1Anthu okhuta vinyo amanyodola anzao,
omwa zaukali amautsa phokoso.
Aliyense wosokera nazo zimenezi ndi wopanda nzeru.
2Mkwiyo woopsa wa mfumu uli ngati kubangula kwa mkango.
Amene amauputa dala mkwiyowo, amataya moyo wake.
3Nchaulemu kwa munthu kumalewa mikangano,
koma aliyense wopusa amakonda kulongolola.
4Waulesi sasoseratu pa nthaŵi yoyenera.
Pa nthaŵi yokolola adzafunafuna dzinthu,
koma sadzapeza kanthu.
5Zolinga za mtima wa munthu zili ngati madzi ozama,
ndi munthu wanzeru yekha angazitulutse.
6Anthu ambiri amalankhula za kukhulupirika kwao,
koma ndani angathe kumpeza munthu wokhulupirika
kwenikweni?
7Munthu abwino amakhala mwachilungamo,
ndipo Mulungu amadalitsa ana amene amatsata njira yake.
8Pamene mfumu ikhala pa mpando wake wa chiweruzo,
imazindikira ndi maso chabe anthu onse amene ali oipa.
9Ndani angathe kunena kuti,
“Ine ndauyeretsa mtima wanga,
ndilibenso tchimo lililonse.”
10Masikelo ndi miyeso ina yoyesera zinthu
zikakhala zonyenga,
zonsezo zimamunyansa Chauta.
11Ngakhale mwana yemwe amadziŵika ndi ntchito zake,
kuti zimene amachitazo ndi zabwino ndi zolungama.
12Makutu amene timamvera ndiponso
maso amene timapenyera,
zonsezo adazilenga ndi Chauta.
13Usakondetse tulo, kuwopa kuti ungagwe mu umphaŵi.
Khala maso, ndipo udzakhala ndi chakudya chambiri.
14Munthu akamagula kumene chinthu amati,
“Nchoipa, nchoipa,”
koma atagula nkuchokapo, amayamba kudzitama.
15Pali golide ndi miyala yambirimbiri yamtengowapatali,
koma mau olankhula zanzeru
ali ndi mtengo woposa zonsezo.
16Munthu amene waperekera mlendo chikole,
umlande chovala chake,
chimenecho chikhale chigwiriro chako,
chifukwa chakuti waperekera chikole mlendo wosadziŵika.
17Chakudya chochipeza monyenga chimamkomera munthu,
koma pambuyo pake chimakasanduka ngati lubwe
m'kamwa mwake.
18Ukakonzekera kuchita zinthu, uziyamba wafunsa.
Usanamenye nkhondo, uyambe wapempha malangizo oyenera.
19Amene amanka nachita ugogodi, amaulula zinsinsi.
Nchifukwa chake usamagwirizane naye wolankhula zopusayo.
20Wina akatemberera bambo wake kapena mai wake,
moyo wake udzatha ngati nyale yozima
mu mdima wandiweyani.
21Choloŵa chopata mofulumira poyamba,
sichidzakhala dalitso pambuyo pake.
22Usamanena kuti, “Ndidzabwezera choipa ndine.”
Udikire Chauta, ndipo adzakuthandiza.
23Miyeso yosintha imanyansa Chauta,
masikelo onyenga ndi oipanso.
24Mayendedwe a munthu amaŵalamula ndi Chauta:
Tsono munthu angadziŵe bwanji njira yake?
25Ndi msampha kwa munthu kupereka chinthu kwa Chauta
mosaganiza bwino,
chifukwa mwina atha kusintha maganizo atalumbira kale.
26Mfumu yanzeru imazindikira oipa,
ndipo imaŵalanga mopanda chisoni.
27Mpweya wa munthu uli ngati nyale ya Chauta,
nyaleyo imafufuza ziwalo zake zonse zam'kati.
28Kukoma mtima ndi kukhulupirika ndizo zimasunga mfumu,
chilungamo ndiye chimalimbitsa ufumu wake.
29Kukongola kwa achinyamata kwagona pa nyonga zao,
koma ulemerero wa nkhalamba wagona pa imvi zao.
30Mikwingwirima ndiye mankhwala ochotsa zoipa.
Mikwapulo imachiza zam'katikati mwa munthu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.