1 Ate. 3 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Ntc. 17.15 Nchifukwa chake pamene sitidathenso kupirira, tidalolera kutsalira tokha ku Atene.

2Choncho tidatuma Timoteo, mbale wathu ndi mnzathu wogwira naye ntchito ya Mulungu yolalika Uthenga Wabwino wa Khristu. Tidamtuma kuti adzakulimbitseni mtima ndi kukukhazikitsani m'chikhulupiriro chanu,

3kuwopa kuti wina aliyense mwa inu angagwedezeke chifukwa cha mazunzoŵa. Mukudziŵa nokha kuti Mulungu ndiye adalola kuti zimenezi zitigwere.

4Pajatu pamene tinali pamodzi nanu, tidaakuuziranitu kuti tidzayenera kuzunzidwa. Ndipo monga mukudziŵa, zimenezi zidachitikadi.

5Nchifukwa chake, pamene sindidathenso kupirira, ndidatuma Timoteo kuti adzaone m'mene chiliri chikhulupiriro chanu. Pakuti ndinkaopa kuti kapena Satana, Wonyenga uja, adakunyengani, ndipo kuti ntchito zathu zonse pakati panupo zidangopita pachabe.

6 Ntc. 18.5 Koma tsopano Timoteo wabwerako kuchokera kwanuko, ndipo watisimbira mbiri yokoma ya chikhulupiriro chanu ndi chikondi chanu. Watiwuzanso kuti masiku onse mumatikumbukira mokondwa, ndipo kuti mumalakalaka kutiwona ife, monga momwe ifeyo timafunitsitsira kukuwonaninso inuyo.

7Motero abale, pakati pa masautso ndi mazunzo athu onse, chikhulupiriro chanu chatithuzitsa mtima.

8Takhalanso ndi moyo tsopano pakuti mukulimbika pa chikhristu chanu.

9Nanga tingathe bwanji kuyamika Mulungu mokwanira chifukwa cha inu, poona chimwemwe chonse chimene tili nacho pamaso pa Mulungu wathu?

10Ndi mtima wonse timapemphera usana ndi usiku kuti tiwonane nanunso maso ndi maso, kuti tikakwaniritse zimene zikusoŵa pakuwonetsa chikhulupiriro chanu.

11Tikupempha kuti Mulungu Atate athu mwini, ndi Ambuye athu Yesu atikonzere njira yabwino kuti tidzafike kwanuko.

12Ambuye akulitsirekulitsire kukondana kwanu, ndiponso chikondi chanu cha pa anthu onse, monga momwe chikondi chathu cha pa inu chikukulirakulira.

13Motero Iye adzalimbitsa mitima yanu kuti idzakhale yangwiro ndi yoyera pamaso pa Mulungu Atate athu, pamene Ambuye Yesu adzabwerenso pamodzi ndi oyera ake onse.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help