulimbikitsa mpingo.
27Ngati alipo ena ofuna kulankhula m'chilankhulo chosadziŵika, alankhule aŵiri okha, kapena atatu, koma osapitirira pamenepo. Alankhule modikirana, ndipo pakhale wina wotanthauzira mauwo.
28Koma ngati palibe munthu wotha kutanthauzira mauwo, iyeyo akhale chete mu msonkhano, ndipo azingolankhula ndi Mulungu payekha.
29Kunena za olankhula mau ochokera kwa Mulungu, aŵiri kapena atatu alankhule, ndipo ena onse aweruze zimene iwowo akunena.
30Koma Mulungu akaulula kanthu kwa munthu wina amene ali pomwepo, amene akulankhulayo akhale chete.
31Nonsenu mungathe kulankhula mau ochokera kwa Mulungu malinga nkupatsana mpata, kuti onse aphunzire ndi kulimbikitsidwa.
32Anthu amene ali ndi mphatso ya kulankhula mau ochokera kwa Mulungu, adziŵe kuilamulira mphatsoyo.
33Mulungu safuna chisokonezo ai, koma mtendere. Monga zimachitikira m'mipingo yonse ya anthu a Mulungu,
34akazi akhale chete m'misonkhano ya mpingo, pakuti iwo saloledwa kulankhula. Monga Malamulo a Mose anenera, akazi azikhala omvera.
35Ngati ali ndi mafunso, akafunse amuna ao kunyumba. Pajatu nchamanyazi kuti mkazi alankhule mu msonkhano wa mpingo.
36Monga nkuti mau a Mulungu adachokera kwa inu? Kaya kapena adafika kwa inu nokha?
37Ngati wina akuyesa kuti akulankhula mau ochokera kwa Mulungu, kapena kuti akuuzidwa mau ndi Mzimu Woyera, avomereze kuti zimene ndikukulemberanizi ndi lamulo lochokera kwa Ambuye.
38Ngati munthuyo savomereza zimenezi, Mulungunso samuvomereza iyeyo.
39Nchifukwa chake tsono, abale anga, ikani mtima pa kulankhula mau ochokera kwa Mulungu, ndipo musaletse anthu kulankhula zilankhulo zosadziŵika.
40Koma tsono, zonse zizichitika moyenera ndi molongosoka.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.