Chiv. 3 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Kalata yolembera mpingo wa ku Sardi

1“Mtsogoleri wa mpingo wa ku Sardi umlembere kuti, Naŵa mau ochokera kwa amene amalamulira mizimu ya Mulungu isanu ndi iŵiri ija, ndi nyenyezi zisanu ndi ziŵiri zija zili m'manja mwakezi. Akuti: Ntchito zanu zonse ndikuzidziŵa. Ndikudziŵa kuti muli ndi mbiri yoti ndinu amoyo, chonsecho ndinu akufa.

2Dzukani, ndi kulimbitsa zokutsalirani zimene zili pafupi kutha. Pakuti ndikuwona kuti ntchito zanu sizili zangwiro konse pamaso pa Mulungu wanga.

3Mt. 24.43, 44; Lk. 12.39, 40; Chiv. 16.15Tsono kumbukirani zimene mudaphunzira, ndi zimene mudamva. Muzisunge ndipo mutembenuke mtima. Mukapanda kudzuka, ndidzabwera mwadzidzidzi ngati mbala, mwakuti nthaŵi imene ndidzakupezeniyo simudzaidziŵa.

4Koma alipo angapo pakati panu ku Sardi amene sadadetse zovala zao. Iwowo adzayenda nane pamodzi atavala zoyera, pakuti ndi oyeneradi.

5Eks. 32.32, 33; Mas. 69.28; Chiv. 20.12; Mt. 10.32; Lk. 12.8Motero aliyense amene adzapambane, adzamuvekanso zovala zoyera. Dzina lake sindidzalifafaniza m'buku la amoyo, ndipo ndidzamchitira umboni pamaso pa Atate anga, ndi pamaso pa angelo ao.

6“Amene ali ndi makutu, amvetsetse zimene Mzimu Woyera akuuza mipingozi.”

Kalata yolembera mpingo wa ku Filadelfiya

7 Yes. 22.22; Yob. 12.14 “Mtsogoleri wa mpingo wa ku Filadelfiya umlembere kuti, Naŵa mau ochokera kwa Iye amene ali woyera ndi woona, amene ali ndi kiyi yaulamuliro ya Mfumu Davide. Uja amene amati akatsekula, palibe wotinso nkutseka, ndipo akatseka, palibe wotinso nkutsekula.

8Akuti: Ntchito zanu zonse ndikuzidziŵa. Ndakutsekulirani pa khomo, ndipo palibe amene angatsekepo. Ndikudziŵa kuti mphamvu zanu nzochepa, komabe mwasunga mau anga, ndipo simudandikane.

9Yes. 49.23; 60.14; Yes. 43.4Alipo ena a mpingo wa Satana, amene sali Ayuda, koma amanama kuti ndi Ayuda. Iwoŵa ndidzaŵabweretsa kwa inu kuti adzadzigwetse kumapazi kwanu. Pamenepo adzadziŵa kuti ndimakukondani.

10Popeza kuti mwasunga mau anga oti mupirire mosatepatepa, Inenso ndidzakusungani pa nthaŵi yamayeso imene ilikudza m'dziko lonse lapansi, kuti anthu onse okhalamo adzayesedwe.

11Ndikubwera posachedwa. Gwiritsani chimene muli nacho, kuti wina angakulandeni mphotho yanu.

12Chiv. 21.2; Yes. 62.2; 65.15Amene adzapambane, ndidzamsandutsa mzati wokhazikika m'Nyumba ya Mulungu wanga. Sadzatulukamonso, ndipo pa iye ndidzalemba dzina la Mulungu wanga, ndi la mzinda wa Mulungu wanga. Mzindawo ndi Yerusalemu watsopano, wotsika Kumwamba kuchokera kwa Mulungu wanga. Pa iye ndidzalembanso dzina langa latsopano.

13“Amene ali ndi makutu, amvetsetse zimene Mzimu Woyera akuuza mipingozi.”

Kalata yolembera mpingo wa ku Laodikea

14 Miy. 8.22 “Mtsogoleri wa mpingo wa ku Laodikea umlembere kuti, Naŵa mau ochokera kwa Iye amene amatchedwa Amen uja, amene ali mboni yokhulupirika ndi yoona, ndiponso gwero la zolengedwa zonse za Mulungu.

15Akuti: Ntchito zanu zonse ndikuzidziŵa. Sindinu ozizira, sindinunso otentha. Bwenzi zili bwino mukadakhala ozizira kapena otentha.

16Koma popeza kuti ndinu ofunda chabe, osati otentha kapena ozizira, ndidzakusanzani.

17Paja inu mumati, ‘Ndife olemera, ndife achuma, sitisoŵa kanthu;’ osadziŵa kuti ndinu ovutika, ochititsa chifundo, amphaŵi, akhungu ndi amaliseche.

18Choncho ndikukulangizani kuti mugule kwa Ine golide woyeretsedwa ndi moto, kuti mukhale olemera. Mugulenso kwa Ine zovala zoyera, kuti muvale ndi kubisa maliseche anu ochititsa manyaziwo. Ndiponso mugule kwa Ine mankhwala a maso kuti mupenye.

19Miy. 3.12; Ahe. 12.6Onse amene ndimaŵakonda, ndimaŵadzudzula ndi kuŵalanga motero. Tsono chitani khama, mutembenuke mtima.

20Ndaima pakhomo pano, ndipo ndikugogoda. Wina akamva mau anga, nkutsekula chitseko, ndiloŵa, ndipo Ine ndi iye tidyera limodzi.

21Amene adzapambane, ndidzamlola kukhala nane pamodzi pa mpando wanga wachifumu, monga momwe ndidachitira Ineyo: ndidapambana, ndipo ndikukhala pamodzi ndi Atate anga pa mpando wao wachifumu.

22“Amene ali ndi makutu, amvetsetse zimene Mzimu Woyera akuuza mipingozi.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help