1Kusunga Malamulo kuli chimodzimodzi kupereka
nsembe zambiri.
Kusamala Malamulo ndiye ngati kupereka nsembe
zothokozera.
2Kubwezera zachifundo mothokoza kuli ngati
kupereka nsembe zaufa.
Pothandiza wosauka, umachita ngati ukupereka
nsembe yoyamikira.
3Kuleka zoipa kumakondweretsa Ambuye,
kusiya zochimwa ndiye nsembe yopepesera machimo.
4Usabwere pamaso pa Ambuye chimanjamanja.
5Nsembe zonsezi ziyenera kuperekedwa chifukwa
Malamulo akutero.
6Munthu wolungama akamapereka nsembe ku guwa,
fungo lake labwino limafika kwa Mulungu Wopambanazonse.
7Nsembe za munthu wolungama Ambuye amazilandira,
ndipo sadzaziiŵala.
8Uzikonda kulemekeza Ambuye ndi mtima wachifundo,
ndipo usaleke kupereka kwa Ambuye zipatso zako
zoyamba kucha.
9 2Ako. 9.7 Uzipereka mphatso zako ndi chimwemwe,
ndipo uzisangalala popereka chachikhumi chako.
10Uzipatsa Mulungu Wopambanazonse monga momwe adakupatsira,
uzipereka mwaufulu monga ungathere.
11Paja Ambuye amapereka mphotho mwaufulu;
adzakuchulukitsira kasanunkaŵiri.
Za kulungama kwa Mulungu12Usayese kupereka chiphuphu kwa Ambuye,
chifukwa sadzachilandira.
Ndipo usadalire nsembe yopanda chilungamo,
chifukwa Ambuye ndiwo muweruzi,
muweruzi wake wopanda tsankho.
13Saonetsa kukondera poweruza wosauka,
amamvera pemphero la amene anzake adamulakwira.
14Sanyozera pempho la mwana wamasiye
kapena madandaulo a mkazi wamasiye.
15Suja misozi ya mkazi wamasiye imatsika pamasaya pake,
akamaneneza munthu amene adamliritsa?
16Uzitumikira Ambuye mokhulupirika,
ndipo Iwowo adzakulandira.
Pamenepo mapemphero ako akafika kumwamba.
17Pemphero la munthu wodzichepetsa limabzola mitambo,
ndipo mtima wake sudzakhazikika mpaka Ambuye
atamva pempherolo.
Sadzaleka kupempha mpaka Wopambanazonse atamuyendera,
ndi kuchitira chilungamo anthu abwino
pakuweruza moona.
18Ambuye sadzachedwa
ndipo sadzapirira anthu ochimwa,
mpaka atadzaphwanya misana ya anthu opanda chisoni,
ndi kulipsira mitundu ya akunja;
mpaka ataonongeratu anthu achipongwe
ndi kuthyola mphamvu za anthu osalungama;
19mpaka aliyense atampatsa molingana ndi zochita zake,
ndi kulipira ntchito zakezo potsata zolinga
za mumtima mwake;
mpaka atagamula mlandu wa anthu ake,
ndi kuŵasangalatsa ndi chifundo chao.
20Pa nthaŵi ya mavuto chifundo cha Ambuye
nchokondweretsa,
ngati mitambo yamvula pa nthaŵi yachilala.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.