1 Aro. 4.7, 8 Ngwodala amene zolakwa zake zakhululukidwa,
amene machimo ake afafanizidwa.
2Ngwodala amene Chauta samuŵerengera mlandu wake,
amene mumtima mwake mulibe zonyenga.
3Pamene ndinali ndisanaulule tchimo langa,
thupi langa linali lofooka,
chifukwa cha kubuula tsiku lonse.
4Pakuti usana ndi usiku dzanja lanu lidandipsinja,
motero nyonga zanga zidatha,
monga amafotera masamba ndi dzuŵa lachilimwe.
5Koma ndidavomera tchimo langa kwa Inu,
sindidabise kuipa kwanga.
Ndidati, “Ndidzaulula machimo anga kwa Chauta,”
pomwepo Inu mudakhululukiradi
mlandu wa machimo anga.
6Nchifukwa chake munthu aliyense wosamala za Inu
apemphere kwa Inu.
Akadzafika mavuto, akadzafika madzi a chigumula,
zonsezo sizidzamufika.
7Inu ndinu kobisalira kwanga.
Inu mumanditchinjiriza nthaŵi yamavuto.
Nchifukwa chake ndimaimba nyimbo
zotamanda chipulumutso chanu.
8Chauta akuti,
“Ndidzakudziŵitsa ndi kukuphunzitsa njira
imene uyenera kuyendamo.
Ndidzakulangiza ndi kukuyang'anira.
9“Musakhale opanda nzeru ngati kavalo kapena bulu
amene ayenera kumuwongolera
ndi chitsulo cham'kamwa ndi chapamutu,
chifukwa ukapanda kutero, nyamazo sizidzakumvera.”
10Anthu oipa amapeza zoŵaŵa zambiri,
koma munthu wokhulupirira Chauta
amazingidwa ndi chikondi chosasinthika.
11Sangalalani ndi kukondwa
inu nonse okonda Mulungu,
chifukwa cha zimene Chautayo adakuchitirani.
Inu anthu ake onse, fuulani ndi chimwemwe.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.