1Dariusi, mbadwa ya ku Medi, mwana wa Ahasuwero, adaloŵa ufumu wolamulira dziko la Babiloni.
2Tsono pa chaka choyamba cha ufumu wake, ine Daniele, poŵerenga mabuku oyera, ndidapeza kuti padzapita zaka makumi asanu ndi aŵiri Yerusalemu akali bwinja. Izi ndiye zimene Chauta adaauza mneneri Yeremiya.
3Pamenepo ndidayang'ana kwa Ambuye Mulungu ndilikupemphera ndi kupempha, ndilikusala chakudya nditavala chiguduli, ndiponso nditadzola phulusa.
4Ndidapemphera kwa Chauta, Mulungu wanga, ndi kuvomera kuti tidachimwa, ndidati, “Inu Ambuye, Mulungu wamkulu ndi woopsa, mumasunga mokhulupirika chipangano chanu ndi anthu amene amakukondani ndi kutsata malamulo anu.
5Tachimwa ife, tachita zoipa ndi zolakwa. Takuukirani posiya malamulo anu ndi malangizo anu.
6Sitidamvere aneneri, atumiki anu, amene ankalankhula m'dzina lanu kwa mafumu athu, kwa akalonga athu ndi kwa anthu onse a m'dziko.
7Inu Ambuye, ndinu olungama, koma mpaka pano manyazi atigwera ife anthu a ku Yuda, mbadwa za ku Yerusalemu, ndi anthu onse a ku Israele, apafupi ndi akutali, ku maiko onse kumene mudatipirikitsira, chifukwa chakuti takuchimwirani.
8Inu Ambuye, manyazi akhale pa ife ndi mafumu athu, pa akalonga athu ndi makolo athu, chifukwa cha zaupandu zimene tidakuchitani.
9Ambuye, Mulungu wathu, ndinu achifundo ndiponso okhululuka, ngakhale tidakupandukirani.
10Ife sitidamvere mau anu, Inu Chauta Mulungu wathu, sitidatsate malamulo anu amene mudatipatsa kudzera mwa aneneri atumiki anu.
11Aisraele onse adachimwira malamulo anu, ndipo adapatuka, nakana kumvera mau anu. Motero mau otemberera ndi olumbira amene adalembedwa m'Malamulo a Mose, mtumiki wa Mulungu, atigwera ife chifukwa choti tidakuchimwirani.
12Mwachitadi zimene munkanena zodzudzula ife, ndiponso zodzudzula olamulira athu. Mwatigwetsera tsoka loopsa ifeyo ndi Yerusalemu, tsoka limene silidachitikepo nkale lonse pa dziko lonse lapansi.
13Monga zidaalembedweratu m'Malamulo a Mose, tsoka lonse latigweradi. Komabe sitidayese kukupembani, Inu Chauta, Mulungu wathu, kuti mutikomere mtima. Sitidalape zolakwa zathu, sitidasamale mau anu oona.
14Nchifukwa chake Inu Chauta mudakonzekera zoti mutigwetsere tsoka limeneli, ndiye latigweradi. Inu Chauta, Mulungu wathu, ndinu olungama pa zonse zimene mwachita, komabe ifeyo sitidamvere mau anu.
15“Inu Ambuye, Mulungu wathu, mudatulutsa anthu anu ku Ejipito ndi dzanja lanu lamphamvu, ndipo dzina lanu nlotchuka mpaka pano. Koma ife tachimwa, tachita zoipa.
16Inu Ambuye, malinga ndi mtima wanu wolungama, tikupempha kuti mkwiyo wanu ndi ukali wanu zichoke pa mzinda wa Yerusalemu, phiri lanu loyera. Anthu a m'maiko ozunguliraŵa amanyoza Yerusalemu ndi anthu anu, chifukwa cha machimo athu ndi zoipa za makolo athu.
17Nchifukwa chake tsono, Inu Mulungu wathu, imvani pemphero la mtumiki wanu ndiponso mau ake opemba. Tsono kuti onse akudziŵeni kuti ndinu Ambuye, muyang'ane ndi chifundo malo anu oyera amene adasanduka bwinja.
18Inu Mulungu wanga, mutchere khutu kuti mumve mau anga. Mutsekule maso anu kuti mupenye mabwinja athu ndi mzinda umene umadziŵika ndi dzina lanu. Tikupemphera kwa Inu chifukwa Inuyo ndinu achifundo, osati chifukwa choti ifeyo ndife olungama ai.
19Inu Chauta, imvani mau athu. Inu Chauta, tikhululukireni. Inu Chauta, mutimvere, ndipo muchitepo kanthu. Kuti anthu akudziŵeni kuti ndinu Mulungu, musachedwe Inu Mulungu wanga, pakuti mzinda wanu ndiponso anthu anu amadziŵika ndi dzina lanu.”
Mngelo Gabriele amasulira ulosi20Ndinkalankhula ndi kupemphera ndi kuvomera machimo anga ndi machimo a anthu anga Aisraele. Ndinkapemba pamaso pa Chauta, Mulungu wanga, pokumbukira phiri loyera la Mulungu.
21Ndikupemphera choncho, mngelo Gabriele, amene adaandiwonekerapo kale pamene ndinkaona zinthu m'masomphenya, adabwera kwa ine chouluka mwaliŵiro. Inali nthaŵi yopereka nsembe yamadzulo.
22Iye adadzandiwuza kuti, “Iwe Daniele, ndabwera tsopano kuti ndikupatse nzeru, uzimvetsa zinthu.
23Pamene unkayamba kupemba kwako, Mulungu adaayankha, ndiye ine ndabwera kudzakuuza yankholo, poti Mulunguyo amakukonda kwambiri. Nchifukwa chake uŵamvetsetse bwino mauwo, pamene ndikufotokoza zinthu zimene udaziwona m'masomphenya zija.
24“Zaka makumi asanu ndi aŵiri kuchulukitsa kasanunkaŵiri zidaikidwa kuti anthu ako ndi mzinda wako woyera aleke zaupandu ndi kusiya machimo ndi zolakwa. Adzapepesera machimo ndipo chilungamo chamuyaya chidzafika. Tsono zimene udaziwona m'masomphenya zija ndiponso zimene zidalosedwa zidzachitikadi, ndipo malo opatulika kwambiri adzakhazikitsidwa.
25Udziŵe tsono ndipo umvetse kuti kuchokera nthaŵi imene mau adamveka akuti Yerusalemu akonzedwenso ndi kumangidwa, mpaka pamene kalonga wodzozedwa adzafike, padzapita zaka zisanu ndi ziŵiri kuchulukitsa kasanunkaŵiri. Pamenepo mzindawo udzamangidwanso uli ndi mabwalo ndi ngalande zoteteza, ndipo udzakhalako zaka 62 kuchulukitsa kasanunkaŵiri, koma padzaoneka mavuto pa nthaŵi imeneyo.
26Pakutha pa zaka zimenezi wodzozedwa uja adzaphedwa mopanda chilungamo, koma osati chifukwa cha iyeyo. Gulu lankhondo la mtsogoleri wamphamvu amene adzabwere lidzaononga mzindawo pamodzi ndi Nyumba ya Mulungu. Tsono kutha kwake kudzabwera ngati chigumula, ndipo kudzabweretsa chiwonongeko ndi nkhondo, zimene Mulungu adakonza.
27Mtsogoleri ameneyo adzapangana ndi anthu ambiri chipangano cholimba kwa zaka zisanu ndi ziŵiri. Patapita theka la nthaŵi imeneyi, adzaletsa kupereka nsembe ndi zopereka zina. Chonyansa chosakaza chija adzachiika pamwamba, ndipo chidzakhalapo mpaka wochita zimenezi adzalangidwe ndi chiwonongeko chimene Mulungu adamkonzera.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.