1 Eza. 4.24—5.1; 6.14 Mwezi wachisanu ndi chitatu, chaka chachiŵiri cha ufumu wa Dariusi, Chauta adapatsa mneneri Zekariya, mwana wa Berekiya, mdzukulu wa Ido, uthenga uwu wakuti,
2“Chauta adaŵakwiyira kwambiri makolo anu.
3Tsono uŵauze anthuŵa kuti zimene akunena Chauta Wamphamvuzonse ndi izi, akuti, Bwererani kwa Ine, ndipo Ine ndidzabwerera kwa inu.
4Musakhale ngati makolo anu, amene adamva mau a aneneri akale ofotokoza uthenga wanga wakuti, ‘Lekani makhalidwe anu oipa ndi ntchito zanu zoipa.’ Koma iwowo sadamve kapena kulabadako, akutero Chauta.
5Kodi makolo anuwo ali kuti tsopano? Nanga aneneri, kodi amakhalapo mpaka muyaya?
6Kodi mau anga ndi malamulo anga amene ndidauza atumiki anga aneneri, suja adamveka kwa makolo anu? Choncho iwo adalapa ndi kunena kuti, ‘Chauta Wamphamvuzonse watichitadi zomwe adaatsimikiza kuti adzatichita, potsata makhalidwe athu ndi ntchito zathu zoipa.’ ”
Aona akavalo m'masomphenya7Tsiku la 24 la mwezi wa khumi ndi umodzi, mwezi wa Sebati, chaka chachiŵiri cha ufumu wa Dariusi, Chauta adapatsa uthenga mneneri Zekariya, mwana wa Berekiya, mdzukulu wa Ido. Tsono Zekariya adati,
8Chiv. 6.4; Chiv. 6.2 “Usiku wathawu ndinaona zinthu m'masomphenya. Ndinaona munthu atakwera pa kavalo wofiira. Munthuyo anaima pa timitengo tazitsamba m'chigwa. Kumbuyo kwake kunalinso akavalo, ena ofiira, ena odera, ena oyera.
9Ndiye ine ndinamufunsa kuti, ‘Mbuye wanga, kodi nchiyaninso chikatere?’ Mngelo amene ankalankhula nane anayankha kuti, ‘Ndikufotokozera tanthauzo lake.’
10Tsono munthu amene anaima pa timitengo tazitsamba uja anayankha kuti, ‘Ameneŵa ndiwo amene Chauta waŵatuma kuti ayendere dziko lapansi.’
11Ndipo onsewo anauza mngelo wa Chauta amene anaima pakati pa timitengo tazitsamba uja, kuti, ‘Tayendera dziko lapansi, ndipo anthu onse ali pa mtendere, akupumula.’
12Tsono mngelo wa Chautayo anafunsa kuti, ‘Inu Chauta Wamphamvuzonse, kodi Yerusalemu ndi mizinda ya ku Yuda imene mudaikwiyira pa zaka makumi asanu ndi aŵiri, mudzakhalabe oiwumira mtima mpaka liti?’
13Chauta anamuyankha mau abwino ndi okondweretsa mngelo amene amalankhula naneyo.
14Pamenepo mngeloyo anandiwuza kuti, ‘Lengeza kuti, Chauta Wamphamvuzonse akuti, “Maganizo anga onse ndi mtima wanga wonse zili pa Yerusalemu ndi Ziyoni.
15Ndaŵakwiyira kwambiri anthu a mitundu ina amene ali pa mtendere. Pamene ndinkakwiyira anthu anga motsinira, mpamene anthu enawo ankakakatira kuzunza anthu anga.
16Nchifukwa chake ndabwerera ku Yerusalemu ndi mtima wachifundo. Nyumba yanga adzaimanganso kumeneko, ndipo adzatenga chingwe choyesera kuti amangenso mzinda wa Yerusalemu,” akutero Chauta Wamphamvuzonse.
17Ulengezenso kuti Chauta Wamphamvuzonse akuti, “M'mizinda yangayi mudzakhalanso chuma chambiri. Ndidzasangalatsanso Ziyoni, ndipo Yerusalemu ndidzamsandutsanso mzinda wanga wapamtima.” ’ ”
Za nyanga zinai18“Pambuyo pake m'masomphenyanso ndidaona nyanga zinai.
19Ndidafunsa mngelo amene ankalankhula nane tanthauzo lake la nyanga zimenezo. Iye adandiyankha kuti, ‘Zimenezi ndizo mphamvu zapansi pano zimene zidabalalitsa anthu a ku Yuda, a ku Israele ndi a ku Yerusalemu.’
20“Kenaka Chauta adandiwonetsa amisiri anai osula.
21Ine ndidafunsa kuti, ‘Kodi akudzachita chiyani?’ Iye adayankha kuti, ‘Mphamvu zijazi zidabalalitsa Yuda ndi Yerusalemu kotheratu, kotero kuti panalibe ndi mmodzi yemwe woŵeramutsa mutu. Koma amisiri osulaŵa, abwera kudzaopsa ndi kudzaononga mphamvu za mitundu ya anthu imene idaagonjetsa dziko la Yuda, ndi kumwaza anthu ake.’ ”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.