1Usakhumbe kukhala ndi ana ambiri achabechabe,
kapena kukondwera nawo ana osaopa Mulungu.
2Angachuluke bwanji, usakondwere nawo,
koma pokhapokha ngati amaopa Ambuye.
3Usakhulupirire kutalika kwa moyo wao,
usadalire kuchuluka kwao.
Ndi bwino kukhala ndi mwana mmodzi yekha
koma woopa Mulungu,
kupambana kukhala nawo 1,000 oipa.
Ndi bwino kufa opanda ana
kupambana kukhala ndi ana osasamala za Mulungu.
4Chifukwa cha munthu mmodzi yekha woopa Mulungu
mzinda ukhoza kudzaza ndi anthu.
Koma chifukwa cha chigulu cha anthu osatsata Malamulo,
mzinda ukhoza kuwonongeka.
5Nthaŵi zambiri ndaona zinthu zoterezi
ndipo ndamva zina zambiri zodabwitsa kupambana zimenezi.
6M'gulu la anthu ochimwa moto udzabuka,
ndipo mkwiyo udzayakira anthu a mtundu waupandu.
7 Gen. 6.4; Lun. 14.6 Mulungu sadakhululukire ziphona zakale
zimene zinkanyadira mphamvu zao ndi kuchita zaupandu.
8Sadaleke kuŵalanga anthu oyandikana ndi Loti aja,
chipongwe chao chidamnyansa Mulungu.
9Sadaŵachitire chifundo anthu oyenera kutayikawo,
anthu amene ankanyadira machimo ao.
10Adaŵateronso anthu oyenda pansi 600,000 aja
amene adasonkhana mwaupandu atakhuta mwano.
11Ngakhale atakhala wokanika mmodzi yekha,
zingakhale zodabwitsa atapanda kulangidwa.
Paja Ambuye ali ndi chifundo,
komanso ukali ngwao.
Amaonetsa mphamvu pokhululuka,
komanso amaonetsa mkwiyo.
12Chifundo chao nchachikulu,
komanso amalanga koopsa.
Amaweruza munthu potsata ntchito zake.
13Salola kuti wochimwa athaŵe ndi phindu lake loipa.
Kupirira kwa munthu woopa Mulungu sikudzapita
pachabe.
14Ambuye amalipira ntchito iliyonse yachifundo,
ndipo munthu aliyense amamchitira potsata ntchito zake.
15Mulungu adaumitsa mtima Farao kuti asamzindikire,
kuti ntchito za Mulungu zidziŵike pa dziko lapansi.
16Amachitira chifundo zolengedwa zake zonse,
ndiye amene adagaŵa kuŵala ndi mdima pakati pa anthu.
Chilango sichilephera kufika17Usanene kuti, “Ndiŵabisalira Ambuye.
Nanga ndani kumwambako angathe kundikumbukira?
Pakati pa anthu ambiri chotere sangathe kundizindikira.
Kodi ine ndine chiyani pakati pa zolengedwa zonse?
18Onani mlengalenga, thambo la kumwamba, phompho ndi dziko lapansi,
zonsezi zimagwedezeka akamabwera Ambuye.
19Mapiri ndi maziko a dziko lapansi
nawonso amanjenjemera, Ambuye akaŵayang'ana.
20Koma ndani amaganizako za zimenezi,
ndipo ndani amayesa kumvetsa njira za Ambuye?
21Monga namondwe amafikira anthu modzidzimutsa,
momwemonso ntchito zambiri za Ambuye zimachitika mobisika.
22Ndani angasimbe za ntchito zolungama za Ambuye?
Ndani angaziyembekezere?
Ndipotu chipangano chake chili kutali.”
23Ameneŵa ndiwo maganizo a munthu wopanda nzeru,
malingaliro opusa a munthu wosokonezeka.
Za munthu pakati pa zolengedwa24Mwana wanga, undimvere ndipo uphunzire nzeru.
Mvetsetsa bwino zimene ndikunena!
25Ndidzakuphunzitsa mwambo mosamala,
ndi kukuuza nzeru mosaphonya.
26Ambuye adalenga zinthu poyambayamba,
ndipo atazilenga, adazipatsa malire ake.
27Adazilongosola dwakedwake mpaka muyaya,
kuyambira pa chiyambi mpaka nthaŵi yakutsogolo.
Zonsezo sizimva njala kapena kutopa,
ndipo sizisiya ntchito zimene adazipatsa.
28Palibe chimene chimaombana ndi chinzake,
ndipo sizidzaleka kumvera lamulo la Ambuye.
29Tsono Ambuye adayang'ana dziko lapansi,
ndipo adalidzaza ndi zinthu zao zabwino.
30Adadzaza nthaka yonse ndi zolengedwa zamoyo
wa mitundu yonse,
ndipo zonsezo zidzabwerera ku nthaka komweko.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.