Eks. 24 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Kusindikizidwa kwa chipangano

1Mulungu adauza Mose kuti, “Bwera kwa Ine kuno ku phiri pamodzi ndi Aroni, Nadabu, Abihu ndiponso atsogoleri a Aisraele 70. Tsono mundipembedze Ine muli chapatali ndithu.

2Mose yekha ndiye andiyandikire, koma enawo asafike pafupi. Anthu ena onse nawonso asabwere ndi Moseyo.”

3Mose adapita kukauza anthu mau ndi malangizo onse amene Chauta adamuuza. Ndipo anthu onse adayankha kuti, “Tidzachita zonse zimene Chauta wanena.”

4Apo Mose adalemba mau onse a Chauta. Ndipo adadzuka m'maŵa ndithu nayamba kumanga guwa patsinde pa phiri. Kenaka adaimiritsa miyala khumi ndi iŵiri ya mafuko khumi ndi aŵiri a Aisraele.

5Tsono adatuma Aisraele achinyamata kuti iwoŵa apereke nsembe zopsereza, ndi kupha ng'ombe kuti apereke nsembe zamtendere kwa Chauta.

6Mose adatengako theka la magazi, naŵathira m'mbale, ndipo magazi otsala adawaza pa guwa.

7Pambuyo pake adatenga buku lachipangano, naŵaŵerengera momveka anthuwo. Tsono anthuwo adati, “Tidzachita zonse zimene Chauta walamula. Tidzamumvera Iyeyo.”

8Mt. 26.28; Mk. 14.24; Lk. 22.20; 1Ako. 11.25; Ahe. 10.29; Ahe. 9.19, 20 Apo Mose adatenga magazi am'mbale aja, nawaza anthuwo, ndipo adati, “Magazi ameneŵa ndiwo amene akutsimikiza chipangano chimene Chauta wapangana nanu pakukupatsani mau onseŵa.”

9Tsono Mose, Aroni, Nadabu ndi Abihu ndiponso anthu 70 mwa atsogoleri aja a Aisraele, adakwera phiri,

10ndipo adaonana ndi Mulungu wa Aisraele. Pansi pa mapazi ake panali china chooneka ngati mseu wopangidwa ndi mwala wa safiro woyalidwa bwino, wa maonekedwe onga thambo.

11Mulungu sadaŵaononge atsogoleri a Aisraelewo. Iwowo adampenyadi Mulungu, kenaka adadya ndi kumwa.

Mose pa phiri la Sinai

12Chauta adauza Mose kuti, “Bwera kwa Ine kuphiri kuno, ndipo udikire konkuno. Ndidzakupatsa miyala imene ndalembapo malamulo, kuti ndiphunzitse anthu.”

13Apo Mose adanyamuka pamodzi ndi mtumiki wake Yoswa, ndipo Moseyo adakwera phiri la Mulungu.

14Iyeyo anali atauza atsogoleri aja kuti, “Batiyembekezani pano, mpaka tidzakupezeni. Aroni ndi Huri muli nawo pompano. Amene akhale ndi milandu, apite kwa iwowo.”

15Tsono Mose adakwera phiri, ndipo phirilo lidaphimbidwa ndi mtambo.

16Ulemerero wa Chauta udatsikira pa phiri la Sinai, ndipo lidaphimbidwa ndi mtambo masiku asanu ndi limodzi. Pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri Chauta adaitana Mose m'kati mwa mtambomo.

17Kwa Aisraele aja, ulemerero wa Chauta uja unkaoneka ngati malaŵi a moto pa phiri.

18Deut. 9.9 Mose adakaloŵa mumtambomo mpaka kukafika pamwamba pa phiri. Adakhala kumeneko masiku makumi anai, usana ndi usiku.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help