Daniel Greek 14 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Belo ndi Chinjoka

1Mfumu Asitiyage atafa, Kirusi wa ku Persiya adaloŵa m'malo mwake.

2Daniele ndi mfumu Kirusi anali pa chinzao, motero mfumu inkamulemekeza kwambiri Daniele kupambana abwenzi ake onse.

3Anthu a ku Babiloni anali ndi fano lina dzina lake Belo. Tsiku ndi tsiku anthu ankalipatsa madengu khumi ndi aŵiri a ufa wosalala, nkhosa makumi anai ndi mitsuko ya vinyo makumi asanu.

4Mfumuyo inkalemekeza Belo ngati mulungu wake, ndipo inkapita kukampembedza tsiku ndi tsiku. Koma Daniele ankapembedza Mulungu wake.

5Tsiku lina mfumu idafunsa Daniele kuti, “Kodi iwe, chifukwa chiyani supembedza nawo Belo?” Iye adayankha kuti, “Nchifukwa choti sindipembedza mafano opangidwa ndi anthu. Koma ndimapembedza Mulungu wamoyo, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndipo amalamulira anthu onse.”

6Mfumu idafunsa kuti, “Monga iweyo sukhulupirira kuti Belo ndi mulungu wamoyo? Suwona kuti amadya kwambiri ndi kumwa tsiku ndi tsiku?”

7Daniele adaseka, nati, “Musanyengedwe amfumu, Belo wanuyu ndi mtapo chabe ndipo kunja kwake adakutidwa ndi mkuŵa. Chikhalire sanadyepo kanthu kapena kumwa chilichonse.”

8Apo mfumu idakwiya nkuitana ansembe a Belo, niŵauza kuti, “Ngati simundiwuza munthu amene amadya chakudya chonsechi, inuyo mwafa. Koma mutatsimikiza kuti ndi Belodi amene amadya, ndiye kuti Daniele aphedwa, chifukwa chonyoza Belo.”

9Daniele adayankha mfumu kuti, “Chabwino, zikhale monga momwe mwaneneramu.”

10Adaalipo ansembe makumi asanu ndi aŵiri a Belo, osaŵerengera akazi ao ndi ana.

11Mfumu idapita ku nyumba ya Belo pamodzi ndi Daniele. Ansembe a Belo adauza mfumu kuti, “Tsopano tikutuluka, tikusiyani amfumu, kuti muike ndinu chakudya ndi vinyo. Pambuyo pake mungathe kutseka chitseko nkusindikizapo chidindo chanu.

12Tsono inu amfumu mukabwera m'maŵa, mukadzapeza kuti chakudyachi Belo sadadye, mudzatiphe. Koma mukadzapeza kuti Belo wadya, ndiye kuti Daniele adzafa, chifukwa chotinyengezera ife.”

13Pamenepo ansembewo sadade nkhaŵa, chifukwa kunsi kwa tebulo adaaboola khomo lodziŵa okha, limene ankaloŵerapo tsiku ndi tsiku, kukadya zopereka zonsezo.

14Ansembe aja atachoka, mfumu idapereka chakudya kwa Belo. Tsono Daniele adalamula anyamata ake kuti atenge phulusa nkuliwaza pansi m'nyumba yonse yachipembedzoyo. Mfumu yokha ndiyo idaaona pamene anyamatawo ankachita zimenezo. Atamaliza, anyamatawo adatuluka m'nyumba yachipembedzo ija, natseka chitseko. Adasindikizapo chidindo cha mfumu nachoka.

15Pakati pa usiku, ansembe aja, akazi ao ndi ana, onse adakaloŵa m'nyumba yachipembedzo ija, nkudya ndi kumwa zonse monga ankachitira nthaŵi zonse.

16M'maŵa mwake, mfumu idabwera pamodzi ndi Daniele.

17Mfumu idafunsa kuti, “Daniele, kodi zidindo zija zikali zosasweka?” Daniele adayankha kuti, “Inde, amfumu, nzosasweka.”

18Mfumu idatsekula chitseko, nkuwona kuti patebulo paja pali mbee, popanda chilichonse. Pamenepo idafuula kuti, “Mutamandike, inu Belo. Ndinu wosanyenga.”

19Koma Daniele adangoseka, naletsa mfumu kuti isaloŵe. Adati, “Amfumu, tayang'anani pansipa, kodi mapaziŵa ndi a yani?”

20Mfumu idayankha kuti, “Ndikuwonadi mapazi a anthu aamuna, a anthu aakazi ndi a ana.”

21Apo mfumuyo idapsa mtima zedi nigwira ansembe onse aja, akazi ao ndi ana ao omwe. Kenaka ansembewo adaonetsa mfumuyo khomo lobisika limene ankaloŵera pokadya zonse zapatebulo zija.

22Pambuyo pake mfumu idaŵapha onsewo, nipereka Belo kwa Daniele. Danieleyo adamuwononga Beloyo pamodzi ndi nyumba yake.

Daniele apha Chinjoka

23Panali chinjoka chachikulu chimene anthu a ku Babiloni ankachipembedza.

24Tsiku lina mfumu idauza Daniele kuti, “Sunganene kuti mulungu uyu si wamoyo. Mpembedze tsono.”

25Daniele adayankha kuti, “Ndidzapembedza Ambuye Mulungu wanga chifukwa choti Iyeyo ndiye Mulungu wamoyo.

26Koma mutandilola amfumu, chinjokachi ine nkuchipha, popanda lupanga kapena ndodo.” Mfumu idayankha kuti, “Chabwino, ndakulola.”

27Tsono Daniele adatenga phula, mafuta ndi tsitsi naziphika zonse pamodzi. Adapanga nazo makeke nkukadyetsa chinjoka chija. Chinjokacho chitadya, chidaphulika. Tsono Daniele adati, “Tachiwonani chinthu chija mwakhala mukupembedzachi!”

28Anthu a ku Babiloni atamva zimenezi, adakwiya kwambiri, nkuchita upo woukira mfumu. Adayamba kufuula kuti, “Mfumu yasanduka Myuda. Yaphwanya Belo, yapha chinjoka chija nkuphanso ansembe onse ndi lupanga.”

29Tsono adapita kwa mfumu nakaiwuza kuti, “Amfumu, tipatseni Danieleyu. Mukakana, ndiye kuti tikuphani inuyo pamodzi ndi banja lanu.”

30Mfumu poona kuti aipanikiza, idamperekadi Daniele kwa iwo.

31Anthuwo adamponya Daniele m'phanga la mikango. Adakhala m'menemo masiku asanu ndi limodzi.

32M'phangamo munali mikango isanu ndi iŵiri. Tsiku lililonse ankaiponyera anthu aŵiri ndi nkhosa ziŵiri kuti idye. Koma ulendo uno adaayamba aigoneka ndi njala, kuti idzamudyedi Danieleyo.

Daniele ampulumutsa m'phanga la mikango

33Nthaŵi imeneyo nkuti mneneri Habakuku akukhala ku Yudeya. Tsiku lina adaphika chipere, nkunyenyeramo buledi. Adanyamuka kunka nacho ku munda chakudyacho, kukapatsa anthu okolola.

34Koma Mngelo wa Ambuye adauza Habakuku kuti, “Chakudyachi pita nacho ku Babiloni, ukapatse Daniele, amene ali m'phanga la mikango.”

35Habakuku adayankha kuti, “Bwana, ine ku Babiloni sindinapiteko. Sindidziŵa kumene kuli phanga la mikango.”

36Pomwepo Mngelo wa Ambuyeyo adamnyamula Habakuku pomugwira tsitsi lakumutu, napita naye ku Babiloni ndi liŵiro la mphepo, nkumuika pafupi ndi phanga la mikango lija.

37Habakuku adafuula kuti, “Daniele, Daniele, idya chakudya chimene Mulungu wakutumizira.”

38Daniele adati, “Inu Mulungu, mwandikumbukira. Anthu amene amakukondani simuŵasiya.”

39Tsono adaimirira naadya. Pambuyo pake mngelo wa Ambuye uja adamtenganso Habakuku kubwerera naye kwao.

40Pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, mfumu idapita kuphanga kuja kukalira Daniele. Itafika, posuzumiramo, idangoona Daniele ali phee!

41Pamenepo mfumu idafuula kuti, “Inu Ambuye, Mulungu wa Daniele, ndinudi wamkulu. Palibe Mulungu wina koma Inu nokha.”

42Pambuyo pake mfumu idamtulutsa Danieleyo m'phangamo, ndipo anthu amene ankafuna kuwononga Daniele aja, adaŵaponya m'phanga momwemo. Pompo mikango ija idaŵadya, mfumu ikuwona.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help