1 Tim. 2 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za misonkhano yachipembedzo

1Tsono choyamba ndikukupemphani kuti pakhale mapemphero opempherera anthu onse. Mapemphero ake akhale opemba, opempha ndi othokoza Mulungu.

2Muziŵapempherera mafumu ndi onse amene ali ndi ulamuliro, kuti tikhale ndi moyo wabata ndi wamtendere, tizitamanda Mulungu pa zonse ndi kumadzilemekeza.

3Zimenezi nzabwino ndi zokondweretsa pamaso pa Mulungu, Mpulumutsi wathu.

4Iye amafuna kuti anthu onse apulumuke ndipo kuti adziŵe choona.

5Pajatu Mulungu ndi mmodzi yekha, Mkhalapakati mmodzi yekhanso pakati pa Mulungu ndi anthu, munthu uja timati Khristu Yesu.

6Iyeyo adadzipereka kuti akhale momboli wa anthu onse. Umenewu unali umboni umene udaperekedwa pa nthaŵi yake.

72Tim. 1.11 Nchifukwa chake ine adandiika kuti ndikhale mlaliki wake ndiponso mtumwi, wophunzitsa anthu a mitundu ina mau a chikhulupiriro choona. Sindikunamatu ai, ndikunena zoona.

8Ndikufuna kuti paliponse amuna popemphera azikweza manja ao kwa Mulungu momchitira ulemu, mopanda mkwiyo kapena kukangana.

9 1Pet. 3.3 Ndikufunanso kuti akazi azivala mwaulemu, mwanzeru ndi moyenera. Inde adzikongoletse, komatu osati ndi tsitsi lochita kukonza monyanyira, kapena ndi zokongoletsa zagolide, kapena mikanda yamtengowapatali, kapena zovala zamtengowapatali.

10Kwenikweni adzikongoletse ndi ntchito zabwino, monga ayenera kuchitira akazi amene amati ndi opembedza Mulungu.

11Akazi pophunzitsidwa, azikhala chete ndi a mtima wodzichepetsa.

12Sindilola kuti mkazi aziphunzitsa kapena kukhala ndi ulamuliro pa amuna. Mkazi kwake nkukhala chete.

13Gen. 2.7; Gen. 2.21, 22 Paja Adamu ndiye adaayambira kulengedwa, pambuyo pake Heva.

14Gen. 3.1-6 Ndiponso si Adamu amene adaanyengedwa, koma mkaziyo ndiye adaanyengedwa, naphwanya lamulo la Mulungu.

15Koma mkazi adzapulumukabe kudzera m'kubala ana, malinga akalimbikira modzichepetsa m'chikhulupiriro, m'chikondi ndi m'kuyera mtima.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help