1Chauta adandiwuza kuti, “Pita ku nyumba ya mfumu ya ku Yuda, ukaiwuze kuti,
2‘Iwe mfumu ya ku Yuda, imva mau a Chauta. Imva iwe amene umakhala pa mpando waufumu wa Davide, iweyo pamodzi ndi atumiki ako ndiponso anthu ako amene amaloŵera pa zipata izi.
3Chautatu akuti uziweruza molungama ndi mosakondera. Munthu amene adambera zake uzimpulumutsa kwa womsautsa. Usavutitse mlendo, mwana wamasiye kapena mkazi wamasiye. Usakhetse magazi a anthu osachimwa pa malo ano.
4Ndithu, ukamadzamvera mau aŵa, ndiye kuti mafumu okhala pa mpando waufumu wa Davide adzapitirirabe kumalamulira. Azidzaloŵera pa zipata izi za ku nyumba ya mfumu, atakwera pa magaleta ndi pa akavalo, iwowo pamodzi ndi atumiki ao ndi anthu ao.
5 mwana wa Yehoyakimu mfumu ya ku Yuda, ngakhale ukadakhala ngati mphete ya ku dzanja langa lamanja, ndikadakuvula nkukutaya.
25Ndidzakupereka kwa anthu ofuna kukupha, amene umaŵaopa, ndiye kuti kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni ndi anthu ake.
26Ndidzakupititsa ku dziko lina pamodzi ndi mai wako amene adakubala. Simudabadwire kumeneko, komabe nonsenu mudzafera kumeneko.
27Simudzabwereranso kudziko kumene mudzafuna kubwerera.”
28Ine ndidati,
“Kodi ndiye kuti Yehoyakiniyu
wakhala ngati mbiya yonyozeka, yosweka,
chinthu chimene anthu sakuchisamala?
Nanga chifukwa chiyani iyeyu ndi ana ake akuŵachotsa
ndi kuŵaponya ku dziko losadziŵika konse?”
29Iwe dziko, iwe dziko, iwe dziko,
imva mau a Chauta.
30Chauta akuti,
“Munthu ameneyu mumtenge ngati wopanda ana,
munthu amene sadzakhoza pa moyo wake.
Ndithu, palibe ndi mmodzi yemwe mwa zidzukulu zake
amene adzakhale pa mpando waufumu wa Davide
ndi kudzalamuliranso Yuda.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.