1Tamandani Mulungu ndi chimwemwe mokweza mau,
inu anthu onse a pa dziko lapansi.
2Imbani nyimbo zoyamika dzina lake laulemerero,
mumtamande mwaulemu.
3Muuzeni Mulungu kuti,
“Ntchito zanu nzodabwitsa kwambiri.
Mphamvu zanu nzazikulu,
kotero kuti adani anu amakuŵeramirani moopa.
4Anthu onse a pa dziko lapansi amakupembedzani,
amaimba nyimbo zotamanda Inu,
amaimba nyimbo zotamanda dzina lanu.”
5Bwerani mudzaone zimene Mulungu wachita,
ntchito zake nzodabwitsa pakati pa anthu.
6 Eks. 14.21; Yos. 3.14-17 Adasandutsa nyanja kuti ikhale nthaka youma.
Anthu adaoloka mtsinje uja poyenda pansi.
Nchifukwa chake timukondwerere Iye.
7Iye amalamula ndi mphamvu zake mpaka muyaya,
maso ake amalonda mitundu ina ya anthu.
Anthu oukira asadzikweze.
8Lemekezani Mulungu wathu,
inu mitundu ya anthunu,
mau omtamanda Iye amveke.
9Iye watchinjiriza moyo wathu,
sadalole kuti mapazi athu aterereke.
10Inu Mulungu, mwatiyesa,
mwatiyeretsa monga m'mene amayeretsera siliva.
11Inu mudatiloŵetsa mu ukonde wa adani,
mudatisenzetsa katundu wolemera pamsana pathu.
12Inu mudalola kuti adani atikwere pa mutu,
tidaloŵa m'moto ndiponso m'madzi,
komabe Inu mwatifikitsa ku malo opulumukirako.
13Ndidzabwera ku Nyumba yanu ndi nsembe zopsereza,
ndidzachitadi zimene ndidazilumbira kwa Inu,
14zimene ndidalankhula ndi pakamwa panga,
ndiponso zimene ndidalonjeza pamene ndinali pa mavuto.
15Ndidzapereka kwa Inu nsembe zopsereza
za nyama zonenepa,
utsi wa nsembe za nkhosa zamphongo udzafika kwa Inu.
Ndidzaperekanso ngati nsembe
ng'ombe zamphongo ndi mbuzi.
16Bwerani mudzamve,
inu nonse amene opembedza Mulungu,
ndidzakusimbireni zimene Iye wandichitira.
17Ndidafuula kwa Iye,
ndipo ndidamtamanda ndi pakamwa panga.
18Ndikadazindikira choipa chilichonse mumtima mwanga
ndi kuchibisa,
Ambuye sakadandimvera.
19Koma zoonadi, Mulungu wandimvera,
wasamala mau a pemphero langa.
20Mulungu atamandike
chifukwa sadakane pemphero langa,
sadachotse chikondi chake chosasinthika kwa Ine.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.